< Amosi 9 >

1 Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati: “Kantha mitu ya nsanamira kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke. Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse, onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe, palibe amene adzapulumuke.
Vidi Dominum stantem super altare. et dixit: Percute cardinem, et commoveantur superliminaria: avaritia enim in capite omnium, et novissimum eorum in gladio interficiam: non erit fuga eis. Et qui fugerit ex eis non salvabitur.
2 Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko. Ngakhale atakwera kumwamba Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko. (Sheol h7585)
Si descenderint usque ad infernum, inde manus mea educet eos: et si ascenderint usque in caelum, inde detraham eos. (Sheol h7585)
3 Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira. Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu, ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.
Et si absconditi fuerint in vertice Carmeli, inde scrutans auferam eos: et si celaverint se ab oculis meis in profundo maris, ibi mandabo serpenti, et mordebit eos.
4 Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo, ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko. Ndidzawayangʼanitsitsa kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.”
Et si abierint in captivitatem coram inimicis suis, ibi mandabo gladio, et occidet eos: et ponam oculos meos super eos in malum, et non in bonum.
5 Ambuye Yehova Wamphamvuzonse amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka, onse amene amakhala mʼmenemo amalira. Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo, kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.
Et Dominus Deus exercituum, qui tangit terram, et tabescet: et lugebunt omnes habitantes in ea: et ascendet sicut rivus omnis, et defluet sicut fluvius Aegypti.
6 Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba, ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi, Iye amene amayitana madzi a ku nyanja ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova.
Qui aedificat in caelo ascensionem suam, et fasciculum suum super terram fundavit: qui vocat aquas maris, et effundit eas super faciem terrae, Dominus nomen eius.
7 “Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli chimodzimodzi ndi Akusi?” Akutero Yehova. “Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto, Afilisti ku Kafitori ndi Aaramu ku Kiri?
Numquid non ut filii Aethiopum vos estis mihi, filii Israel, ait Dominus? numquid non Israel ascendere feci de Terra Aegypti: et Palaesthinos de Cappadocia, et Syros de Cyrene?
8 “Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wochimwawu. Ndidzawufafaniza pa dziko lapansi. Komabe sindidzawononga kotheratu nyumba ya Yakobo,” akutero Yehova.
Ecce oculi Domini Dei super regnum peccans, et conteram illud a facie terrae: verumtamen conterens non conteram domum Iacob, dicit Dominus.
9 “Pakuti ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amasefera ufa mʼsefa, koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.
Ecce enim mandabo ego, et concutiam in omnibus gentibus domum Israel, sicut concutitur triticum in cribro: et non cadet lapillus super terram.
10 Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga adzaphedwa ndi lupanga, onse amene amanena kuti, ‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’
In gladio morientur omnes peccatores populi mei: qui dicunt: Non appropinquabit, et non veniet super nos malum.
11 “Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzakonzanso malo amene anagumuka, ndi kuyimanganso monga inalili poyamba,
In die illa suscitabo tabernaculum David, quod cecidit: et reaedificabo aperturas murorum eius, et ea quae corruerant, instaurabo: et reaedificabo illud sicut in diebus antiquis.
12 kuti adzatengenso otsala a Edomu ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,” akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.
Ut possideant reliquias Idumaeae, et omnes nationes, eo quod invocatum sit nomen meum super eos: dicit Dominus faciens haec.
13 Yehova akunena kuti “Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu. Mapiri adzachucha vinyo watsopano ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
Ecce dies veniunt, dicit Dominus: et comprehendet arator messorem, et calcator uvae mittentem semen: et stillabunt montes dulcedinem, et omnes colli culti erunt.
14 Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli; mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo. Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake; adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
Et convertam captivitatem populi mei Israel: et aedificabunt civitates desertas, et inhabitabunt: et plantabunt vineas, et bibent vinum earum: et facient hortos, et comedent fructus eorum.
15 Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo, ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko limene Ine ndawapatsa,” akutero Yehova Mulungu wako.
Et plantabo eos super humum suam: et non evellam eos ultra de terra sua, quam dedi eis, dicit Dominus Deus tuus.

< Amosi 9 >