< Machitidwe a Atumwi 7 >
1 Kenaka mkulu wa ansembe anafunsa Stefano kuti, “Kodi zimene akukunenerazi ndi zoona?”
Alors le prince des prêtres lui demanda: Les choses sont-elles ainsi?
2 Stefano anayankha kuti, “Abale ndi makolo, tamverani! Mulungu waulemerero anaoneka kwa kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani.
Il répondit: Hommes, mes frères et mes pères, écoutez: Le Dieu de gloire apparut à notre père Abraham lorsqu’il était en Mésopotamie, avant qu’il demeurât à Charan,
3 Mulungu anati, ‘Tuluka mʼdziko lako, siya abale ako, ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.’
Et il lui dit: Sors de ton pays et de la parenté, et viens dans la terre que je te montrerai.
4 “Ndipo iye anatulukadi mʼdziko la Akaldeya ndi kukakhala ku Harani. Atamwalira abambo ake, Mulungu anamuchotsa kumeneko ndi kumubweretsa mʼdziko lino limene inu mukukhalamo tsopano.
Alors il sortit du pays des Chaldéens, et il demeura à Charan. Et de là, après que son père fut mort, Dieu le transporta dans cette terre que vous habitez aujourd’hui.
5 Mulungu sanamupatse cholowa kuno, ngakhale kadera kakangʼono kadziko. Koma Mulungu anamulonjeza kuti adzapereka dziko lino kwa iye ndi kwa zidzukulu zake, ngakhale kuti pa nthawi imeneyi analibe mwana.
Et il ne lui donna là ni héritage, ni même où poser le pied; mais il promit de la lui donner en sa possession et à sa postérité après lui, lorsqu’il n’avait point encore de fils.
6 Mulungu anayankhula motere kwa iye: ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo, ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.’
Toutefois Dieu lui dit que sa postérité habiterait en une terre étrangère, où elle serait réduite en servitude et maltraitée pendant quatre cents ans;
7 Mulungu anati, ‘Ine ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo, ndipo pambuyo pake akadzatuluka mʼdzikolo adzandipembedza Ine pamalo pano.’
Mais la nation qui l’aura tenue en servitude, c’est moi qui la jugerai, dit le Seigneur, et après cela, elle sortira et me servira en ce lieu-ci.
8 Kenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.
Il lui donna l’alliance de la circoncision; et ainsi il engendra Isaac, et le circoncit le huitième jour; et Isaac, Jacob; et Jacob, les douze patriarches.
9 “Makolo athu anachita nsanje ndi Yosefe ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Igupto. Koma Mulungu anali naye
Et les patriarches envieux vendirent Joseph pour l’Egypte; mais Dieu était avec lui;
10 ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.
Et il le délivra de toutes ses tribulations, et il lui donna grâce et sagesse devant Pharaon, roi d’Egypte, qui le préposa sur l’Egypte et sur toute sa maison.
11 “Kenaka munalowa njala mʼdziko la Kanaani, kotero kuti anthu anavutika kwambiri, ndipo makolo athu sanathe kupeza chakudya.
Or vint une famine dans toute l’Egypte et en Chanaan, et une grande tribulation, et nos pères ne trouvaient pas de nourriture.
12 Pamene Yakobo anamva kuti ku Igupto kunali tirigu, iye anatuma makolo athu ulendo woyamba.
Mais quand Jacob eut appris qu’il y avait du blé en Egypte, il y envoya nos pères une première fois,
13 Pa ulendo wawo wachiwiri, Yosefe anadziwulula kwa abale akewo ndipo Farao anadziwa za banja la Yosefe.
Et la seconde, Joseph fut reconnu de ses frères, et son origine fut découverte à Pharaon.
14 Izi zinachitika, Yosefe anayitanitsa abambo ake Yakobo ndi banja lonse, onse pamodzi analipo 75.
Or Joseph envoya quérir Jacob son père et toute sa parenté, au nombre de soixante-quinze personnes.
15 Motero Yakobo anapita ku Igupto, kumene iye ndiponso makolo athu anamwalira.
Jacob descendit donc en Egypte, et il y mourut, lui et nos pères.
16 Mitembo yawo anayinyamula ndi kupita nayo ku Sekemu kumene inayikidwa mʼmanda amene Abrahamu anagula kochokera kwa ana a Hamori ku Sekemuko.
Et ils furent transportés à Sichem, et déposés dans le sépulcre qu’Abraham avait acheté à prix d’argent des fils d’Hémor, fils de Sichem.
17 “Nthawi itayandikira yakuti Mulungu achite zimene analonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu unakula ndi kuchuluka kwambiri mu Igupto.
Mais comme approchait le temps de la promesse que Dieu avait jurée à Abraham, le peuple crût et se multiplia en Egypte,
18 Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto.
Jusqu’à ce qu’il s’éleva en Egypte un autre roi, qui ne connaissait point Joseph.
19 Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.
Celui-ci, circonvenant notre nation, affligea nos pères jusqu’à leur faire exposer leurs enfants pour en empêcher la propagation.
20 “Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola kwambiri. Iye analeredwa mʼnyumba ya abambo ake kwa miyezi itatu.
En ce même temps naquit Moïse qui fut agréable à Dieu, et nourri trois mois dans la maison de son père.
21 Atakamutaya, mwana wamkazi wa Farao anamutola nakamulera ngati mwana wake.
Exposé ensuite, la fille de Pharaon le prit et le nourrit comme son fils.
22 Mose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu mʼmawu ndi ntchito zake.
Et Moïse fut instruit dans toute la sagesse des Egyptiens, et il était puissant en paroles et en œuvres.
23 “Mose ali ndi zaka makumi anayi, anaganizira zokayendera abale ake Aisraeli.
Mais lorsque s’accomplissait sa quarantième année, il lui vint dans l’esprit de visiter ses frères, les enfants d’Israël.
24 Iye ataona mmodzi wa iwo akuzunzidwa ndi Mwigupto, anatchinjiriza Mwisraeliyo, namupha Mwiguptoyo.
Et ayant vu l’un d’eux injustement traité, il défendit et vengea celui qui souffrait l’injure, en frappant l’Egyptien.
25 Mose anaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu anamuyika kuti awapulumutse koma iwo sanazindikire.
Or il pensait que ses frères comprendraient que Dieu les sauverait par sa main; mais ils ne le comprirent pas.
26 Mmawa mwake Mose anaona Aisraeli awiri akukangana. Iye anayesa kuwayanjanitsa ponena kuti, ‘Amuna inu, ndinu abale; chifukwa chiyani mukufuna kupwetekana?’
Le jour suivant, il en vit qui se querellaient, et il tâchait de les remettre en paix, disant: Hommes, vous êtes frères; pourquoi vous nuisez-vous l’un à l’autre?
27 “Koma munthu amene amavutitsa mnzakeyo anakankha Mose ndipo anati, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza.
Mais celui qui faisait injure à l’autre le repoussa, disant: Qui t’a établi chef et juge sur nous?
28 Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja dzulo?’
Veux-tu me tuer, comme tu as tué hier l’Egyptien?
29 Mose atamva mawu awa anathawira ku Midiyani, kumene anakhala mlendo ndipo anabereka ana amuna awiri.
Moïse s’enfuit à cette parole, et il demeura comme étranger, dans la terre de Madian, où il engendra deux fils.
30 “Ndipo patapita zaka makumi anayi mngelo anaonekera kwa Mose mʼmalawi amoto pa chitsamba mʼchipululu pafupi ndi Phiri la Sinai.
Et quarante ans s’étant passés, un ange lui apparut au désert de la montagne de Sina, dans le feu d’un buisson enflammé,
31 Iye ataona zimenezi, anadabwa. Akupita kuti akaonetsetse pafupi, Mose anamva mawu a Ambuye:
Ce que Moïse apercevant, il admira la vision; et comme il s’approchait pour regarder, la voix du Seigneur se fit entendre à lui, disant:
32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.’ Mose ananjenjemera chifukwa cha mantha ndipo sanalimbe mtima kuyangʼananso.
Je suis le Dieu de vos pères, le Dieu d’Abraham, le Dieu d’Isaac et le Dieu de Jacob. Mais devenu tout tremblant, Moïse n’osait regarder.
33 “Ndipo Ambuye anati kwa Mose, ‘Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika.
Et le Seigneur lui dit: Ôte la chaussure de tes pieds, car le lieu où tu es est une terre sainte.
34 Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse. Tsopano tiye ndikutume ku Igupto.’
J’ai vu parfaitement l’affliction de mon peuple qui est en Egypte; j’ai entendu son gémissement, et je suis descendu pour le délivrer. Maintenant, viens, je t’enverrai en Egypte.
35 “Uyu ndi Mose yemwe uja amene Aisraeli anamukana ndi kunena kuti, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza?’ Iyeyo anatumidwa ndi Mulungu mwini kuti akakhale wowalamulira ndiponso mpulumutsi, mothandizidwa ndi mngelo amene anamuonekera pa chitsamba.
Ce Moïse qu’ils avaient renié, disant: Qui t’a établi chef et juge? fut celui-là même que Dieu envoya chef et libérateur par la main de l’ange qui lui apparut dans le buisson;
36 Iye anawatulutsa mu Igupto ndipo anachita zodabwitsa ndi zizindikiro zozizwitsa mu Igupto, pa Nyanja Yofiira, ndiponso mʼchipululu kwa zaka makumi anayi.
C’est lui qui les lira de la terre d’Egypte, y opérant des prodiges et des miracles, aussi bien que dans la mer Rouge, et pendant quarante ans dans le désert.
37 “Uyu ndi Mose uja amene anati kwa Aisraeli, ‘Mulungu adzawutsa pakati pa abale anu mneneri ngati ine.’
C’est ce Moïse qui dit aux enfants d’Israël: Dieu vous suscitera d’entre vos frères un prophète comme moi; vous l’écouterez.
38 Iyeyu anali mʼgulu la Aisraeli mʼchipululu pamodzi ndi mngelo amene anamuyankhula pa phiri la Sinai ndiponso makolo athu; ndipo Mose analandira mawu amoyo kuti atipatse ife.
C’est lui qui se trouva dans l’assemblée du peuple, au désert, avec l’ange qui lui parlait sur le mont Sina, et avec nos pères; lui qui reçut des paroles de vie pour nous les donner.
39 “Koma makolo athu anakana kumumvera iye. Iwo anamukana iye ndipo mʼmitima mwawo anatembenukira ku Igupto.
Et nos pères ne voulurent point lui obéir, mais ils le repoussèrent, retournant de cœur en Egypte,
40 Iwo anati kwa Aaroni, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitsogolera kutuluka mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.
Et disant à Aaron: Fais-nous des dieux qui aillent devant nous; car ce Moïse qui nous a tirés de la terre d’Egypte, nous ne savons ce qui lui est arrivé
41 Iyi ndi nthawi imene anapanga fano la mwana wangʼombe. Anapereka nsembe kwa fanoli nachita chikondwerero kulemekeza ntchito ya manja awo.
Et ils firent un veau en ces jours-là, et ils offrirent une hostie à l’idole, et ils se réjouissaient dans l’œuvre de leurs mains.
42 Koma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti, “‘Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?’
Et Dieu se détourna et les laissa servir la milice du ciel, comme il est écrit au livre des prophètes: Maison d’Israël, m’avez-vous offert des victimes et des hosties pendant quarante ans dans le désert?
43 Ayi, inu mwanyamula tenti ya Moloki ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene munapanga kuti muziwapembedza. Chifukwa chake, Ine ndidzakutumizani kutali, kupitirira dziko la Babuloni.
Au contraire, vous avez porté le tabernacle de Moloch et l’astre de votre dieu Remphan, figures que vous avez faites pour les adorer. Aussi je vous transporterai au-delà de Babylone.
44 “Makolo athu anali ndi tenti ya msonkhano pakati pawo mʼchipululu. Anayipanga monga momwe Mulungu anawuzira Mose, molingana ndi chithunzi chimene Mose anachiona.
Le tabernacle de témoignage a été avec nos pères dans le désert, comme Dieu leur ordonna, parlant à Moïse, afin qu’il le fît selon le modèle qu’il avait vu.
45 Makolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide,
Et l’ayant reçu, nos pères l’emportèrent sous Jésus, dans le pays des nations que Dieu chassa devant nos pères, jusqu’aux jours de David,
46 amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo.
Lequel trouva grâce devant Dieu et demanda de trouver une demeure pour le Dieu de Jacob.
47 Koma anali Solomoni amene anamanga nyumbayo.
Et ce fut Salomon qui lui bâtit un temple.
48 “Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti,
Mais le Très-Haut n’habite point dans les temples faits de la main des hommes, selon ce que dit le prophète:
49 “‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Akutero Ambuye. Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
Le ciel est mon trône, et la terre l’escabeau de mes pieds. Quelle maison me bâtirez-vous, dit le Seigneur, ou quel est le lieu de mon repos?
50 Kodi si dzanja langa linapanga zonsezi?’
N’est-ce pas ma main qui a fait toutes ces choses?
51 “Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera:
Durs de tête et incirconcis de cœur et d’oreilles, vous résistez toujours à l’Esprit-Saint; il en est de vous comme de vos pères.
52 Kodi analipo mneneri amene makolo anu sanamuzunze? Iwo anapha ngakhale amene ananeneratu za kubwera kwa Wolungamayo. Ndipo tsopano inu munamupereka ndi kumupha Iye.
Lequel des prophètes vos pères n’ont-ils point persécuté! Ils ont tué ceux qui prédisaient l’avènement du Juste que vous venez de trahir, et dont vous êtes les meurtriers, vous,
53 Inu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.”
Qui avez reçu la loi par le ministère des anges, et qui ne l’avez point gardée.
54 Atamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano.
Entendant cela, ils frémissaient de rage en leur cœur, et grinçaient des dents contre lui.
55 Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.
Mais comme il était rempli de l’Esprit-Saint, levant les yeux au ciel, il vit la gloire de Dieu, et Jésus qui se tenait à la droite de Dieu, et il dit: Voilà que je vois les cieux ouverts, et le Fils de l’homme qui est à la droite de Dieu.
56 Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”
Eux alors, criant d’une voix forte et se bouchant les oreilles, se précipitèrent tous ensemble sur lui,
57 Koma iwo anatseka mʼmakutu mwawo, ndipo anafuwula kolimba, onse anathamangira kwa iye,
Et l’entraînant hors de la ville, ils le lapidaient; et les témoins déposèrent leurs vêtements aux pieds d’un jeune homme nommé Saul.
58 anamukokera kunja kwa mzinda ndipo anayamba kumugenda miyala. Mboni zinasungitsa zovala zawo kwa mnyamata otchedwa Saulo.
Et ils lapidaient Etienne qui priait et disait: Seigneur Jésus, recevez mon esprit.
59 Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.”
Puis s’étant mis à genoux, il cria d’une voix forte: Seigneur, ne leur imputez point ce péché. Et lorsqu’il eut dit cela, il s’endormit dans le Seigneur. Or Saul était consentant de sa mort.
60 Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.