< Machitidwe a Atumwi 28 >

1 Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita.
Et cum evasissemus, tunc cognovimus quia Melita insula vocabatur. Barbari vero praestabant non modicam humanitatem nobis.
2 Anthu a pa chilumbacho anatichitira zokoma zimene sizichitika kawirikawiri. Iwo anakoleza moto natilandira tonse chifukwa kumagwa mvula ndipo kumazizira.
Accensa enim pyra, reficiebant nos omnes propter imbrem, qui imminebat, et frigus.
3 Paulo anatola mtolo wankhuni, pamene amayika pa moto, munatulukamo njoka chifukwa cha kutentha, ndipo inamuluma pa dzanja.
Cum congregasset autem Paulus sarmentorum aliquantam multitudinem, et imposuisset super ignem, vipera a calore cum processisset, invasit manum eius.
4 Anthu a pa chilumbacho ataona njokayo ili lende pa dzanja lake, iwo anawuzana kuti, “Munthu uyu akuyenera kukhala munthu wopha anthu; pakuti ngakhale wapulumuka pa nyanja, chilungamo sichinamulore kuti akhale ndi moyo.”
Ut vero viderunt Barbari pendentem bestiam de manu eius, ad invicem dicebant: Utique homicida est homo hic, qui cum evaserit de mari, ultio non sinit eum vivere.
5 Koma Paulo anayikutumulira pa moto njokayo, ndipo sanamve kupweteka.
Et ille quidem excutiens bestiam in ignem, nihil mali passus est.
6 Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu.
At illi existimabant eum in tumorem convertendum, et subito casurum, et mori. Diu autem illis expectantibus, et videntibus nihil mali in eo fieri, convertentes se, dicebant eum esse Deum.
7 Pafupi ndi malowa panali munda wa Popliyo, mkulu wa boma la pa chilumbacho. Iye anatilandira natisamala bwino masiku atatu.
In locis autem illis erant praedia principis insulae, nomine Publii, qui nos suscipiens, triduo benigne se exhibuit.
8 Abambo ake anali gone, chifukwa amadwala malungo ndi kamwazi. Paulo analowa mʼchipinda chake kukawaona, ndipo atapemphera, anasanjika manja ake pa iwo nawachiritsa.
Contigit autem, patrem Publii febribus, et dysenteria vexatum iacere. Ad quem Paulus intravit: et cum orasset, et imposuisset ei manus, salvavit eum.
9 Zitachitika zimenezi, anthu onse odwala a pa chilumbacho anabwera ndipo anachiritsidwa.
Quo facto, omnes qui in insula habebant infirmitates, accedebant, et curabantur:
10 Anthuwo anatilemekeza ife mʼnjira zambiri ndipo pamene tinakonzeka kuti tiyambe ulendo, anatipatsa zonse zomwe tinazisowa.
qui etiam multis honoribus nos honoraverunt, et navigantibus imposuerunt quae necessaria erant.
11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pa sitima ina imene inakhala pa chilumbacho chifukwa cha kuzizira. Inali sitima ya ku Alekisandriya imene inali ndi chizindikiro cha milungu ya mapasa yotchedwa Kastro ndi Polikisi.
Post menses autem tres navigavimus in navi Alexandrina, quae in insula hiemaverat, cui erat insigne Castorum.
12 Tinakafika ku Surakusa ndipo kumeneko tinakhalako masiku atatu.
Et cum venissemus Syracusam, mansimus ibi triduo.
13 Kuchokera kumeneko tinayenda ndi kukafika ku Regio. Mmawa mwake mphepo yochokera kummwera inawomba, ndipo tsiku linalo tinakafika ku Potiyolo.
Inde circumlegentes devenimus Rhegium: et post unum diem flante Austro, secunda die venimus Puteolos;
14 Kumeneko tinapezako abale amene anatiyitana kuti tikhale nawo sabata limodzi. Ndipo kenaka tinapita ku Roma.
ubi inventis fratribus rogati sumus manere apud eos dies septem: et sic venimus Romam.
15 Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa.
Et inde cum audissent fratres, occurrerunt nobis usque ad Appii forum, ac tres Tabernas. Quos cum vidisset Paulus, gratias agens Deo, accepit fiduciam.
16 Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kukhala pa yekha ndi msilikali womulondera.
Cum autem venissemus Romam, permissum est Paulo manere sibimet cum custodiente se milite.
17 Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa pamodzi atsogoleri a Ayuda. Atasonkhana, Paulo anawawuza kuti, “Abale anga, ngakhale kuti ine sindinachite kanthu kalikonse kulakwira mtundu wathu kapena miyambo ya makolo athu, koma anandigwira mu Yerusalemu ndi kundipereka mʼmanja mwa Aroma.
Post tertium autem diem convocavit primos Iudaeorum. Cumque convenissent, dicebat eis: Ego, viri fratres, nihil adversus plebem faciens, aut morem paternum, vinctus ab Ierosolymis traditus sum in manus Romanorum,
18 Iwo anandifufuza ndipo anafuna kundimasula chifukwa sanandipeze wopalamula mlandu woyenera kuphedwa.
qui cum interrogationem de me habuissent, voluerunt me dimittere, eo quod nulla esset causa mortis in me.
19 Koma Ayuda atakana, ine ndinakakamizidwa kupempha kuti ndikaonekere pamaso pa Kaisara, sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga.
Contradicentibus autem Iudaeis, coactus sum appellare Caesarem, non quasi gentem meam habens aliquid accusare.
20 Pa chifukwa ichi ndapempha kuti ndionane nanu ndi kuyankhula nanu. Pakuti nʼchifukwa cha chiyembekezo cha Israeli ndamangidwa unyolo uwu.”
Propter hanc igitur causam rogavi vos videre, et alloqui. Propter spem enim Israel catena hac circumdatus sum.
21 Iwo anayankha kuti, “Ife sitinalandire kalata iliyonse yochokera ku Yudeya yonena za iwe, ndipo palibe mmodzi wa abale amene anachokera kumeneko anafotokoza kapena kunena kalikonse koyipa ka iwe.
At illi dixerunt ad eum: Nos neque litteras accepimus de te a Iudaea, neque adveniens aliquis fratrum nunciavit, aut locutus est quid de te malum.
22 Koma ife tikufuna kumva maganizo ako ndi otani, pakuti tikudziwa kuti ponseponse anthu akuyankhula zotsutsana ndi mpatuko umenewu.”
Rogamus autem a te audire quae sentis: nam de secta hac notum est nobis quia ubique ei contradicitur.
23 Iwo anakonza tsiku lina loti akumane ndi Paulo, ndipo anabwera anthu ambiri ku nyumba kumene amakhala. Kuyambira mmawa mpaka madzulo, Paulo anawafotokozera ndi kuwawuza za ufumu wa Mulungu ndipo anayesa kuwakopa kuti akhulupirire Yesu kuchokera mʼMalamulo a Mose ndiponso mʼmabuku a Aneneri.
Cum constituissent autem illi diem, venerunt ad eum in hospitium plurimi, quibus exponebat testificans regnum Dei, suadensque eis de Iesu ex Lege Moysi, et Prophetis a mane usque ad vesperam.
24 Ena anakopeka ndi zimene Paulo ananena, koma enanso sanakhulupirire.
Et quidam credebant his, quae dicebantur: quidam vero non credebant.
25 Ndipo anayamba kuchoka popeza sanagwirizane pakati pawo Paulo atanena mawu awa omaliza akuti, “Mzimu Woyera anayankhula zoona za makolo anu pamene Iye ananena kudzera mwa Mneneri Yesaya kuti,
Cumque invicem non essent consentientes, discedebant dicente Paulo unum verbum: Quia bene Spiritus sanctus locutus est per Isaiam prophetam ad Patres nostros,
26 “Pita kwa anthu awa ndi kuwawuza kuti, ‘Kumva mudzamva, koma osamvetsetsa; kupenya mudzapenya, koma osaona kanthu.’
dicens: Vade ad populum istum, et dic ad eos: Aure audietis, et non intelligetis: et videntes videbitis, et non perspicietis.
27 Pakuti mtima wa anthu ndi wokanika; mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.
Incrassatum est enim cor populi huius, et auribus graviter audierunt, et oculos suos compresserunt: ne forte videant oculis, et auribus audiant, et corde intelligant, et convertantur, et sanem eos.
28 “Chifukwa chake ine ndikufuna mudziwe kuti chipulumutso cha Mulungu chatumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzamvera.”
Notum ergo sit vobis, quoniam Gentibus missum est hoc salutare Dei, et ipsi audient.
29 Paulo atanena mawu amenewa, Ayuda aja anachoka akutsutsana kwambiri.
Et cum haec dixisset, exierunt ab eo Iudaei, multam habentes inter se quaestionem.
30 Paulo anakhala kumeneko zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yobwereka yomwe amalipira ndipo ankalandira aliyense amene amabwera kudzamuona.
Mansit autem biennio toto in suo conducto: et suscipiebat omnes, qui ingrediebantur ad eum,
31 Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.
praedicans regnum Dei, et docens quae sunt de Domino Iesu Christo cum omni fiducia, sine prohibitione.

< Machitidwe a Atumwi 28 >