< Amosi 6 >

1 Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya, inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka, kumene Aisraeli amafikako!
הוי השאננים בציון והבטחים בהר שמרון נקבי ראשית הגוים ובאו להם בית ישראל׃
2 Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane; mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja, ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti. Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa? Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu?
עברו כלנה וראו ולכו משם חמת רבה ורדו גת פלשתים הטובים מן הממלכות האלה אם רב גבולם מגבלכם׃
3 Inu simulabadirako kuti tsiku loyipa lidzafika, zochita zanu zimafulumizitsa ulamuliro wankhanza.
המנדים ליום רע ותגישון שבת חמס׃
4 Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu, mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu. Mumadya ana ankhosa onona ndi ana angʼombe onenepa.
השכבים על מטות שן וסרחים על ערשותם ואכלים כרים מצאן ועגלים מתוך מרבק׃
5 Mumayimba azeze anu ndi kumangopeka nyimbo pa zingʼwenyengʼwenye ngati Davide.
הפרטים על פי הנבל כדויד חשבו להם כלי שיר׃
6 Mumamwera vinyo mʼzipanda zodzaza ndipo mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa Yosefe.
השתים במזרקי יין וראשית שמנים ימשחו ולא נחלו על שבר יוסף׃
7 Nʼchifukwa chake inu mudzakhala mʼgulu la anthu oyamba kupita ku ukapolo; maphwando ndi zikondwerero zanu zidzatheratu.
לכן עתה יגלו בראש גלים וסר מרזח סרוחים׃
8 Ambuye Yehova walumbira mʼdzina lake. Yehova Mulungu Wamphamvuzonse walengeza kuti, “Ndimanyansidwa ndi kunyada kwa Yakobo, ndimadana ndi nyumba zake zaufumu; Ine ndidzawupereka mzindawu pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.”
נשבע אדני יהוה בנפשו נאם יהוה אלהי צבאות מתאב אנכי את גאון יעקב וארמנתיו שנאתי והסגרתי עיר ומלאה׃
9 Ngati anthu khumi otsala adzabisala mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa ndithu.
והיה אם יותרו עשרה אנשים בבית אחד ומתו׃
10 Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.”
ונשאו דודו ומסרפו להוציא עצמים מן הבית ואמר לאשר בירכתי הבית העוד עמך ואמר אפס ואמר הס כי לא להזכיר בשם יהוה׃
11 Pakuti Yehova walamula kuti nyumba zikuluzikulu Iye adzazigamulagamula, ndipo nyumba zazingʼono zidzasanduka maduka okhaokha.
כי הנה יהוה מצוה והכה הבית הגדול רסיסים והבית הקטן בקעים׃
12 Kodi akavalo amathamanga pa thanthwe? Kodi wina amatipula ndi ngʼombe mʼnyanja? Koma chiweruzo cholungama mwachisandutsa kukhala zinthu zakupha ndipo chipatso cha chilungamo mwachisandutsa kukhala chowawa.
הירצון בסלע סוסים אם יחרוש בבקרים כי הפכתם לראש משפט ופרי צדקה ללענה׃
13 Inu amene mukunyadira kuti munagonjetsa Lo Debara ndipo mukunena kuti, “Kodi sitinatenge Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
השמחים ללא דבר האמרים הלוא בחזקנו לקחנו לנו קרנים׃
14 Koma Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akulengeza kuti, “Inu nyumba ya Israeli, ndidzakudzutsirani mtundu wina wa anthu umene udzakuzunzani kuchokera ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha Araba.”
כי הנני מקים עליכם בית ישראל נאם יהוה אלהי הצבאות גוי ולחצו אתכם מלבוא חמת עד נחל הערבה׃

< Amosi 6 >