< Machitidwe a Atumwi 10 >
1 Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Korneliyo, mkulu wa asilikali 100 wa gulu la Italiya.
Il y avait à Césarée un homme, nommé Corneille, centenier de la cohorte appelée Italique.
2 Iye ndi banja lake lonse amapembedza ndi kuopa Mulungu. Iye amathandiza osowa mowolowamanja ndipo amapemphera kwa Mulungu nthawi zonse.
Il était pieux et craignait Dieu, lui et toute sa maison; il faisait beaucoup d'aumônes au peuple et priait Dieu continuellement.
3 Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.”
Il vit clairement dans une vision, vers la neuvième heure du jour, un ange de Dieu, qui entrait chez lui, et qui lui dit: Corneille!
4 Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?” Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso.
Les yeux fixés sur l'ange et tout effrayé, il répondit: Qu'y a-t-il, Seigneur? L'ange lui dit: Tes prières et tes aumônes sont montées jusqu'à Dieu, et il s'en est souvenu.
5 Tsopano tuma anthu apite ku Yopa kuti akayitane munthu dzina lake Simoni Petro.
Maintenant donc, envoie des hommes à Joppé, et fais venir un certain Simon, surnommé Pierre.
6 Iye akukhala ndi Simoni mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.”
Il est logé chez Simon, le corroyeur, dont la maison est près de la mer.
7 Mngeloyo anayankhula naye anachoka, Korneliyo anayitana antchito ake awiri ndiponso msilikali mmodzi wa iwo amene ankamutumikira yemwe ankapembedza Mulungu.
Quand l'ange qui lui parlait se fut retiré. Corneille appela deux de ses serviteurs et un soldat pieux, de ceux qui étaient attachés à sa personne;
8 Iye anawafotokozera zonse zimene zinachitika ndipo anawatuma kuti apite ku Yopa.
et leur ayant tout raconté, il les envoya à Joppé.
9 Mmawa mwake, nthawi ili ngati 12 koloko anthuwo atayandikira mzindawo, Petro anakwera pa denga kukapemphera.
Le lendemain, comme ils étaient en route et qu'ils approchaient de la ville, Pierre monta sur le haut de la maison, vers la sixième heure, pour prier.
10 Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka.
Il eut faim et voulut prendre de la nourriture; et pendant qu'on la lui préparait, il fut ravi en extase.
11 Iye anaona kuthambo kutatsekuka, ndi chinthu china chikutsitsidwa pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa msonga zake zinayi.
Il vit le ciel ouvert, et un objet ressemblant à une grande nappe retenue aux quatre coins, qui descendait et s'abaissait jusqu'à terre;
12 Mʼmenemo munali nyama zonse zamiyendo inayi pamodzinso ndi zokwawa za dziko lapansi ndiponso mbalame zamlengalenga.
il s'y trouvait des quadrupèdes de toute espèce, des reptiles de la terre et des oiseaux du ciel.
13 Petro anamva mawu akuti, “Petro, dzuka, ipha nudye.”
Une voix lui dit: Pierre, lève-toi, tue et mange.
14 Petro anayankha kuti, “Ayi, Ambuye! Ine sindinadyepo kanthu kosayeretsedwa kapena konyansa.”
Mais Pierre répondit: Non, Seigneur; car je n'ai jamais rien mangé de souillé ni d'impur.
15 Petro anamvanso kachiwiri mawu akuti, “Usachiyese chonyansa chimene Mulungu wachiyeretsa.”
La voix, parlant une seconde fois, lui dit: Ce que Dieu a purifié, ne le regarde pas comme souillé!
16 Zimenezi zinachitika katatu ndipo nthawi yomweyo chinsalu chija chinatengedwanso kupita kumwamba.
Cela se répéta par trois fois; et aussitôt après, l'objet fut retiré dans le ciel.
17 Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata.
Pierre ne savait que penser de la vision qu'il avait eue, lorsque les hommes envoyés par Corneille, s'étant informés de la maison de Simon, se présentèrent à la porte.
18 Iwo anayitana nafunsa ngati Simoni amene amadziwika ndi dzina loti Petro amakhala kumeneko.
Ayant appelé, ils demandèrent si c'était là que logeait Simon, surnomme Pierre.
19 Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna.
Comme Pierre réfléchissait à cette vision, l'Esprit lui dit; Voici trois hommes qui te cherchent.
20 Dzuka, tsika. Usakayike upite nawo pakuti ndawatuma ndine.”
Lève-toi donc, descends, et pars avec eux sans hésiter; car c'est moi qui les ai envoyés.
21 Petro anatsika ndipo anati kwa anthuwo, “Amene mukufunayo ndine. Mwabwera kuno chifukwa chiyani?”
Alors Pierre, étant descendu vers ces hommes, leur dit: Me voici; je suis celui que vous cherchez; pour quel motif êtes-vous venus?
22 Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.”
Ils répondirent: Corneille, centenier, homme juste et craignant Dieu, auquel la nation juive rend un bon témoignage, a reçu d'un saint ange l'ordre de te faire venir dans sa maison et d'écouter tes paroles.
23 Pamenepo Petro anawalowetsa mʼnyumba ndipo anawasamala ngati alendo ake. Mmawa mwake Petro ananyamuka napita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye pamodzi.
Alors Pierre les fit entrer et leur donna l'hospitalité. Le lendemain, il se leva et partit avec eux et quelques-uns des frères de Joppé l'accompagnèrent.
24 Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima.
Le jour suivant, ils arrivèrent à Césarée. Corneille les attendait avec ses parents et ses amis intimes, qu'il avait réunis chez lui.
25 Petro akulowa mʼnyumba, Korneliyo anakumana naye ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake namulambira.
Comme Pierre entrait, Corneille alla au-devant de lui, et, se jetant à ses pieds, il l'adora.
26 Koma Petro anamuyimiritsa nati, “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe.”
Mais Pierre le releva, en disant: Lève-toi, je ne suis moi-même qu'un homme!
27 Akuyankhula naye, Petro analowa mʼnyumba ndipo anapeza gulu lalikulu la anthu litasonkhana.
Et tout en s'entretenant avec lui, il entra et trouva plusieurs personnes réunies.
28 Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa.
Vous savez, leur dit-il, qu'il est interdit à un Juif d'entrer en relation avec un étranger, ou d'aller chez lui; mais Dieu m'a fait voir que je ne devais appeler aucun homme souillé ou impur.
29 Nʼchifukwa chake ndabwera mosawiringula pamene munandiyitana. Tsopano ndikufunseni,” Mwandiyitanira chiyani?
Aussi n'ai-je fait aucune difficulté pour venir, lorsque vous m'avez envoyé chercher. Je demande donc pour quel motif vous m'avez fait venir.
30 Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira.
Corneille lui répondit: Il y a maintenant quatre jours, à la neuvième heure, j'étais chez-moi en prière, quand tout à coup un homme, portant un vêtement resplendissant, se présenta devant moi,
31 Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka.
et il me dit: Corneille, ta prière a été exaucée, et Dieu s'est souvenu de tes aumônes.
32 Tuma anthu ku Yopa akayitane Simoni wotchedwa Petro. Iye akukhala mʼnyumba ya Simoni mmisiri wazikopa amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’
Envoie donc à Joppé, et fais venir Simon, surnommé Pierre: il est logé chez Simon, le corroyeur, près de la mer.
33 Nʼchifukwa chake ndinatumiza anthu nthawi yomweyo ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano ife tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akukulamulani kuti mutiwuze ife.”
J'ai sur-le-champ envoyé vers toi, et tu as bien fait de venir. Maintenant donc, nous voici tous en présence de Dieu, pour entendre tout ce que le Seigneur t'a commandé de nous dire.
34 Ndipo Petro anayamba kuyankhula nati, “Zoonadi, tsopano ndazindikira kuti Mulungu sakondera.
Alors Pierre ouvrit la bouche et dit: En vérité, je reconnais que Dieu ne fait pas acception de personnes,
35 Koma amalandira anthu a mtundu uli wonse amene amaopa Iye ndiponso kuchita chilungamo.
mais qu'en toute nation, celui qui le craint et qui pratique la justice lui est agréable.
36 Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse.
C'est la parole qu'il a adressée aux enfants d'Israël, en leur faisant annoncer la bonne nouvelle de la paix par Jésus-Christ, qui est le Seigneur de tous.
37 Inu mukudziwa zimene zinachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikira,
Vous savez les faits qui se sont passés dans toute la Judée, et qui avaient commencé à se produire en Galilée, à la suite du baptême prêché par Jean:
38 kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.
comment Dieu a oint d'Esprit saint et de puissance Jésus de Nazareth, qui allait de lieu en lieu, faisant du bien et guérissant tous ceux qui étaient sous l'empire du Diable; car Dieu était avec lui.
39 “Ife ndife mboni za zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndiponso ku Yerusalemu. Anamupha Iye pakumupachika pa mtengo,
Nous avons été témoins de tout ce qu'il a fait dans le pays des Juifs et à Jérusalem. Ils l'ont fait mourir, en le pendant au bois.
40 koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa pa tsiku lachitatu, ndipo analola kuti aonekere poyera.
Mais Dieu l'a ressuscité le troisième jour, et il a permis qu'il se montrât,
41 Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa.
non à tout le peuple, mais aux témoins choisis d'avance par Dieu, à nous qui avons mangé et bu avec lui après sa résurrection d'entre les morts.
42 Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa.
Et il nous a commandé de prêcher au peuple, et d'attester que c'est lui qui a été établi par Dieu pour juger les vivants et les morts.
43 Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.”
Tous les prophètes rendent de lui ce témoignage, que quiconque croit en lui reçoit par son nom la rémission des péchés.
44 Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo.
Comme Pierre parlait encore, le Saint-Esprit descendit sur tous ceux qui écoutaient la Parole.
45 Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina.
Et les fidèles circoncis, qui étaient venus avec Pierre, étaient fort étonnés de voir que le don du Saint-Esprit était aussi accordé aux Païens.
46 Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati,
Car ils les entendaient parler en langues étrangères et glorifier Dieu.
47 “Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.”
Alors Pierre reprit la parole et dit: Peut-on refuser l'eau du baptême à ceux qui ont reçu le Saint-Esprit aussi bien que nous?
48 Tsono iye analamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu. Ndipo anthu aja anamupempha Petro kuti akhale nawo masiku angapo.
Et il ordonna de les baptiser au nom de Jésus-Christ. Ils le prièrent alors de demeurer quelques jours avec eux.