< Machitidwe a Atumwi 27 >
1 Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa sitima ya pa madzi, anamupereka Paulo pamodzi ndi a mʼndende ena kwa msilikali wolamulira asilikali 100, dzina lake Yuliyo, amene anali wa gulu la asilikali lotchedwa, Gulu la Mfumu.
Ut autem judicatum est navigare eum in Italiam, et tradi Paulum cum reliquis custodiis centurioni nomine Julio cohortis Augustæ,
2 Tinakwera sitima ya pamadzi yochokera ku Adramutiyo imene inali yokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tinanyamuka. Aristariko, wa ku Makedoniya wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe.
ascendentes navem Adrumetinam, incipientes navigare circa Asiæ loca, sustulimus, perseverante nobiscum Aristarcho Macedone Thessalonicensi.
3 Mmawa mwake tinafika ku Sidoni; ndipo Yuliyo, mokomera mtima Paulo, anamulola kupita kwa abwenzi ake kuti akamupatse zosowa zake.
Sequenti autem die devenimus Sidonem. Humane autem tractans Julius Paulum, permisit ad amicos ire, et curam sui agere.
4 Kuchokera kumeneko tinayambanso ulendo pa nyanja ndipo tinadutsa kumpoto kwa chilumba cha Kupro chifukwa mphepo imawomba kuchokera kumene ife timapita.
Et inde cum sustulissemus, subnavigavimus Cyprum, propterea quod essent venti contrarii.
5 Titawoloka nyanja mbali ya gombe la Kilikiya ndi Pamfiliya, tinakafika ku Mura, mzinda wa ku Lukia.
Et pelagus Ciliciæ et Pamphyliæ navigantes, venimus Lystram, quæ est Lyciæ:
6 Kumeneko wolamulira asilikali 100 uja anapeza sitima ya pamadzi ya ku Alekisandriya imene imapita ku Italiya, ndipo anatikweza mʼmenemo.
et ibi inveniens centurio navem Alexandrinam navigantem in Italiam, transposuit nos in eam.
7 Tinayenda pangʼonopangʼono kwa masiku ambiri ndipo tinakafika kufupi ndi Knido movutikira. Pamene mphepo sinatilole kupitirira ulendo wathu molunjika, tinadzera kummwera kwa chilumba cha Krete, moyangʼanana ndi Salimoni.
Et cum multis diebus tarde navigaremus, et vix devenissemus contra Gnidum, prohibente nos vento, adnavigavimus Cretæ juxta Salmonem:
8 Timayenda movutikira mʼmbali mwa chilumbacho ndipo tinafika pa malo wotchedwa Madooko Okoma, pafupi ndi mzinda wa Laseya.
et vix juxta navigantes, venimus in locum quemdam qui vocatur Boniportus, cui juxta erat civitas Thalassa.
9 Tinataya nthawi yayitali, ndipo kuyenda pa nyanja kunali koopsa chifukwa nʼkuti tsopano nthawi yosala kudya itapita kale. Choncho Paulo anawachenjeza kuti,
Multo autem tempore peracto, et cum jam non esset tuta navigatio eo quod et jejunium jam præteriisset, consolabatur eos Paulus,
10 “Anthu inu, ine ndikuona kuti ulendo wathuwu ukhala woopsa ndipo katundu ndi sitima ziwonongeka, ngakhalenso miyoyo yathu.”
dicens eis: Viri, video quoniam cum injuria et multo damno non solum oneris, et navis, sed etiam animarum nostrarum incipit esse navigatio.
11 Koma wolamulira asilikali 100 uja, mʼmalo momvera zimene Paulo amanena, anatsatira malangizo a woyendetsa sitimayo ndiponso mwini wa sitimayo.
Centurio autem gubernatori et nauclero magis credebat, quam his quæ a Paulo dicebantur.
12 Popeza kuti dookolo silinali labwino kukhalako nthawi yozizira anthu ambiri anaganiza kuti tichoke. Ife tinkayembekeza kukafika ku Foinikisi ndi kukhala kumeneko nthawi yachisanu. Ili linali dooko la ku Krete, limene limaloza kummwera cha kumadzulo ndiponso kumpoto cha kumadzulo.
Et cum aptus portus non esset ad hiemandum, plurimi statuerunt consilium navigare inde, si quomodo possent, devenientes Phœnicen hiemare, portum Cretæ respicientem ad Africum et ad Corum.
13 Mphepo yochokera kummwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anthuwo anaganiza kuti apeza chimene amafuna; kotero analowetsa nangula ndipo anayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Krete.
Aspirante autem austro, æstimantes propositum se tenere, cum sustulissent de Asson, legebant Cretam.
14 Pasanathe nthawi yayitali, mphepo yamkuntho yotchedwa Eurokulo, inayamba kuwomba kuchokera ku chilumbacho.
Non post multum autem misit se contra ipsam ventus typhonicus, qui vocatur Euroaquilo.
15 Mphepo yamkunthoyo inawomba sitima ija ndipo sinathe kulimbana nayo, kotero ife tinayigonjera ndi kuyamba kutengedwa nayo.
Cumque arrepta esset navis, et non posset conari in ventum, data nave flatibus, ferebamur.
16 Tikudutsa mʼmbali mwa kachilumba kakangʼono kotchedwa Kawuda, tinavutika kuti tisunge bwato lopulumukiramo.
In insulam autem quamdam decurrentes, quæ vocatur Cauda, potuimus vix obtinere scapham.
17 Anthuwo atakweza bwatolo mʼsitima, anakulunga zingwe sitimayo kuti ayilimbitse. Poopa kuti angakagunde mchenga wa ku Surti, iwo anatsitsa nangula ndi kuyilola sitima kuti idzingoyenda ndi mphepo.
Qua sublata, adjutoriis utebantur, accingentes navem, timentes ne in Syrtim inciderent, summisso vase sic ferebantur.
18 Ife tinavutika kwambiri ndi namondwe kotero kuti mmawa mwake tinayamba kuponya katundu mʼmadzi.
Valida autem nobis tempestate jactatis, sequenti die jactum fecerunt:
19 Pa tsiku lachitatu anaponya mʼnyanja zipangizo za mʼsitima ndi manja awo.
et tertia die suis manibus armamenta navis projecerunt.
20 Sitinaone dzuwa kapena nyenyezi kwa masiku ambiri ndipo namondwe anapitirira kuwomba kwambiri, pomaliza ife tonse tinalibenso chiyembekezo choti nʼkupulumuka.
Neque autem sole, neque sideribus apparentibus per plures dies, et tempestate non exigua imminente, jam ablata erat spes omnis salutis nostræ.
21 Anthu aja atakhala nthawi yayitali osadya, Paulo anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga oti tisachoke ku Krete: zonsezi sizikanawonongeka ndi kutayika.
Et cum multa jejunatio fuisset, tunc stans Paulus in medio eorum, dixit: Oportebat quidem, o viri, audito me, non tollere a Creta, lucrique facere injuriam hanc et jacturam.
22 Koma tsopano ndikuti limbani mtima, chifukwa palibe aliyense wa inu amene adzataya moyo wake; koma sitima yokhayi idzawonongeka.
Et nunc suadeo vobis bono animo esse: amissio enim nullius animæ erit ex vobis, præterquam navis.
23 Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine,
Astitit enim mihi hac nocte angelus Dei, cujus sum ego, et cui deservio,
24 ndipo iyeyu anati, ‘Usachite mantha, Paulo. Ukuyenera kukayima pamaso pa Kaisara; ndipo Mulungu mwa kukoma mtima kwake wakupatsa miyoyo ya anthu onse amene ukuyenda nawo.’
dicens: Ne timeas, Paule: Cæsari te oportet assistere: et ecce donavit tibi Deus omnes qui navigant tecum.
25 Tsono limbani mtima, anthu inu, pakuti ine ndili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu kuti zichitika monga momwe wandiwuzira.
Propter quod bono animo estote, viri: credo enim Deo quia sic erit, quemadmodum dictum est mihi.
26 Komabe tiyenera kukatsakamira pa chilumba china chake.”
In insulam autem quamdam oportet nos devenire.
27 Pakati pa usiku wa tsiku la khumi ndi chinayi tikukankhidwabe ndi mphepo mʼnyanja ya Adriya, oyendetsa sitimayo anazindikira kuti timayandikira ku mtunda.
Sed posteaquam quartadecima nox supervenit, navigantibus nobis in Adria circa mediam noctem, suspicabantur nautæ apparere sibi aliquam regionem.
28 Iwo anatenga choyezera kuzama kwa nyanja ndi kupeza kuti kuzama kwake kunali mamita 36. Atayendanso pangʼono anatenganso choyezera chija napeza kuti kuzama kwake kunali 27.
Qui et summittentes bolidem, invenerunt passus viginti: et pusillum inde separati, invenerunt passus quindecim.
29 Poopa kuti tingagunde miyala, iwo anatsitsira anangula anayi mʼmadzi kumbuyo kwa sitimayo ndipo tinapemphera kuti kuche.
Timentes autem ne in aspera loca incideremus, de puppi mittentes anchoras quatuor, optabant diem fieri.
30 Pofuna kuthawa mʼsitimayo, oyendetsa aja anatsitsira mʼnyanja bwato lopulumukiramo nʼkumachita ngati akufuna kutsitsira anangula mʼnyanjamo kutsogolo kwa sitimayo.
Nautis vero quærentibus fugere de navi, cum misissent scapham in mare, sub obtentu quasi inciperent a prora anchoras extendere,
31 Pamenepo Paulo anawuza wolamulira asilikali uja ndi asilikaliwo kuti, “Ngati anthu awa sakhala mʼsitima muno, inu simungapulumuke.”
dixit Paulus centurioni et militibus: Nisi hi in navi manserint, vos salvi fieri non potestis.
32 Pamenepo asilikaliwo anadula zingwe za bwatolo ndipo linagwera mʼmadzi.
Tunc absciderunt milites funes scaphæ, et passi sunt eam excidere.
33 Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anawawumiriza anthu onse kuti adye. Iye anati, “Kwa masiku khumi ndi anayi mwakhala mukuda nkhawa ndipo simumadya kanthu kalikonse.
Et cum lux inciperet fieri, rogabat Paulus omnes sumere cibum, dicens: Quartadecima die hodie exspectantes jejuni permanetis, nihil accipientes.
34 Tsopano ine ndikukupemphani kuti mudye. Muyenera kudya kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe wa inu adzataye ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pake.”
Propter quod rogo vos accipere cibum pro salute vestra: quia nullius vestrum capillus de capite peribit.
35 Paulo atanena zimenezi, anatenga buledi nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo ananyema bulediyo nayamba kudya.
Et cum hæc dixisset, sumens panem, gratias egit Deo in conspectu omnium: et cum fregisset, cœpit manducare.
36 Onse analimba mtima nayamba kudyanso.
Animæquiores autem facti omnes, et ipsi sumpserunt cibum.
37 Tonse pamodzi mʼsitimamo tinalipo anthu 276.
Eramus vero universæ animæ in navi ducentæ septuaginta sex.
38 Onse atadya, nakhuta anapeputsa sitimayo potaya tirigu mʼnyanja.
Et satiati cibo alleviabant navem, jactantes triticum in mare.
39 Kutacha, anthu sanazindikire dzikolo, koma anaona pomwe sitima zimayimapo pamodzi ndi mchenga wa pa gombe. Iwo anaganiza zokocheza sitimayo kumeneko ngati zikanatheka kutero.
Cum autem dies factus esset, terram non agnoscebant: sinum vero quemdam considerabant habentem littus, in quem cogitabant si possent ejicere navem.
40 Atadula anangula aja, nawasiya mʼnyanja, pa nthawi yomweyo anamasula zingwe zimene anamangira zowongolera sitimayo. Kenaka anayimika chinsalu chimene mphepo imakankha kuti sitima iyende, ndipo anayamba kupita ku gombe.
Et cum anchoras sustulissent, committebant se mari, simul laxantes juncturas gubernaculorum: et levato artemone secundum auræ flatum, tendebant ad littus.
41 Koma sitimayo inagunda mchenga wobisika ndipo inayima. Mbali ya kutsogolo ya sitimayo inakanirira ndipo sinathe kuyendanso, ndipo mbali yakumbuyo inasweka ndi kuwomba kwa mafunde.
Et cum incidissemus in locum dithalassum, impegerunt navem: et prora quidem fixa manebat immobilis, puppis vero solvebatur a vi maris.
42 Asilikali anaganiza za kupha amʼndende onse, kuti angasambire kupita pa mtunda ndi kuthawa.
Militum autem consilium fuit ut custodias occiderent, ne quis cum enatasset, effugeret.
43 Koma wolamulira asilikali uja anafuna kupulumutsa Paulo ndipo anawaletsa kuchita zimene anakonza. Iye analamulira asilikali kuti amene amatha kusambira kuti adziponye mʼmadzi ndi kuyamba kukafika pa mtunda.
Centurio autem volens servare Paulum, prohibuit fieri: jussitque eos qui possent natare, emittere se primos, et evadere, et ad terram exire:
44 Otsalawo anayenera kugwira matabwa kapena tizidutswa ta sitimayo. Motero onse anapulumuka nakafika pa mtunda.
et ceteros, alios in tabulis ferebant, quosdam super ea quæ de navi erant. Et sic factum est, ut omnes animæ evaderent ad terram.