< Machitidwe a Atumwi 13 >

1 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo.
Now there were in the church that was at Antioch certain prophets and teachers; as Barnabas, and Simeon that was called Niger, and Lucius of Cyrene, and Manaen, who had been brought up with Herod the tetrarch, and Saul.
2 Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.”
As they ministered to the Lord, and fasted, the Holy Spirit said, Separate for me Barnabas and Saul for the work to which I have called them.
3 Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.
And when they had fasted and prayed, and laid their hands on them, they sent them away.
4 Barnaba ndi Saulo motumidwa ndi Mzimu Woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro.
So they, being sent forth by the Holy Spirit, departed to Seleucia; and from there they sailed to Cyprus.
5 Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira.
And when they were at Salamis, they preached the word of God in the synagogues of the Jews: and they had also John as their helper.
6 Iwo anayenda pa chilumba chonse mpaka anafika ku Pafo, kumeneko anapezanako ndi Myuda, wamatsenga amene analinso mneneri wonama dzina lake Barayesu.
And when they had gone through the isle to Paphos, they found a certain sorcerer, a false prophet, a Jew, whose name was Barjesus:
7 Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu.
Who was with the deputy of the country, Sergius Paulus, a prudent man; who called for Barnabas and Saul, and desired to hear the word of God.
8 Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire.
But Elymas the sorcerer ( for so is his name by interpretation ) withstood them, seeking to turn away the deputy from the faith.
9 Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati,
Then Saul, ( who also is called Paul, ) filled with the Holy Spirit, set his eyes on him,
10 “Iwe ndiwe mwana wa mdierekezi ndiponso mdani wa chilungamo! Ndiwe wodzaza ndi chinyengo cha mtundu uliwonse ndi kuchenjera konse. Kodi sudzaleka kupotoza njira zolungama za Ambuye?
And said, O full of all deceit and all mischief, thou child of the devil, thou enemy of all righteousness, wilt thou not cease to pervert the right ways of the Lord?
11 Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere.
And now, behold, the hand of the Lord is upon thee, and thou shalt be blind, not seeing the sun for a season. And immediately there fell on him a mist and a darkness; and he went about seeking some to lead him by the hand.
12 Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.
Then the deputy, when he saw what was done, believed, being astonished at the doctrine of the Lord.
13 Kuchokera ku Pafo, Paulo ndi anzake anayenda pa sitima ya pamadzi kupita ku Perga wa ku Pamfiliya, kumeneko Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu.
Now when Paul and his company loosed from Paphos, they came to Perga in Pamphylia: and John departing from them returned to Jerusalem.
14 Kuchokera ku Perga anapita ku Pisidiya wa ku Antiokeya. Pa tsiku la Sabata analowa mʼsunagoge, nakhala pansi.
But when they departed from Perga, they came to Antioch in Pisidia, and went into the synagogue on the sabbath day, and sat down.
15 Atawerenga mawu a mʼMalamulo ndi Aneneri, akulu a sunagoge anawatumizira mawu ndi kuti, “Abale ngati muli ndi mawu olimbikitsa nawo anthuwa, nenani.”
And after the reading of the law and the prophets the rulers of the synagogue sent to them, saying, Men, brethren, if ye have any word of exhortation for the people, say on.
16 Atayimirira, Paulo anakweza dzanja lake ndi kuti, “Inu Aisraeli ndiponso inu a mitundu ina amene mumapembedza Mulungu, tandimverani!
Then Paul stood up, and beckoning with his hand said, Men of Israel, and ye that fear God, listen.
17 Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu.
The God of this people Israel chose our fathers, and exalted the people when they dwelt as strangers in the land of Egypt, and with an high arm he brought them out of it.
18 Ndipo Iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu kwa zaka makumi anayi.
And about the time of forty years he bore their manners in the wilderness.
19 Mulungu anawagonjetsera mitundu isanu ndi iwiri ya ku Kanaani ndipo anapereka dzikolo kwa Israeli kuti likhale lawo.
And when he had destroyed seven nations in the land of Canaan, he divided their land to them by lot.
20 Izi zonse zinatenga zaka 450. “Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli.
And after these things, which took about four hundred and fifty years, he gave to them judges, until Samuel the prophet.
21 Kenaka anthu anapempha kuti awapatse mfumu, ndipo anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, wa fuko la Benjamini amene analamulira zaka makumi anayi.
And afterward they desired a king: and God gave to them Saul the son of Kish, a man of the tribe of Benjamin, by the space of forty years.
22 Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’
And when he had removed him, he raised up to them David to be their king; to whom also he gave testimony, and said, I have found David the son of Jesse, a man after my own heart, who shall fulfil all my will.
23 “Kuchokera mwa zidzukulu za munthu ameneyu, Mulungu anawutsa Yesu kukhala Mpulumutsi wa Aisraeli, monga analonjezera.
Of this man’s seed hath God according to his promise raised up to Israel a Saviour, Jesus:
24 Yesu asanabwere, Yohane analalikira kwa anthu onse Aisraeli za kutembenuka mtima ndi ubatizo.
After John had first preached before his coming the baptism of repentance to all the people of Israel.
25 Pamene Yohane amatsiriza ntchito yake anati: ‘Mukuganiza kuti ine ndine yani? Ine sindine ameneyo ayi, koma Iye akubwera pambuyo panga, amene ine sindine woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.’
And as John fulfilled his course, he said, Whom think ye that I am? I am not he. But, behold, there cometh one after me, whose shoes of his feet I am not worthy to loose.
26 “Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife.
Men, brethren, children of the stock of Abraham, and whoever among you feareth God, to you is the word of this salvation sent.
27 Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse.
For they that dwell at Jerusalem, and their rulers, because they knew him not, nor yet the words of the prophets which are read every sabbath, they have fulfilled them in condemning him.
28 Ngakhale sanapeze chifukwa choti afe, anapempha Pilato kuti amuphe.
And though they found no cause of death in him, yet they desired Pilate that he should be put to death.
29 Atachita zonse zimene zinalembedwa za Iye, iwo anamuchotsa pa mtengo ndipo anamuyika mʼmanda.
And when they had fulfilled all that was written concerning him, they took him down from the tree, and laid him in a sepulchre.
30 Koma Mulungu anamuukitsa,
But God raised him from the dead:
31 ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anayenda naye kuchokera ku Galileya mpaka ku Yerusalemu. Iwowa tsopano ndi mboni zake kwa anthu a Israeli.
And he was seen many days by them who came up with him from Galilee to Jerusalem, who are his witnesses to the people.
32 “Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu.
And we declare to you the glad tidings, that the promise which was made to the fathers,
33 Iye wakwaniritsa zimenezi kwa ife ana awo, poukitsa Yesu kuchokera kwa akufa. Monga zinalembedwa mu Salimo lachiwiri kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero ine ndakhala Atate ako.”
God hath fulfilled the same to us their children, in that he hath raised up Jesus again; as it is also written in the second psalm, Thou art my Son, this day have I begotten thee.
34 Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa: “‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’
And as concerning that he raised him from the dead, now no more to return to corruption, he said in this way, I will give you the sure mercies of David.
35 Nʼchifukwa chakenso zinalembedwa mu Salimo lina kuti, “‘Simudzalekerera woyera wanu kuti awole.’
Therefore he saith also in another psalm, Thou shalt not allow thy Holy One to see corruption.
36 “Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola.
For David, after he had served his own generation by the will of God, fell asleep, and was laid to his fathers, and saw corruption:
37 Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi.
But he, whom God raised again, saw no corruption.
38 “Nʼchifukwa chake, abale anga, dziwani kuti mwa Yesu chikhululukiro cha machimo chikulalikidwa.
Be it known to you therefore, men, brethren, that through this man is preached to you the forgiveness of sins:
39 Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose.
And by him all that believe are justified from all things, from which ye could not be justified by the law of Moses.
40 Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu:
Beware therefore, lest that come upon you, which is spoken in the prophets;
41 “‘Onani, inu anthu onyoza, dabwani ndipo wonongekani, chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu, inu simudzazikhulupirira ngakhale wina atakufotokozerani!’”
Behold, ye despisers, and wonder, and perish: for I work a work in your days, a work which ye shall by no means believe, though a man declare it to you.
42 Pamene Paulo ndi Barnaba amatuluka mʼSunagoge, anthu anawapempha kuti adzapitirize kuyankhula zinthu zimenezi Sabata linalo.
And when the Jews had gone out of the synagogue, the Gentiles besought that these words might be preached to them the next sabbath.
43 Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu.
Now when the congregation was broken up, many of the Jews and religious proselytes followed Paul and Barnabas: who, speaking to them, persuaded them to continue in the grace of God.
44 Pa Sabata linalo pafupifupi anthu onse a mu mzindawo anasonkhana kudzamva Mawu a Ambuye.
And the next sabbath came almost the whole city together to hear the word of God.
45 Pamene Ayuda anaona gulu la anthu, anachita nsanje ndipo anayankhula zamwano kutsutsana ndi zimene Paulo amanena.
But when the Jews saw the multitudes, they were filled with envy, and spoke against those things which were spoken by Paul, contradicting and blaspheming.
46 Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina. (aiōnios g166)
Then Paul and Barnabas became bold, and said, It was necessary that the word of God should first be spoken to you: but seeing ye reject it, and judge yourselves unworthy of everlasting life, lo, we turn to the Gentiles. (aiōnios g166)
47 Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife: “‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina, kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’”
For so hath the Lord commanded us, saying, I have set thee to be a light of the Gentiles, that thou shouldest be for salvation to the ends of the earth.
48 Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira. (aiōnios g166)
And when the Gentiles heard this, they were glad, and glorified the word of the Lord: and as many as were ordained to eternal life believed. (aiōnios g166)
49 Mawu a Ambuye anafalikira mʼchigawo chonse.
And the word of the Lord was proclaimed throughout all the region.
50 Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo.
But the Jews stirred up the devout and honourable women, and the chief men of the city, and raised persecution against Paul and Barnabas, and drove them out of their land.
51 Tsono iwo anasasa fumbi la ku mapazi awo powatsutsa, ndipo anapita ku Ikoniya.
But they shook off the dust of their feet against them, and came to Iconium.
52 Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndiponso ndi Mzimu Woyera.
And the disciples were filled with joy, and with the Holy Spirit.

< Machitidwe a Atumwi 13 >