< 2 Atesalonika 2 >
1 Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikumane naye, abale, tikukupemphani
Prosímeť pak vás, bratří, skrze příští Pána našeho Jezukrista a naše shromáždění v něj,
2 kuti musagwedezeke msanga mʼmaganizo kapena kuopsezedwa ndi uneneri, mbiri kapena kalata yokhala ngati yachokera kwa ife, yonena kuti tsiku lija la Ambuye linafika kale.
Abyste se nedali rychle vyrážeti z mysli, ani kormoutiti, buď skrze ducha, buďto skrze řeč, neb skrze list, jako od nás poslaný, jako by nastával den Kristův.
3 Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo.
Nesvodiž vás žádný nižádným obyčejem. Neboť nenastane den Páně, než až prve přijde odstoupení, a zjeven bude ten člověk hřícha, syn zatracení,
4 Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
Protivící a povyšující se nade všecko, což slove Bůh, anebo čemuž se děje Božská čest, takže se posadí v chrámě Božím, tak sobě počínaje, jako by byl Bůh.
5 Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu pamodzi ndinkakuwuzani zimenezi?
Nepomníte-liž, že ještě byv u vás, o tom jsem vám pravil?
6 Ndipo tsopano mukudziwa chimene chikumuletsa kuonekera, koma adzawululika pa nthawi yake yoyenera.
A nyní co mešká, víte, totiž aby on teprv zjeven byl časem svým.
7 Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe.
Nebo již tajemství nepravosti působí, toliko až by ten, jenž jej zdržuje nyní, z prostředku byl vyvržen.
8 Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake.
A tehdážť zjeven bude ten bezbožník, kteréhož Pán zabije duchem úst svých a zkazí zjevením jasné přítomnosti své,
9 Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo.
Kteréhožto nešlechetníka příští jest podle mocného díla satanova, se vší mocí a divy i zázraky lživými,
10 Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe.
A se všelikým podvodem nepravosti v těch, jenž hynou, protože lásky pravdy nepřijali, aby spaseni byli.
11 Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza.
A protož pošle jim Bůh mocné dílo podvodů, aby věřili lži,
12 Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa.
A aby odsouzeni byli všickni, kteříž neuvěřili pravdě, ale oblíbili sobě nepravost.
13 Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi.
Myť pak jsme povinni děkovati Bohu vždycky z vás, bratří Pánu milí, že vyvolil vás Bůh od počátku k spasení, v posvěcení Ducha a u víře pravdy,
14 Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu.
K čemuž povolal vás skrze evangelium naše, k dojití slávy Pána našeho Jezukrista.
15 Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata.
A protož, bratří, stůjtež a držtež se učení vydaného, jemuž jste se naučili, buďto skrze řeč, buďto i skrze list náš.
16 Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino, (aiōnios )
On pak Pán náš Ježíš Kristus, a Bůh i Otec náš, kterýž zamiloval nás a dal nám potěšení věčné a naději dobrou z milosti, (aiōnios )
17 akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse.
Potěšujž srdcí vašich a utvrdiž vás v každém slovu i skutku dobrém.