< Machitidwe a Atumwi 2 >
1 Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi.
Kad je napokon došao dan Pedesetnice, svi su bili zajedno na istome mjestu.
2 Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala.
I eto iznenada šuma s neba, kao kad se digne silan vjetar. Ispuni svu kuću u kojoj su bili.
3 Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo.
I pokažu im se kao neki ognjeni razdijeljeni jezici te siđe po jedan na svakoga od njih.
4 Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.
Svi se napuniše Duha Svetoga i počeše govoriti drugim jezicima, kako im već Duh davaše zboriti.
5 Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi.
A u Jeruzalemu su boravili Židovi, ljudi pobožni iz svakog naroda pod nebom.
6 Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana.
Pa kad nasta ona huka, strča se mnoštvo i smetÄe jer ih je svatko čuo govoriti svojim jezikom.
7 Mothedwa nzeru anafunsana kuti, “Kodi anthu onse amene akuyankhulawa si Agalileya?
Svi su bili izvan sebe i divili se govoreći: “Gle! Nisu li svi ovi što govore Galilejci?
8 Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo?
Pa kako to da ih svatko od nas čuje na svojem materinskom jeziku?
9 Apanti, Amedi ndi Aelami; okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya,
Parti, Međani, Elamljani, žitelji Mezopotamije, Judeje i Kapadocije, Ponta i Azije,
10 ku Frugiya ndi Pamfiliya, ku Igupto ndi ku madera a ku Libiya kufupi ndi ku Kurene; alendo ochokera ku Roma,
Frigije i Pamfilije, Egipta i krajeva libijskih oko Cirene, pridošlice Rimljani,
11 Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.”
Židovi i sljedbenici, Krećani i Arapi - svi ih mi čujemo gdje našim jezicima razglašuju veličanstvena djela Božja.”
12 Modabwa ndi mothedwa nzeru anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Zimenezi zikutanthauzanji?”
Svi su izvan sebe zbunjeno jedan drugog pitali: “Što bi to moglo biti?”
13 Koma ena anawaseka nati, “Aledzera vinyo watsopano.”
Drugi su pak, podrugujući se, govorili: “Slatkog su se vina ponapili!”
14 Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena.
A Petar zajedno s jedanaestoricom ustade, podiže glas i prozbori: “Židovi i svi što boravite u Jeruzalemu, ovo znajte i riječi mi poslušajte:
15 Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa!
Nisu ovi pijani, kako vi mislite - ta istom je treća ura dana -
16 Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:
nego to je ono što je rečeno po proroku Joelu:
17 “‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, anyamata anu adzaona masomphenya, nkhalamba zanu zidzalota maloto.
“U posljednje dane, govori Bog: Izlit ću Duha svoga na svako tijelo i proricat će vaši sinovi i kćeri, vaši će mladići gledati viđenja, a starci vaši sne sanjati.
18 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi, ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.
Čak ću i na sluge i sluškinje svoje izliti Duha svojeg u dane one i proricat će.
19 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano, ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
Pokazat ću čudesa na nebu gore i znamenja na zemlji dolje, krv i oganj i stupove dima.
20 Dzuwa lidzadetsedwa ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.
Sunce će se prometnut u tminu, a mjesec u krv prije nego svane Dan Gospodnji velik i slavan.
21 Ndipo aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’
I tko god prizove ime Gospodnje bit će spašen.”
22 “Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa.
“Izraelci, čujte ove riječi: Isusa Nazarećanina, čovjeka kojega Bog pred vama potvrdi silnim djelima, čudesima i znamenjima koja, kao što znate, po njemu učini među vama -
23 Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda.
njega, predana po odlučenu naumu i promislu Božjem, po rukama bezakonika razapeste i pogubiste.
24 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.
Ali Bog ga uskrisi oslobodivši ga grozote smrti jer ne bijaše moguće da ona njime ovlada.
25 Pakuti Davide ananena za Iye kuti, “‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse. Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja, Ine sindidzagwedezeka.
David doista za nj kaže: Gospodin mi je svagda pred očima jer mi je zdesna da ne posrnem.
26 Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera; thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo.
Stog mi se raduje srce i kliče jezik, pa i tijelo mi spokojno počiva.
27 Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda, kapena kulekerera Woyerayo kuti awole. (Hadēs )
Jer mi nećeš ostaviti dušu u Podzemlju ni dati da pravednik tvoj truleži ugleda. (Hadēs )
28 Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo; Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
Pokazat ćeš mi stazu života, ispuniti me radošću lica svoga.
29 “Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino.
Braćo, dopustite da vam otvoreno kažem: praotac je David umro, pokopan je i eno mu među nama groba sve do današnjeg dana.
30 Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu.
Ali kako je bio prorok i znao da mu se zakletvom zakle Bog plod utrobe njegove posaditi na prijestolje njegovo,
31 Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole. (Hadēs )
unaprijed je vidio i navijestio uskrsnuće Kristovo: Nije ostavljen u Podzemlju niti mu tijelo truleži ugleda. (Hadēs )
32 Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi.
Toga Isusa uskrisi Bog! Svi smo mi tomu svjedoci.
33 Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi.
Desnicom dakle Božjom uzvišen, primio je od Oca Obećanje, Duha Svetoga, i izlio ga kako i sami gledate i slušate.
34 Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti, “‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti: Khala kudzanja langa lamanja
Ta David nije bio uznesen na nebesa, a veli: Reče Gospodin Gospodinu mojemu: 'Sjedi mi zdesna'
35 mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.’
dok ne položim neprijatelje tvoje za podnožje nogama tvojim!
36 “Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”
Pouzdano dakle neka znade sav dom Izraelov da je toga Isusa kojega vi razapeste Bog učinio i Gospodinom i Kristom.”
37 Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?”
Kad su to čuli, duboko potreseni rekoše Petru i drugim apostolima: “Što nam je činiti, braćo?”
38 Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Petar će im: “Obratite se i svatko od vas neka se krsti u ime Isusa Krista da vam se oproste grijesi i primit ćete dar, Duha Svetoga.
39 Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.”
Ta za vas je ovo obećanje i za djecu vašu i za sve one izdaleka, koje pozove Gospodin Bog naš.”
40 Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.”
I mnogim je drugim riječima još svjedočio i hrabrio ih: “Spasite se od naraštaja ovog opakog!”
41 Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.
I oni prigrliše riječ njegovu i krstiše se te im se u onaj dan pridruži oko tri tisuće duša.
42 Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera.
Bijahu postojani u nauku apostolskom, u zajedništvu, lomljenju kruha i molitvama.
43 Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita.
Strahopoštovanje obuzimaše svaku dušu: apostoli su činili mnoga čudesa i znamenja.
44 Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse.
Svi koji prigrliše vjeru bijahu združeni i sve im bijaše zajedničko.
45 Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake.
Sva bi imanja i dobra prodali porazdijelili svima kako bi tko trebao.
46 Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona.
Svaki bi dan jednodušno i postojano hrlili u Hram, u kućama bi lomili kruh te u radosti i prostodušnosti srca zajednički uzimali hranu
47 Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.
hvaleći Boga i uživajući naklonost svega naroda. Gospodin je pak danomice zajednici pridruživao spasenike.