< Amosi 3 >
1 Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:
2 “Inu nokha ndi amene ndinakusankhani pakati pa mabanja onse a dziko lapansi; nʼchifukwa chake ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu onse.”
3 Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi asanapangane?
4 Kodi mkango umabangula mʼnkhalango usanagwire nyama? Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwake pamene sunagwire kanthu?
5 Kodi mbalame nʼkutera pa msampha pamene palibe nyambo yake? Kodi msampha umafwamphuka usanakole kanthu?
6 Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda, anthu sanjenjemera? Pamene tsoka lafika mu mzinda, kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?
7 Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu asanawulule zimene akufuna kuchita kwa atumiki ake, aneneri.
8 Mkango wabangula, ndani amene sachita mantha? Ambuye Yehova wayankhula, ndani amene sanganenere?
9 Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto: “Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya; onani chisokonezo pakati pake ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”
10 “Iwo sadziwa kuchita zolungama, ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.
11 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi: “Mdani adzalizungulira dzikoli; iye adzagwetsa malinga ako, ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”
12 Yehova akuti, “Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu, moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli amene amakhala mu Samariya pa msonga za mabedi awo, ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”
13 “Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
14 “Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake, ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli; nyanga za guwa zidzathyoka ndipo zidzagwa pansi.
15 Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha; nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,” akutero Yehova.