< Amosi 2 >
1 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Mowabu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu, mpaka kuwasandutsa phulusa,
2 Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti. Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa, mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga.
3 Ndidzawononga wolamulira wake ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,” akutero Yehova.
4 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo akana lamulo la Yehova ndipo sanasunge malangizo ake, popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza, milungu imene makolo awo ankayitsatira,
5 Ine ndidzatumiza moto pa Yuda, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”
6 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva, ndi osauka ndi nsapato.
7 Amapondereza anthu osauka ngati akuponda fumbi, ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa. Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo, ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.
8 Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe pa zovala zimene anatenga ngati chikole. Mʼnyumba ya mulungu wawo amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.
9 “Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo, ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu. Ndinawononga zipatso zawo ndiponso mizu yawo.
10 “Ine ndinakutulutsani ku Igupto, ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kudzakupatsani dziko la Aamori.
11 Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri, ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri. Kodi si choncho, inu Aisraeli?” akutero Yehova.
12 “Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja, ndipo munalamula aneneri kuti asanenere.
13 “Tsono Ine ndidzakupsinjani monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu.
14 Munthu waliwiro sadzatha kuthawa, munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga, wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15 Munthu wa uta sadzalimbika, msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka, ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16 Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri adzathawa ali maliseche pa tsikulo,” akutero Yehova.