< Machitidwe a Atumwi 3 >

1 Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana.
Now Peter and John were going up into the temple at the hour of prayer, [being] the ninth [hour].
2 Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo.
And a certain man that was lame from his mother’s womb was carried, whom they laid daily at the door of the temple which is called Beautiful, to ask alms of them that entered into the temple;
3 Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama.
who seeing Peter and John about to go into the temple, asked to receive an alms.
4 Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!”
And Peter, fastening his eyes upon him, with John, said, Look on us.
5 Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo.
And he gave heed unto them, expecting to receive something from them.
6 Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.”
But Peter said, Silver and gold have I none; but what I have, that give I thee. In the name of Jesus Christ of Nazareth, walk.
7 Ndipo anamugwira dzanja lamanja, namuthandiza kuti ayimirire ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi akakolo ake analimba.
And he took him by the right hand, and raised him up: and immediately his feet and his ankle-bones received strength.
8 Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu.
And leaping up, he stood, and began to walk; and he entered with them into the temple, walking, and leaping, and praising God.
9 Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu,
And all the people saw him walking and praising God:
10 anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira.
and they took knowledge of him, that it was he which sat for alms at the Beautiful Gate of the temple: and they were filled with wonder and amazement at that which had happened unto him.
11 Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni.
And as he held Peter and John, all the people ran together unto them in the porch that is called Solomon’s, greatly wondering.
12 Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu?
And when Peter saw it, he answered unto the people, Ye men of Israel, why marvel ye at this man? or why fasten ye your eyes on us, as though by our own power or godliness we had made him to walk?
13 Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule.
The God of Abraham, and of Isaac, and of Jacob, the God of our fathers, hath glorified his Servant Jesus; whom ye delivered up, and denied before the face of Pilate, when he had determined to release him.
14 Koma inu munamukana Woyera ndi Wolungamayo ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wakupha anthu.
But ye denied the Holy and Righteous One, and asked for a murderer to be granted unto you,
15 Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi.
and killed the Prince of life; whom God raised from the dead; whereof we are witnesses.
16 Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.
And by faith in his name hath his name made this man strong, whom ye behold and know: yea, the faith which is through him hath given him this perfect soundness in the presence of you all.
17 “Tsopano abale ine ndikudziwa kuti inu munachita zimenezi mosadziwa, monga momwenso anachitira atsogoleri anu.
And now, brethren, I wot that in ignorance ye did it, as did also your rulers.
18 Koma umu ndi mmene Mulungu anakwaniritsira zimene zinanenedwa kale ndi aneneri onse, kuti Khristu adzamva zowawa.
But the things which God foreshewed by the mouth of all the prophets, that his Christ should suffer, he thus fulfilled.
19 Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye,
Repent ye therefore, and turn again, that your sins may be blotted out, that so there may come seasons of refreshing from the presence of the Lord;
20 ndi kuti Iye atumize Yesu Khristu amene anasankhidwa chifukwa cha inu.
and that he may send the Christ who hath been appointed for you, [even] Jesus:
21 Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima. (aiōn g165)
whom the heaven must receive until the times of restoration of all things, whereof God spake by the mouth of his holy prophets which have been since the world began. (aiōn g165)
22 Pakuti Mose anati, ‘Ambuye Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri monga ine kuchokera pakati pa anthu anu; mumvere zonse zimene iye akuwuzeni.
Moses indeed said, A prophet shall the Lord God raise up unto you from among your brethren, like unto me; to him shall ye hearken in all things whatsoever he shall speak unto you.
23 Aliyense amene sadzamvera mawu a mneneriyo, adzayenera kuchotsedwa pakati pa abale ake.’
And it shall be, that every soul, which shall not hearken to that prophet, shall be utterly destroyed from among the people.
24 “Ndipo aneneri onse ambiri amene anayankhula kuyambira Samueli, ananeneratu za masiku ano.
Yea and all the prophets from Samuel and them that followed after, as many as have spoken, they also told of these days.
25 Inu ndinu ana a aneneri ndiponso ana apangano limene Mulungu anachita ndi makolo anu. Iye anati kwa Abrahamu, ‘Anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako.’
Ye are the sons of the prophets, and of the covenant which God made with your fathers, saying unto Abraham, And in thy seed shall all the families of the earth be blessed.
26 Pamene Mulungu anaukitsa mtumiki wake, anamutuma Iye poyamba kwa inu kuti akudalitseni pobweza aliyense wa inu ku zoyipa zake.”
Unto you first God, having raised up his Servant, sent him to bless you, in turning away every one of you from your iniquities.

< Machitidwe a Atumwi 3 >