< Amosi 4 >
1 Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya, inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!”
2 Ambuye Yehova, mwa kuyera mtima kwake walumbira kuti, “Nthawi idzafika ndithu pamene adzakukokani ndi ngowe, womaliza wa inu adzakokedwa ndi mbedza.
3 Mudzatulukira mʼmingʼalu ya pa khoma aliyense payekhapayekha, ndipo mudzatayidwa ku Harimoni,” akutero Yehova.
4 “Bwerani ku Beteli mudzachimwe; ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa. Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse, bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse.
5 Wotchani buledi wokhala ndi yisiti ngati nsembe yachiyamiko ndi kumanyadira poyera za zopereka zanu zaufulu. Inu Aisraeli, zinyadireni nsembezo, pakuti izi ndi zimene mumakonda kuchita,” akutero Ambuye Yehova.
6 “Ndine amene ndinakusendetsani milomo mʼmizinda yanu yonse, ndipo munasowa chakudya mʼmizinda yanu. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
7 “Ndinenso amene ndinamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndinagwetsa mvula pa mzinda wina, koma pa mzinda wina ayi, mvula inkagwa pa munda wina; koma sinagwe pa munda wina ndipo mbewu zinawuma.
8 Anthu ankayenda mzinda ndi mzinda kufuna madzi, koma sanapeze madzi okwanira kumwa. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
9 “Nthawi zambiri ndinakantha mbewu zanu ndiponso minda ya mpesa, ndinayikantha ndi chinsikwi ndiponso ndi chiwawu. Dzombe linawononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
10 “Ine ndinabweretsa miliri pakati panu monga ndinachitira ku Igupto. Ndinapha anyamata anu ndi lupanga, ndinapereka akavalo anu kwa adani. Ndinakununkhitsani fungo la mitembo lochokera mʼmisasa yanu ya nkhondo. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
11 “Ndinawononga ena mwa inu monga ndinawonongera Sodomu ndi Gomora. Inu munali ngati chikuni choyaka chimene chafumulidwa pa moto. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
12 “Choncho izi ndi zimene ndidzakuchitire iwe Israeli, chifukwa ndidzakuchitira zimenezi, konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Israeli.”
13 Iye amene amawumba mapiri, amalenga mphepo, ndipo amawululira munthu za mʼmaganizo ake, Iye amene amasandutsa usana kuti ukhale mdima, ndipo amayenda pa zitunda za dziko lapansi, dzina lake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.