< Machitidwe a Atumwi 18 >

1 Zitatha izi, Paulo anachoka ku Atene ndipo anapita ku Korinto.
Подир това Павел тръгна от Атина и дойде в Коринт,
2 Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Akula, nzika ya ku Ponto amene anali atangofika kumene kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Paulo anapita kukawaona.
О А когато го замолиха да поседи повечко време, той не склони;
3 Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi.
И понеже имаше същото занятие, седеше у тях и работеха; защото занятието им беше да правят шатри.
4 Tsiku la Sabata lililonse Paulo amakambirana ndi anthu mʼsunagoge, kufuna kukopa Ayuda ndi Agriki.
И всяка събота той разискваше в синагогата с юдеи и гърци, и се стараеше да ги убеждава.
5 Sila ndi Timoteyo atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo ankangogwira ntchito yolalikira yokha basi, kuchitira umboni Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.
А когато Сила и Тимотей слязоха от Македония, Павел се притесняваше от своя дух да свидетелствува на юдеите, че Исус е Христос.
6 Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, “Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina.”
Но понеже те се противяха и хулеха, той отърси дрехите си и рече: Кръвта ви да бъде на главите ви; аз съм чист от нея; отсега ще отивам между езичниците.
7 Ndipo Paulo anatuluka mʼsunagoge napita ku nyumba yoyandikana ndi sunagoge ya Tito Yusto, munthu wopembedza Mulungu.
И като се премести оттам, дойде в дома на някого си на име Тит Юст, който се кланяше на Бога, и чиято къща беше до синагогата.
8 Krispo, mkulu wa sunagoge, pamodzi ndi a pa banja lake lonse anakhulupirira Ambuye; ndiponso Akorinto ambiri amene anamva Paulo akulalikira anakhulupiriranso nabatizidwa.
А Крисп, началникът на синагогата, повярва в Господа с целия си дом; и мнозина от Коринтяните, като слушаха, вярваха и се кръщаваха.
9 Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, “Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete.
И Господ каза на Павла нощя във видение: Не не бой се, но говори и не млъквай;
10 Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri.”
защото аз съм с тебе, и никой няма да те нападне та да ти стори зло; защото имам много люде в тоя град.
11 Choncho Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi akuphunzitsa Mawu a Mulungu.
И той преседя там година и шест месеца та ги поучаваше в Божието слово.
12 Galiyo ali mkulu wa boma wa ku Akaya, Ayuda mogwirizana anamugwira Paulo napita naye ku bwalo la milandu.
А когато Галион беше управител в Ахаия, юдеите се подигнаха единодушно против Павла, доведоха го пред съдилището, и казаха:
13 Iwo anati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwanjira zotsutsana ndi malamulo athu.”
Тоя убеждава човеците да се кланят на Бога несъгласно закона.
14 Pamene Paulo ankati ayankhule, Galiyo anati kwa Ayuda, “Ukanakhala mlandu wochita choyipa kapena wolakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino.
Но когато Павел щеше да отвори уста, Галион рече на юдеите: Ако беше ако беше въпрос за някоя неправда или грозно злодеяние, о юдеи, разбира се би трябвало да ви търпя;
15 Koma popeza ndi nkhani yokhudza mawu, mayina ndi malamulo anu, kambiranani nokhanokha. Ine sindidzaweruza zinthu zimenezi.”
но ако въпросите са за учение, за имена и за вашия закон, гледайте си сами; аз не ща да съм съдия на такива работи.
16 Kotero iye anawapirikitsa mʼbwalo la milandu.
И изпъди ги от съдилището.
17 Kenaka iwo anagwira Sositene, mkulu wa sunagoge, ndipo anamumenya mʼbwalo la milandu momwemo. Koma Galiyo sanasamale zimenezi.
Тогава те всички хванаха началника на Синагогата Состена, та го биха пред съдилището; но Галион, не искаше и да знае за това.
18 Paulo anakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Kenaka anawasiya abale nakwera sitima ya pamadzi kupita ku Siriya, pamodzi ndi Prisila ndi Akula. Asanakakwere sitima ya pamadzi, anameta tsitsi lake ku Kenkreya chifukwa anali atalumbira.
А Павел, след като поседя там още доволно време, прости се с братята си, и отплува за Сирия (и с него Прискила и Акила), като си острига главата в Кенхрея, защото имаше обрек.
19 Iwo anafika ku Efeso, kumene Paulo anasiyako Prisila ndi Akula. Iye yekha analowa mʼsunagoge nakambirana ndi Ayuda.
Като стигнаха Ефес, той ги остави там, а сам влезе в Синагогата и разискваше с юдеите.
20 Iwo atapempha kuti akakhale nawo nthawi yayitali, iye anakana.
но се прости с тях, казвайки; Ако ще Бог, пак ще се върна при вас. И отплува от Ефес.
21 Koma pamene amachoka anawalonjeza kuti, “Ndidzabweranso Mulungu akalola.” Ndipo anakwera sitima ya pamadzi kuchoka ku Efeso.
А когато го замолиха да поседи повечко време, той не склони;
22 Pamene Paulo anafika ku Kaisareya, anakwera kukapereka moni ku mpingo kenaka anatsikira ku Antiokeya.
И като слезе в Кесария, възлезе в Ерусалим та поздрави църквата и после слезе в Антиохия.
23 Atakhala kwa kanthawi ku Antiokeya, Paulo anachokako nayendera madera onse a ku Galatiya ndi ku Frugiya kulimbikitsa ophunzira onse.
И като поседя там няколко време, излезе и обикаляше наред Галатийската и Фригийската страна та утвърждаваше всичките ученици.
24 Pa nthawi yomweyi Myuda wina dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Alekisandriya anafika ku Efeso. Anali munthu wophunzira ndi wodziwa bwino Malemba.
И някой си юдеин на име Аполос, роден в Александрия, човек учен и силен в писанията, дойде в Ефес.
25 Apoloyu anaphunzitsidwa njira ya Ambuye, ndipo anayankhula ndi changu chachikulu naphunzitsa za Yesu molondola, ngakhale amadziwa ubatizo wa Yohane wokha.
Той беше наставен в Господния път, и, бидейки по дух усърден, говореше и поучаваше прилежно за Исуса то а познаваше само Йоановото кръщение,
26 Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.
Той почна да говори дързостно в синагогата; но Прискила и Акила, като го чуха, прибраха го и му изложиха по-точно Божия път.
27 Pamene Apolo anafuna kupita ku Akaya, abale anamulimbikitsa, nalemba kalata kwa ophunzira a kumeneko kuti amulandire. Atafika kumeneko, anathandiza kwambiri amene anakhulupirira mwachisomo.
И когато се канеше да замине за Ахаия, братята го насърчиха, и писаха до учениците да го приемат; и той като дойде помогна много на повярвалите чрез благодатта;
28 Pakuti iye anatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza kuchokera mʼMalemba kuti Yesu ndiye Khristu.
защото силно опровергаваше юдеите, и то публично, като доказваше от писанието, че Исус е Христос.

< Machitidwe a Atumwi 18 >