< Amosi 5 >
1 Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:
2 “Namwali Israeli wagwa, moti sadzadzukanso, wasiyidwa mʼdziko lake lomwe, popanda woti ndi kumudzutsa.”
3 Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”
4 Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi: “Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;
5 musafunefune Beteli, musapite ku Giligala, musapite ku Beeriseba. Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, ndipo Beteli adzawonongekeratu.”
6 Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo, mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto; motowo udzawononga, ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.
7 Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa ndi kunyoza chilungamo.
8 (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake.
9 Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),
10 inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu ndi kunyoza amene amanena zoona.
11 Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake.
12 Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.
13 Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu, popeza ndi nthawi yoyipa.
14 Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa, kuti mukhale ndi moyo. Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu, monga mmene mumanenera kuti ali nanu.
15 Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino; mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu. Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.
16 Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena: “Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula, ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse. Adzayitana alimi kuti adzalire, ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.
17 Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,” akutero Yehova.
18 Tsoka kwa inu amene mumalakalaka tsiku la Yehova! Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova? Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.
19 Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango amakumana ndi chimbalangondo, ngati pamene munthu walowa mʼnyumba, natsamira dzanja lake pa khoma ndipo njoka nʼkuluma.
20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala, mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?
21 “Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza; sindikondwera nayo misonkhano yanu.
22 Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya, Ine sindidzazilandira. Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano, Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.
23 Musandisokose nazo nyimbo zanu! Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.
24 Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi, chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!
25 “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?
26 Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene munadzipangira.
27 Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,” akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.