< Amosi 8 >
1 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa.
2 Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?” Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.
3 “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!”
4 Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu.
5 Mumanena kuti, “Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti kuti tigulitse zinthu? Ndipo tsiku la Sabata litha liti kuti tigulitse tirigu, kuti tichepetse miyeso, kukweza mitengo kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,
6 tigule osauka ndi ndalama zasiliva ndi osowa powapatsa nsapato, tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”
7 Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita.
8 “Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi, ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni? Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo; lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata ngati mtsinje wa ku Igupto.
9 “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzadetsa dzuwa masana ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo.
10 Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu ndi kumeta mipala mitu yanu. Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.
11 “Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse; osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi, koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
12 Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina. Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa, kufunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza.
13 “Tsiku limenelo “anamwali okongola ndi anyamata amphamvu adzakomoka ndi ludzu.
14 Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya, kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’ kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’ Iwowo adzagwa ndipo sadzadzukanso.”