< Machitidwe a Atumwi 17 >
1 Atadutsa ku Amfipoli ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge ya Ayuda.
Now when they had passed through Amphipolis and Apollonia, they came to Thessalonica, where there was a Jewish synagogue.
2 Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu,
Paul, as was his custom, went in to them, and for three Sabbath days reasoned with them from the Scriptures,
3 kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, “Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu.”
explaining and demonstrating that the Christ had to suffer and rise again from the dead, and saying, "This Jesus, whom I proclaim to you, is the Christ."
4 Ena mwa Ayuda anakopeka mtima ndipo anatsatira Paulo ndi Sila, monganso linachitira gulu lalikulu la Agriki woopa Mulungu, pamodzi ndi amayi odziwika ambiri.
Some of them were persuaded, and joined Paul and Silas, as did a large number of the devout Greeks, and not a few of the prominent women.
5 Koma Ayuda ena anachita nsanje; kotero anasonkhanitsa anthu akhalidwe loyipa ochokera pa msika ndipo napanga gulu nayambitsa chipolowe mu mzindawo. Anathamangira ku nyumba ya Yasoni kukafuna Paulo ndi Sila kuti awabweretse pa gulu la anthu.
But the Jews, being moved with jealousy, took along some wicked men from the marketplace, and gathering a crowd, set the city in an uproar. Assaulting the house of Jason, they sought to bring them out to the people.
6 Koma atalephera kuwapeza, anakokera Yasoniyo ndi abale ena ku bwalo la akulu a mzindawo akufuwula kuti, “Anthu awa, Paulo ndi Sila, amene akhala akusokoneza dziko lonse lapansi, tsopano afikanso kuno.
When they did not find them, they dragged Jason and certain brothers before the rulers of the city, crying, "These who have turned the world upside down have come here also,
7 Yasoni ndiye anawalandira mʼnyumba mwake. Onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara pomanena kuti palinso mfumu ina, yotchedwa Yesu.”
whom Jason has received. These all act contrary to the decrees of Caesar, saying that there is another king, Jesus."
8 Atamva zimenezi, gulu la anthu ndi akulu a mzinda anavutika mu mtima.
The crowd and the rulers of the city were troubled when they heard these things.
9 Iwo analipiritsa Yasoni ndi anzakewo ndipo anawamasula.
When they had taken security from Jason and the rest, they let them go.
10 Mdima utagwa, abale anatumiza Paulo ndi Sila ku Bereya. Atafika kumeneko anapita ku sunagoge ya Ayuda.
The brothers immediately sent Paul and Silas away by night to Beroea. When they arrived, they went into the Jewish synagogue.
11 Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.
Now these were more noble than those in Thessalonica, in that they received the word with all readiness of the mind, examining the Scriptures daily to see whether these things were so.
12 Ayuda ambiri anakhulupirira, monga anachitiranso amayi ndi amuna ambiri odziwika a Chigriki.
Many of them therefore believed; also of the prominent Greek women, and not a few men.
13 Ayuda a ku Tesalonika atadziwa kuti Paulo akulalikira Mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko, ndi kuwutsa mitima ya anthu nayambitsa chisokonezo.
But when the Jews of Thessalonica had knowledge that the word of God was proclaimed by Paul at Beroea also, they came there likewise, inciting and disturbing the crowds.
14 Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo ku nyanja koma Sila ndi Timoteyo anatsalira ku Bereya.
Then the brothers immediately sent out Paul to go as far as to the sea, and Silas and Timothy still stayed there.
15 Anthu amene anamuperekeza Paulo nafika naye ku Atene, ndipo anabwerera ku Bereya atawuzidwa kuti Sila ndi Timoteyo amutsatire msanga.
But those who escorted Paul brought him as far as Athens. Receiving a commandment to Silas and Timothy that they should come to him very quickly, they departed.
16 Paulo akudikira Timoteyo ndi Sila ku Atene, anavutika mu mtima kwambiri poona kuti mzindawo unali odzaza ndi mafano.
Now while Paul waited for them at Athens, his spirit was provoked within him as he saw the city full of idols.
17 Tsono anakambirana ndi Ayuda ndi Agriki amene amaopa Mulungu mʼsunagoge, komanso anthu amene amapezeka pa msika tsiku ndi tsiku ndi ena amene amakumana nawo.
So he reasoned in the synagogue with the Jews and the devout persons, and in the marketplace every day with those who met him.
18 Gulu la Aepikureya ndi Astoiki, anthu anzeru, anayamba kutsutsana naye. Ena a iwo anafunsa kuti, “Kodi wolongololayu akufuna kunena chiyani?” Enanso anati, “Akuoneka ngati akulalikira milungu yachilendo.” Iwo ananena zimenezi chifukwa Paulo amalalikira Uthenga Wabwino wa Yesu ndi kuuka kwa akufa.
Some of the Epicurean and Stoic philosophers also were conversing with him. Some said, "What does this babbler want to say?" Others said, "He seems to be advocating foreign deities," because he preached Jesus and the resurrection.
19 Kenaka iwo anamutenga nafika naye ku bwalo la Areopagi kumene anamufunsa kuti, “Kodi tingadziweko chiphunzitso chatsopano chimene ukuchifotokozachi?
They took hold of him, and brought him to the Areopagus, saying, "May we know what this new teaching is, which is spoken by you?
20 Iwe ukubweretsa zinthu zina zachilendo mʼmakutu mwathu, ndipo ife tikufuna tidziwe tanthauzo lake.”
For you bring certain strange things to our ears. We want to know therefore what these things mean."
21 Atene onse ndi alendo amene amakhala kumeneko samachita kanthu kena koma kufotokoza ndi kumvera fundo zatsopano.
Now all the Athenians and the strangers living there spent their time in nothing else, but either to tell or to hear some new thing.
22 Paulo anayimirira mʼbwalo la Areopagi nati: “Inu anthu a ku Atene! Ine ndikuona kuti mʼnjira zonse ndinu opembedza kwambiri.
Paul stood in the middle of the Areopagus, and said, "You men of Athens, I perceive that you are very religious in all things.
23 Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, kwa mulungu wosadziwika. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira.
For as I passed along, and observed the objects of your worship, I found also an altar with this inscription: 'TO AN UNKNOWN GOD.' What therefore you worship in ignorance, this I announce to you.
24 “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja.
The God who made the world and all things in it, he, being Lord of heaven and earth, does not dwell in temples made with hands,
25 Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse.
neither is he served by human hands, as though he needed anything, seeing he himself gives to all life and breath, and all things.
26 Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale.
He made from one blood every nation of the human race to dwell on all the surface of the earth, having determined appointed seasons, and the boundaries of their dwellings,
27 Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.
that they should seek God, if perhaps they might reach out for him and find him, though he is not far from each one of us.
28 ‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’
'For in him we live, and move, and have our being.' As some of your own poets have said, 'For we are also his offspring.'
29 “Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu.
Being then the offspring of God, we ought not to think that the Divine Nature is like gold, or silver, or stone, engraved by human art and design.
30 Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima.
The times of ignorance therefore God overlooked. But now he commands that all people everywhere should repent,
31 Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”
because he has appointed a day in which he will judge the world in righteousness by the man whom he has ordained; of which he has given assurance to everyone by raising him from the dead."
32 Atamva za kuuka kwa akufa, ena a iwo anaseka, koma enanso anati, “Ife tikufuna tidzamvenso zimenezi tsiku lina.”
Now when they heard of the resurrection of the dead, some mocked; but others said, "We want to hear you again concerning this."
33 Ndipo Paulo anatuluka mʼBwalolo.
Thus Paul went out from among them.
34 Anthu ena ochepa anamutsatira Paulo ndipo anakhulupirira. Pakati pawo panali Dionisiyo mmodzi wa bwalo la Areopagi ndi mayi wina wotchedwa Damalisi ndi enanso.
But some people joined with him, and believed, among whom also was Dionysius the Areopagite, and a woman named Damaris, and others with them.