< Machitidwe a Atumwi 8 >
1 Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano. Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya.
2 Anthu okonda Mulungu anayika maliro a Stefano ndipo anamulira kwambiri.
3 Koma Saulo anayamba kuwononga mpingo. Amapita nyumba ndi nyumba, ndipo amagwira amuna ndi amayi ndi kukawatsekera ku ndende.
4 Okhulupirira amene anabalalika amalalikira konse kumene amapita.
5 Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko.
6 Gulu la anthu litamva Filipo akulalikira komanso kuona zizindikiro zozizwitsa zimene ankazichita, onse anamvetsetsa zimene iye amanena.
7 Mizimu yoyipa inatuluka mwa anthu ambiri ikufuwula kwambiri ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo ndi olumala anachiritsidwa.
8 Kotero munali chimwemwe chachikulu mu mzindawo.
9 Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana,
10 ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.”
11 Anthu amamutsata chifukwa kwa nthawi yayitali amawadabwitsa ndi matsenga akewo.
12 Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi.
13 Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.
14 Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane.
15 Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera,
16 chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu.
17 Ndipo Petro ndi Yohane anasanjika manja awo pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.
18 Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati,
19 “Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera.”
20 Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama!
21 Ulibe gawo kapena mbali pa utumikiwu, chifukwa mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu.
22 Lapa zoyipa zakozi ndipo upemphere kwa Ambuye. Mwina adzakukhululukira maganizo a mu mtima mwako.
23 Pakuti ine ndikuona kuti ndiwe wowawidwa mtima ndiponso kapolo wa tchimo.”
24 Ndipo Simoni anayankha, “Mundipempherere kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.”
25 Atatha kuchitira umboni ndi kulalikira mawu a Ambuye, Petro ndi Yohane anabwerera ku Yerusalemu, atalalikira Uthenga Wabwino mʼmidzi yambiri ya Asamariya.
26 Mngelo wa Ambuye anati kwa Filipo, “Nyamuka pita chakummwera, ku msewu wa ku chipululu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu.”
27 Ndipo ananyamuka napita, ndipo akuyenda anakumana ndi munthu wa ku Etiopia wa udindo waukulu woyangʼanira chuma cha Kandake, mfumu yayikazi ya ku Etiopia. Munthu ameneyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu,
28 ndipo akubwerera kwawo atakwera pa galeta lake amawerenga buku la mneneri Yesaya.
29 Mzimu anamuwuza Filipo kuti, “Pita pa galeta ilo ndipo ukakhale pafupi nalo.”
30 Pamenepo Filipo anathamangira ku galeta ndipo anamva munthuyo akuwerenga buku la mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti, “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazi?”
31 Iye anayankha kuti, “Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Ndipo iye anayitana Filipo kuti abwere ndikukhala naye mʼgaleta.
32 Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa: “Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
33 Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?”
34 Ndunayo inamufunsa Filipo kuti, “Chonde, uzeni, kodi mneneri akuyankhula za ndani, za iye mwini kapena za munthu wina?”
35 Pamenepo Filipo anayambira pa malemba omwewo kumuwuza za Uthenga Wabwino wa Yesu.
36 Akuyenda mu msewu anafika pamalo pamene panali madzi ndipo ndunayo inati, “Taonani madzi awa. Kodi pali chondiletsa kuti ndibatizidwe?”
37 Filipo anati, “Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mukhoza kubatizidwa.” Ndunayo inayankha kuti, “Ine ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.”
38 Ndipo analamulira galeta kuti liyime. Onse awiriwo, Filipo ndi Ndunayo anatsika ndi kulowa mʼmadzi ndipo Filipo anamubatiza.
39 Pamene iwo anatuluka mʼmadzimo, Mzimu wa Ambuye anamukwatula Filipo, ndipo Ndunayo sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala.
40 Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Azoto ndipo anazungulira konse, kulalikira Uthenga Wabwino mʼmizinda yonse mpaka anakafika ku Kaisareya.