< Machitidwe a Atumwi 22 >
1 Iye anati, “Inu abale anga ndi makolo anga, tamvani mawu akudziteteza kwanga.”
2 Atamva iye akuyankhula Chihebri, anakhala chete. Kenaka Paulo anati,
3 “Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero.
4 Ine ndinkazunza anthu otsatira Njirayi mpaka kuwapha. Ndinkagwira amuna ndi amayi ndi kuwayika mʼndende.
5 Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe.
6 “Nthawi ya masana, nditayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunandizungulira.
7 Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti, ‘Saulo! Saulo! Ukundizunziranji?’”
8 Ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?” Iye anayankha kuti, “Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.”
9 Anzanga a paulendo anaona kuwalako, koma sanamve mawuwo, a Iye amene amayankhula nane.
10 Ine ndinafunsa kuti, “Kodi ndichite chiyani Ambuye?” Ambuye anati, “Imirira ndipo pita ku Damasiko. Kumeneko adzakuwuza zonse zimene ukuyenera kuchita.”
11 Anzanga anandigwira dzanja kupita nane ku Damasiko, popeza kuwala kunja kunandichititsa khungu.
12 “Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu.
13 Iye anayimirira pafupi nane nati, ‘Mʼbale Saulo, penyanso!’ Ndipo nthawi yomweyo ndinapenya ndikumuona iyeyo.
14 “Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake.
15 Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva.
16 Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.’
17 “Nditabwerera ku Yerusalemu, ndikupemphera mʼNyumba ya Mulungu, ndinachita ngati ndakomoka.
18 Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’”
19 Ine ndinayankha Ambuye kuti, “Anthu awa akudziwa kuti ine ndinkapita ku sunagoge iliyonse ndipo ndinkawaponya mʼndende ndi kuwakwapula amene ankakhulupirira inu.
20 Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”
21 Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti, “Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.”
22 Gulu la anthu linamvetsera mawu a Paulo mpaka pamene ananena izi, kenaka anakweza mawu awo nafuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi! Ngosayenera kukhala moyo!”
23 Akufuwula ndi kuponya zovala zawo ndi kuwaza fumbi kumwamba,
24 mkulu wa asilikali analamulira kuti amutenge Paulo kupita naye ku malo a asilikali. Iye analamula kuti Paulo akwapulidwe kwambiri ndi kumufunsa kuti apeze chimene anthu ankafuwulira chotere.
25 Atamumanga kuti amukwapule, Paulo anati kwa msilikali wolamulira asilikali 100 amene anayima pamenepo, “Kodi malamulo amalola kukwapula nzika ya Chiroma imene sinapezedwe yolakwa?”
26 Wolamulira asilikali 100 uja atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali ndi kumufotokozera. Iye anafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani ndi munthuyu amene ndi nzika ya Chiroma?”
27 Mkulu wa asilikali uja anapita kwa Paulo ndipo anamufunsa kuti, “Tandiwuze, kodi ndiwe nzika ya Chiroma?” Paulo anayankha kuti, “Inde.”
28 Kenaka mkulu wa asilikaliyo anati, “Ine ndinapereka ndalama zambiri kuti ndikhale nzika.” Paulo anayankha kuti, “Koma ine ndinabadwa nzika.”
29 Iwo amene anati amufunse analeka nthawi yomweyo. Mkulu wa asilikali uja anachita mantha atazindikira kuti wamanga Paulo amene ndi nzika ya Chiroma.
30 Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.