< 2 Timoteyo 3 >
1 Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri.
2 Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero.
3 Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino,
4 opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu.
5 Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.
6 Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu,
7 amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi.
8 Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa.
9 Koma sadzapita nazo patali kwambiri zimenezi, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwawo monga anachitira Yanesi ndi Yambere.
10 Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga,
11 mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi.
12 Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,
13 pomwe anthu oyipa ndi onyenga adzanka nayipirayipira, kunamiza ena, iwo nʼkumanamizidwanso.
14 Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi.
15 Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.
16 Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo
17 kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.