< Machitidwe a Atumwi 6 >

1 Mʼmasiku amenewo pamene chiwerengero cha ophunzira chinkachuluka, Ayuda a Chihelene pakati pawo anadandaula chifukwa cha Ayuda a Chihebri chifukwa amasiye awo samawagawira chakudya cha tsiku ndi tsiku.
A u ove dane, kad se umnožiše uèenici, podigoše Grci viku na Jevreje što se njihove udovice zaboravljahu kad se dijeljaše hrana svaki dan.
2 Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya.
Onda dvanaestorica dozvavši mnoštvo uèenika, rekoše: nije prilièno nama da ostavimo rijeè Božiju pa da služimo oko trpeza.
3 Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira.
Naðite dakle, braæo, meðu sobom sedam poštenijeh ljudi, punijeh Duha svetoga i premudrosti, koje æemo postaviti nad ovijem poslom.
4 Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.”
A mi æemo u molitvi i u službi rijeèi ostati.
5 Mawu amenewa anakondweretsa gulu lonse la anthu. Iwo anasankha, Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso Mzimu Woyera; anasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanora, Timo, Parmena ndi Nikolao amene anatembenuka mtima ndi kulowa Chiyuda kuchokera kwa Antiokeya.
I ova rijeè bi ugodna svemu narodu. I izbraše Stefana, èovjeka napunjena vjere i Duha svetoga, i Filipa, i Prohora, i Nikanora, i Timona, i Parmena, i Nikolu pokrštenjaka iz Antiohije.
6 Iwo anapereka anthuwa kwa atumwi amene anawapempherera ndi kuwasanjika manja.
Ove postaviše pred apostole, i oni pomolivši se Bogu metnuše ruke na njih.
7 Ndipo Mawu a Mulungu anapitirira kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira mu Yerusalemu chinakula mofulumira ndipo ansembe ochuluka anakhulupirira.
I rijeè Božija rastijaše, i množaše se vrlo broj uèenika u Jerusalimu. I sveštenici mnogi pokoravahu se vjeri.
8 Stefano, munthu wodzazidwa ndi chisomo cha Mulungu ndi mphamvu anachita zodabwitsa ndiponso zizindikiro zazikulu pakati pa anthu.
A Stefan pun vjere i sile èinjaše znake i èudesa velika meðu ljudima.
9 Panauka mtsutso kuchokera kwa anthu a ku Kurene ndi a ku Alekisandriya komanso a ku dera la Silisiya ndi Asiya, otchedwa a Sunagoge ya Mfulu. Anthu amenewa anayamba kutsutsana ndi Stefano.
Tada ustaše neki iz zbornice koja se zove Liveræanska i Kirinaèka i Aleksandrijnaèka i onijeh koji bijahu iz Kilikije i Azije, i prepirahu se sa Stefanom.
10 Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa.
I ne mogahu protivu stati premudrosti i Duhu kojijem govoraše.
11 Iwo ananyengerera anthu ena mwamseri kuti anene kuti, “Ife tinamva Stefano akuchitira chipongwe Mose ndiponso Mulungu.”
Tada podgovoriše ljude te kazaše: èusmo ga gdje huli na Mojsija i na Boga.
12 Motero anawutsa mitima ya anthu, akulu ndi aphunzitsi amalamulo. Anamugwira Stefano ndi kumubweretsa ku Bwalo Lalikulu.
I pobuniše narod i starješine i književnike, i napadoše i uhvatiše ga, i dovedoše ga na sabor.
13 Iwo anabweretsa mboni zonama zimene zinati, “Munthu uyu akupitirirabe kuyankhula mawu onyoza malo oyera ndi malamulo.
I izvedoše lažne svjedoke koji govorahu: ovaj èovjek ne prestaje huliti na ovo sveto mjesto i na zakon.
14 Pakuti tinamumva akunena kuti Yesu uja wa ku Nazareti adzawononga malo ano ndiponso kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”
Jer ga èusmo gdje govori: ovaj Isus Nazareæanin razvaliæe ovo mjesto, i izmijeniæe obièaje koje nam ostavi Mojsije.
15 Onse amene anakhala pansi Mʼbwalo Lalikulu anamuyangʼanitsitsa Stefano, ndipo anaona kuti nkhope yake ikuwala ngati ya mngelo.
I pogledavši na nj svi koji sjeðahu na saboru vidješe lice njegovo kao lice anðela.

< Machitidwe a Atumwi 6 >