< Machitidwe a Atumwi 25 >
1 Patapita masiku atatu Festo atafika mʼdera lake, anachoka ku Kaisareya ndi kupita ku Yerusalemu.
Festus donc, étant arrivé dans la province, monta, trois jours après, de Césarée à Jérusalem.
2 Kumeneko akulu a ansembe ndi atsogoleri a Chiyuda anabwera kwa iye ndi kumufotokozera mlandu wa Paulo.
Et les princes des prêtres et les premiers d’entre les Juifs vinrent vers lui pour accuser Paul, et ils le priaient,
3 Iwo anamupempha Festo kuti awakomere mtima potumiza Paulo ku Yerusalemu, pakuti anali atakonzekera chiwembu kuti amuphe Pauloyo pa njira.
Demandant en grâce, qu’il le fit amener à Jérusalem, ayant préparé des embûches pour le tuer en chemin.
4 Festo anayankha kuti, “Paulo akusungidwa ku Kaisareya, ndipo ndipita kumeneko posachedwa.
Mais Festus répondit que Paul était gardé à Césarée, et que lui-même partirait bientôt.
5 Ena mwa atsogoleri anu apite nane kumeneko, kuti akafotokoze mlandu wa munthuyu, ngati anachita kanthu kalikonse kolakwika.”
Que les principaux donc d’entre vous (dit-il) descendent ensemble, et, s’il y a quelque crime en cet homme, qu’ils l’accusent.
6 Festo atakhala nawo masiku asanu ndi atatu kapena khumi iye anapita ku Kaisareya, ndipo mmawa mwake anayitanitsa bwalo nalamula kuti abweretse Paulo pamaso pake.
Or, après avoir passé huit ou dix jours parmi eux, il descendit à Césarée; et le jour suivant, il s’assit sur son tribunal, et ordonna d’amener Paul.
7 Paulo atafika, Ayuda amene anafika kuchokera ku Yerusalemu anayima momuzungulira. Iwo anamunenera zinthu zoopsa zambiri zimene sakanatha kubweretsa umboni wake.
Lorsqu’on l’eut amené, les Juifs qui étaient descendus de Jérusalem l’entourèrent, l’accusant de beaucoup de crimes graves, qu’ils ne pouvaient prouver,
8 Kenaka Paulo ananena mawu ake odziteteza kuti, “Ine sindinalakwirepo lamulo la Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu kapenanso Kaisara.”
Paul se défendant ainsi: Je n’ai rien fait, ni contre la loi des Juifs, ni contre le temple, ni contre César.
9 Festo, pofuna kuti Ayuda amukonde anafunsa Paulo kuti, “Kodi iwe ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti kumeneko ukafotokoze mlandu wako pamaso panga?”
Mais Festus, qui voulait faire plaisir aux Juifs, répondant à Paul, dit: Veux-tu monter à Jérusalem, et y être jugé sur ces choses devant moi?
10 Paulo anayankha kuti, “Ine tsopano ndayima pamaso pa bwalo la milandu la Kaisara, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ine sindinalakwire Ayuda, monga inu mukudziwa bwino.
Mais Paul répondit: C’est devant le tribunal de César que je suis: c’est là qu’il faut que je sois jugé. Je n’ai nui en rien aux Juifs, comme vous-même le savez fort bien.
11 Koma ngati ndili wolakwa, ngati ndachita kanthu koyenera kuphedwa, ine sindikukana kufa. Koma ngati mlandu umene abweretsa Ayudawa siwoona, palibe munthu angathe kundipereka mʼmanja mwawo. Ndikupempha kuti ndikaweruzidwe ndi Kaisara!”
Car si j’ai nui à quelqu’un ou si j’ai fait quelque chose qui mérite la mort, je ne refuse point de mourir; mais s’il n’en est rien des choses dont ils m’accusent, personne ne peut me livrer à eux. J’en appelle à César.
12 Festo atakambirana ndi akuluakulu abwalo lake, anati, “Popeza wapempha kupita kwa Kaisara, kwa Kaisara udzapitadi!”
Alors Festus, ayant conféré avec le conseil, répondit: C’est à César que tu en as appelé, c’est devant César que tu iras.
13 Patapita masiku ochepa mfumu Agripa pamodzi ndi Bernisi anabwera ku Kaisareya kudzalonjera Festo.
Quelques jours après, le roi Agrippa et Bérénice descendirent à Césarée pour saluer Festus,
14 Atakhala kumeneko masiku angapo, Festo anafotokozera mfumuyo za mlandu wa Paulo. Iye anati, “Kuli munthu wina kuno amene Felike anamusiya mʼndende.
Et comme ils demeurèrent plusieurs jours, Festus parla de Paul au roi, disant: Un certain homme a été laissé ici par Félix comme prisonnier;
15 Nditapita ku Yerusalemu akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda anandifotokozera mlandu wake ndipo anandipempha kuti ndigamule kuti ndi wolakwa.
À son sujet, lorsque j’étais à Jérusalem, les princes des prêtres et les anciens des Juifs sont venus vers moi, demandant une condamnation contre lui.
16 “Ine ndinawayankha kuti si mwambo wa Aroma kungomupereka munthu ayi. Munthu woyimbidwa mlanduyo amayenera kukumana nawo omunenezawo, kuti iye akhale ndi mwayi woyankhapo pa zimene akumuyimba mlanduzo.
Je leur ai répondu: Ce n’est pas la coutume des Romains de condamner un homme avant que l’accusé ait ses accusateurs présents, et qu’on lui ait donné lieu de se défendre, pour se laver de l’accusation.
17 Atabwera kuno pamodzi ndi ine, sindinachedwetse mlanduwo, koma ndinayitanitsa bwalo mmawa mwake ndi kulamula kuti amubweretse munthuyo.
Après donc qu’ils furent venus ici sans aucun délai, le jour suivant, siégeant sur mon tribunal, j’ordonnai d’y amener cet homme.
18 Omuyimba mlandu aja atayimirira kuti ayankhule, iwo sananene cholakwa chilichonse chimene ndimayembekezera.
Ses accusateurs s’étant présentés, ne lui reprochaient aucun des crimes dont je le soupçonnais coupable;
19 Mʼmalo mwake, anatsutsana naye pa fundo zina za chipembedzo chawo ndi za munthu wakufa, dzina lake Yesu, amene Paulo akuti ali moyo.
Mais ils agitaient contre lui quelques questions touchant leur superstition, et un certain Jésus, mort, que Paul affirmait être vivant.
20 Ine ndinathedwa nzeru wosadziwa momwe ndikanafufuzira nkhaniyi; kotero ndinafunsa ngati akanafuna kupita ku Yerusalemu kuti akaweruzidwe kumeneko.
Pour moi, hésitant à l’égard d’une question de cette sorte, je lui demandais s’il voulait aller à Jérusalem pour être jugé sur ces choses.
21 Koma Paulo anapempha kuti akaonekere pamaso pa mfumu ya Chiroma, ndipo ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”
Mais Paul en ayant appelé, pour que sa cause fût réservée à la connaissance d’Auguste, j’ai ordonné qu’on le gardât jusqu’à ce que je l’envoie à César.
22 Ndipo Agripa anati kwa Festo, “Ine ndikufuna ndimumve ndekha munthu ameneyu.” Iye anayankha kuti, “Mudzamumva mawa.”
Agrippa dit alors à Festus: Je voulais, moi aussi, entendre cet homme. Demain, répondit Festus, vous l’entendrez.
23 Mmawa mwake Agripa ndi Bernisi anabwera mwaulemu waukulu waufumu nalowa mʼbwalo la milandu pamodzi ndi akulu a asilikali ndiponso akuluakulu a mu mzindawo. Atalamula Festo kuti Paulo abwere, anabweradi.
Le lendemain donc, Agrippa et Bérénice étant venus en grande pompe, et étant entrés dans la salle des audiences avec les tribuns et les principaux de la ville, Paul fut amené par ordre de Festus.
24 Festo anati, “Mfumu Agripa, ndi onse amene muli nafe pano, mukumuona munthu uyu! Ayuda onse anandipempha ine za uyu ku Yerusalemu ndiponso kuno ku Kaisareya, mofuwula kuti, ameneyu sayenera kukhala ndi moyo.
Et Festus dit: Roi Agrippa, et vous tous qui êtes ici réunis avec nous, vous voyez cet homme, au sujet de qui toute la multitude des Juifs m’a interpellé à Jérusalem, représentant et criant qu’il ne devait pas vivre plus longtemps
25 Ine ndinapeza kuti iyeyu sanachite kanthu koyenera kufa, koma popeza anapempha kuti apite kwa mfumu ya Chiroma, ine ndinatsimikiza zomutumiza ku Roma.
Pour moi, j’ai reconnu qu’il n’avait rien fait qui méritât la mort; cependant lui-même en ayant appelé à Auguste, j’ai décidé de l’y envoyer.
26 Koma ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere Wolemekezekayo za iyeyu. Nʼchifukwa chake ndabwera naye pamaso pa nonsenu, makamaka kwa inuyo mfumu Agripa, kuti mwina mukamufunsitsa ndikhale ndi choti ndilembe.
Et n’ayant rien de certain à écrire de lui à l’Empereur, je l’ai fait venir devant vous tous, mais principalement devant vous, roi Agrippa, afin que, l’interrogation faite, j’aie quelque chose à écrire.
27 Pakuti ine ndikuganiza kuti ndi chinthu chopanda nzeru kutumiza wamʼndende popanda kutchula zifukwa zenizeni za mlandu wake.”
Car il me semble hors de raison d’envoyer un homme chargé de liens, et de ne pas en faire connaître la cause.