< Machitidwe a Atumwi 19 >

1 Apolo ali ku Korinto, Paulo anadutsa mʼmayiko a ku mtunda ndipo anafika ku Efeso. Kumeneko anapeza ophunzira ena.
Factum est autem, cum Apollo esset Corinthi, ut Paulus peragratis superioribus partibus veniret Ephesum, et inveniret quosdam de discipulis:
2 Iye anawafunsa kuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira?” Iwo anayankha kuti, “Ayi, ife sitinamvepo kuti kuli Mzimu Woyera.”
dixitque ad eos: Si Spiritum sanctum accepistis credentes? At illi dixerunt ad eum: Sed neque si Spiritus sanctus est, audivimus.
3 Tsono Paulo anawafunsa kuti, “Nanga munabatizidwa ndi ubatizo wotani?” Iwo anati, “Ubatizo wa Yohane.”
Ille vero ait: In quo ergo baptizati estis? Qui dixerunt: In Ioannis baptismate.
4 Paulo anati, “Ubatizo wa Yohane unali wa kutembenuka mtima. Iye anawuza anthu kuti akhulupirire amene amabwera, ameneyo ndiye Yesu.”
Dixit autem Paulus: Ioannes baptizavit baptismo poenitentiae populum, dicens: In eum, qui venturus esset post ipsum, ut crederent, hoc est, in Iesum.
5 Atamva zimenezi, anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu.
His auditis, baptizati sunt in nomine Domini Iesu.
6 Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera.
Et cum imposuisset illis manus Paulus, venit Spiritus sanctus super eos, et loquebantur linguis, et prophetabant.
7 Anthu onsewo analipo khumi ndi awiri.
Erant autem omnes viri fere duodecim.
8 Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu.
Introgressus autem synagogam, cum fiducia loquebatur per tres menses, disputans, et suadens de regno Dei.
9 Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano.
Cum autem quidam indurarentur, et non crederent, maledicentes viam Domini coram multitudine, discedens ab eis, segregavit discipulos, quotidie disputans in schola tyranni cuiusdam.
10 Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, kotero kuti Ayuda onse ndi Agriki amene amakhala ku Asiya anamva Mawu a Ambuye.
Hoc autem factum est per biennium, ita ut omnes, qui habitabant in Asia, audirent verbum Domini, Iudaei atque Gentiles.
11 Mulungu anachita zodabwitsa zapadera kudzera mwa Paulo.
Virtutesque non modicas quaslibet faciebat Deus per manum Pauli:
12 Kotero kuti mipango yopukutira thukuta ndi yovala pogwira ntchito, zomwe zinakhudza thupi la Paulo amapita nazo kwa odwala ndipo amachiritsidwa ndiponso mizimu yoyipa mwa iwo imatuluka.
ita ut etiam super languidos deferrentur a corpore eius sudaria, et semicinctia, et recedebant ab eis languores, et spiritus nequam egrediebantur.
13 Ayuda ena amene ankayendayenda kutulutsa mizimu yoyipa anayesa kugwiritsa ntchito dzina la Ambuye Yesu pa amene anali ndi ziwanda. Iwo popemphera amati, “Ine ndikulamulira utuluke, mʼdzina la Yesu amene Paulo amamulalikira.”
Tentaverunt autem quidam et de circumeuntibus Iudaeis exorcistis, invocare super eos, qui habebant spiritus malos, nomen Domini Iesu, dicentes: Adiuro vos per Iesum, quem Paulus praedicat.
14 Amene ankachita zimenezi anali ana asanu ndi awiri a Skeva, mkulu wa ansembe wa Chiyuda.
Erant autem cuiusdam Iudaei nomine Scevae principis sacerdotum septem filii, qui hoc faciebant.
15 Tsiku lina mzimu woyipa unawayankha kuti, “Yesu ndimamudziwa ndiponso Paulo ndimamudziwa, nanga inu ndinu ndani?”
Respondens autem spiritus nequam dixit eis: Iesum novi, et Paulum scio: vos autem qui estis?
16 Pamenepo munthu amene anali ndi mzimu woyipa anawalumphira nawagwira onse. Iye anawamenya kwambiri, kotero kuti anathawa mʼnyumbamo ali maliseche, akutuluka magazi.
Et insiliens in eos homo, in quo erat daemonium pessimum, et dominatus amborum, invaluit contra eos, ita ut nudi, et vulnerati effugerent de domo illa.
17 Ayuda ndi Agriki okhala ku Efeso atamva zimenezi, anachita mantha, ndipo anthu anachitira ulemu dzina la Ambuye Yesu koposa.
Hoc autem notum factum est omnibus Iudaeis, atque Gentilibus, qui habitabant Ephesi: et cecidit timor super omnes illos, et magnificabatur nomen Domini Iesu.
18 Ambiri a iwo amene tsopano anakhulupirira anafika ndi kuvomereza poyera ntchito zawo zoyipa.
Multique credentium veniebant, confitentes, et annunciantes actus suos.
19 Ambiri amene amachita za matsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi nawatentha pamaso pa anthu onse. Atawonkhetsa mtengo wa mabukuwo, unakwanira ndalama zasiliva 50,000.
Multi autem ex eis, qui fuerant curiosa sectati, contulerunt libros, et combusserunt eos coram omnibus: et computatis pretiis illorum, invenerunt pecuniam denariorum quinquaginta millium.
20 Kotero Mawu a Ambuye anapitirira kufalikira ndipo anagwira ntchito mwamphamvu.
Ita fortiter crescebat verbum Dei, et confirmabatur.
21 Zonsezi zitachitika Paulo anatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Makedoniya ndi ku Akaya. Iye anati, “Kuchokera kumeneko, ndiyenera kukafikanso ku Roma.”
His autem expletis, proposuit Paulus in Spiritu, transita Macedonia et Achaia ire Ierosolymam, dicens: quoniam postquam fuero ibi, oportet me et Romam videre.
22 Iye anatuma anthu awiri amene amamuthandiza, Timoteyo ndi Erasto ku Makedoniya, pamene iye anakhalabe ku Asiya kwa kanthawi.
Mittens autem in Macedoniam duos ex ministrantibus sibi, Timotheum, et Erastum, ipse remansit ad tempus in Asia.
23 Pa nthawi yomweyo panachitika chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye.
Facta est autem illo tempore turbatio non minima de via Domini.
24 Mmisiri wantchito zasiliva, dzina lake Demetriyo, amene amapanga mafano asiliva a Atemi ankabweretsa phindu lalikulu kwa amisiri a kumeneko.
Demetrius enim quidam nomine, argentarius, faciens aedes argenteas Dianae, praestabat artificibus non modicum quaestum:
25 Iye anasonkhanitsa pamodzi amisiriwo, pamodzinso ndi anthu ena ogwira ntchito yomweyo ndipo anati, “Anthu inu, mukudziwa kuti ife timapeza chuma chathu kuchokera pa ntchito imeneyi.
quos convocans, et eos, qui huiusmodi erant opifices, dixit: Viri, scitis quia de hoc artificio est nobis acquisitio:
26 Ndipo inu mukuona ndi kumva kuti munthu uyu Paulo wakopa ndi kusokoneza anthu ambiri a ku Efeso ndiponso pafupifupi dziko lonse la Asiya. Iye akunena kuti milungu yopangidwa ndi anthu si milungu ayi.
et videtis, et auditis quia non solum Ephesi, sed pene totius Asiae, Paulus hic suadens avertit multam turbam, dicens: Quoniam non sunt dii, qui manibus fiunt.
27 Choopsa ndi chakuti sikungowonongeka kwa ntchito yathu yokha ayi, komanso kuti nyumba ya mulungu wamkulu wamkazi Atemi idzanyozedwa ndipo mulungu wamkazi weniweniyo amene amapembedzedwa ku Asiya konse ndi dziko lapansi, ukulu wake udzawonongekanso.”
Non solum autem haec periclitabitur nobis pars in redargutionem venire, sed et magnae Dianae templum in nihilum reputabitur, sed et destrui incipiet maiestas eius, quam tota Asia, et orbis colit.
28 Atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anayamba kufuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi.”
His auditis, repleti sunt ira, et exclamaverunt dicentes: Magna Diana Ephesiorum.
29 Nthawi yomweyo mu mzinda wonse munabuka chipolowe. Anthu anagwira Gayo ndi Aristariko, anzake a Paulo a ku Makedoniya, ndipo anathamangira nawo ku bwalo la masewero.
Et impleta est civitas confusione, et impetum fecerunt uno animo in theatrum, rapto Gaio, et Aristarcho Macedonibus, comitibus Pauli.
30 Paulo anafuna kulowa pakati pa gulu la anthu, koma ophunzira anamuletsa.
Paulo autem volente intrare in populum, non permiserunt discipuli.
31 Ngakhale olamulira ena aderalo, amene anali abwenzi a Paulo, anatumiza uthenga kumuletsa kuti asayesere kulowa mʼbwalomo.
Quidam autem et de Asiae principibus, qui erant amici eius, miserunt ad eum rogantes ne se darent in theatrum:
32 Munali chisokonezo mʼbwalomo pakuti ena amafuwula zina, enanso zina. Anthu ambiri sanadziwe ngakhale chomwe anasonkhanira.
alii autem aliud clamabant. Erat enim Ecclesia confusa: et plures nesciebant qua ex causa convenissent.
33 Ayuda anamukankhira Alekisandro kutsogolo, ndipo ena anafuwula kumulangiza iye. Iye anatambasula dzanja kuti anthu akhale chete kuti afotokozere anthu nkhaniyo.
De turba autem detraxerunt Alexandrum, propellentibus eum Iudaeis. Alexander autem manu silentio postulato, volebat reddere rationem populo.
34 Koma pamene anthuwo anazindikira kuti ndi Myuda, onse pamodzi kwa maora awiri anafuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi wa ku Efeso!”
Quem ut cognoverunt Iudaeum esse, vox facta una est omnium, quasi per horas duas clamantium: Magna Diana Ephesiorum.
35 Mlembi wa mzindawo anakhazikitsa bata gulu la anthuwo ndipo anati, “Anthu a ku Efeso, kodi ndani pa dziko lonse lapansi amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso umayangʼanira nyumba ya mulungu wamkulu Atemi ndi fanizo lake, limene linagwa kuchokera kumwamba?
Et cum sedasset scriba turbas, dixit: Viri Ephesii, quis enim est hominum, qui nesciat Ephesiorum civitatem cultricem esse magnae Dianae, Iovisque prolis?
36 Chifukwa chake popeza zinthu izi palibe amene angazikane, inu mukuyenera kukhala chete osachita kanthu kalikonse mofulumira.
Cum ergo his contradici non possit, oportet vos sedatos esse, et nihil temere agere.
37 Inu mwabweretsa anthu awa pano, ngakhale kuti iwo sanabe mʼnyumba zathu zamapemphero kapena kunenera chipongwe mulungu wathu wamkazi.
Adduxistis enim homines istos, neque sacrilegos, neque blasphemantes deam vestram.
38 Ngati tsono Demetriyo ndi amisiri anzake ali ndi nkhani ndi munthu wina aliyense, mabwalo a milandu alipo, oweruza aliponso. Akhoza kukapereka nkhaniyo kwa oweruza milanduwo.
Quod si Demetrius, et qui cum eo sunt artifices, habent adversus aliquem causam, conventus forenses aguntur, et proconsules sunt, accusent invicem.
39 Ngati mukufuna kubweretsa kanthu kali konse, ziyenera kukatsimikizidwa ndi bwalo lovomerezeka.
Si quid autem alterius rei quaeritis: in legitima Ecclesia poterit absolvi.
40 Monga mmene zililimu, ife titha kuzengedwa mlandu woyambitsa chipolowe chifukwa cha zimene zachitika lerozi. Motero ife sitingathe kufotokoza za chipolowechi popeza palibe nkhani yake.”
Nam et periclitamur argui seditionis hodiernae: cum nullus obnoxius sit (de quo possimus reddere rationem) concursus istius.
41 Iye atatha kunena zimenezi anawuza gulu la anthulo kuti libalalike.
Et cum haec dixisset, dimisit Ecclesiam.

< Machitidwe a Atumwi 19 >