< 2 Samueli 1 >
1 Atamwalira Sauli, Davide anabwerako kumene anakagonjetsa Aamaleki ndipo anakakhala ku Zikilagi masiku awiri.
掃羅死後,大衛擊殺亞瑪力人回來,在洗革拉住了兩天。
2 Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo.
第三天,有一人從掃羅的營裏出來,衣服撕裂,頭蒙灰塵,到大衛面前伏地叩拜。
3 Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.”
大衛問他說:「你從哪裏來?」他說:「我從以色列的營裏逃來。」
4 Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?” Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.”
大衛又問他說:「事情怎樣?請你告訴我。」他回答說:「百姓從陣上逃跑,也有許多人仆倒死亡;掃羅和他兒子約拿單也死了。」
5 Ndipo Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa nkhaniyi, “Ukudziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?”
大衛問報信的少年人說:「你怎麼知道掃羅和他兒子約拿單死了呢?」
6 Mnyamatayo anati, “Zinangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa, ndipo Sauli anali komweko ataweramira pa mkondo wake, pamodzi ndi magaleta ndi okwera ake atamuyandikira.
報信的少年人說:「我偶然到基利波山,看見掃羅伏在自己槍上,有戰車、馬兵緊緊地追他。
7 Pamene anatembenuka ndi kundiona ine, iye anandiyitana, ndipo ndinati, ‘Kodi ndichite chiyani?’”
他回頭看見我,就呼叫我。我說:『我在這裏。』
8 Iye anandifunsa, “Iwe ndiwe yani?” Ine ndinayankha kuti, “Ndine Mwamaleki.”
他問我說:『你是甚麼人?』我說:『我是亞瑪力人。』
9 “Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’
他說:『請你來,將我殺死;因為痛苦抓住我,我的生命尚存。』
10 “Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.”
我準知他仆倒必不能活,就去將他殺死,把他頭上的冠冕、臂上的鐲子拿到我主這裏。」
11 Apo Davide ndi anthu onse amene anali nawo anangʼamba zovala zawo.
大衛就撕裂衣服,跟隨他的人也是如此,
12 Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga.
而且悲哀哭號,禁食到晚上,是因掃羅和他兒子約拿單,並耶和華的民以色列家的人,倒在刀下。
13 Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa uthengawo, “Iwe umachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine mwana wa mlendo Mwamaleki.”
大衛問報信的少年人說:「你是哪裏的人?」他說:「我是亞瑪力客人的兒子。」
14 Davide anamufunsanso kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunaope kukweza dzanja lako ndi kupha wodzozedwa wa Yehova?”
大衛說:「你伸手殺害耶和華的受膏者,怎麼不畏懼呢?」
15 Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa.
大衛叫了一個少年人來,說:「你去殺他吧!」
16 Pakuti Davide anali atanena kwa iye kuti, “Iwe wadzipha wekha. Pakamwa pako pakunena zokutsutsa wekha, pamene unanena kuti, ‘Ine ndapha wodzozedwa wa Yehova.’”
大衛對他說:「你流人血的罪歸到自己的頭上,因為你親口作見證說:『我殺了耶和華的受膏者。』」少年人就把他殺了。
17 Davide anayimba nyimbo iyi ya maliro, kulira Sauli ndi mwana wake Yonatani.
大衛作哀歌,弔掃羅和他兒子約拿單,
18 Ndipo analamula kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimbo ya maliroyi imene yalembedwa mʼbuku la Yasari:
且吩咐將這歌教導猶大人。這歌名叫「弓歌」,寫在雅煞珥書上。
19 “Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda. Taonani amphamvu agwa kumeneko!
歌中說:以色列啊, 你尊榮者在山上被殺! 大英雄何竟死亡!
20 “Musakanene zimenezi ku Gati, musazilengeze ku misewu ya ku Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasangalale, ana aakazi a osachita mdulidwe angakondwere.
不要在迦特報告; 不要在亞實基倫街上傳揚; 免得非利士的女子歡樂; 免得未受割禮之人的女子矜誇。
21 “Inu mapiri a ku Gilibowa, musakhalenso ndi mame kapena mvula, kapena minda yobereka zopereka za ufa. Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa, chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta.
基利波山哪,願你那裏沒有雨露! 願你田地無土產可作供物! 因為英雄的盾牌在那裏被污丟棄; 掃羅的盾牌彷彿未曾抹油。
22 “Pa magazi a ophedwa, pa mnofu wa amphamvu, uta wa Yonatani sunabwerere, lupanga la Sauli silinabwere chabe.
約拿單的弓箭非流敵人的血不退縮; 掃羅的刀劍非剖勇士的油不收回。
23 “Sauli ndi Yonatani, pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima, ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe. Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga, anali ndi mphamvu zoposa mkango.
掃羅和約拿單- 活時相悅相愛,死時也不分離 -他們比鷹更快,比獅子還強。
24 “Inu ana aakazi a Israeli, mulireni Sauli, amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa, amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide.
以色列的女子啊,當為掃羅哭號! 他曾使你們穿朱紅色的美衣, 使你們衣服有黃金的妝飾。
25 “Taonani amphamvu agwa ku nkhondo! Yonatani wagona ataphedwa ku zitunda.
英雄何竟在陣上仆倒! 約拿單何竟在山上被殺!
26 Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani, unali wokondedwa kwambiri kwa ine. Chikondi chako pa ine chinali chopambana, chopambana kuposa chikondi cha akazi.
我兄約拿單哪,我為你悲傷! 我甚喜悅你! 你向我發的愛情奇妙非常, 過於婦女的愛情。
27 “Taonani amphamvu agwa! Zida zankhondo zawonongeka!”
英雄何竟仆倒! 戰具何竟滅沒!