< 2 Samueli 9 >

1 Davide anafunsa kuti, “Kodi alipo amene watsala mʼbanja la Sauli kuti ndimuchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?”
大卫问说:“扫罗家还有剩下的人没有?我要因约拿单的缘故向他施恩。”
2 Tsono panali mtumiki wina wa banja la Sauli wotchedwa Ziba. Iwo anamuyitana kuti aonekere pamaso pa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Ziba?” Iyeyo anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
扫罗家有一个仆人,名叫洗巴,有人叫他来见大卫,王问他说:“你是洗巴吗?”回答说:“仆人是。”
3 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?” Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”
王说:“扫罗家还有人没有?我要照 神的慈爱恩待他。”洗巴对王说:“还有约拿单的一个儿子,是瘸腿的。”
4 Mfumu inafunsa kuti, “Ali kuti?” Ziba anayankha kuti, “Iye ali ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli ku Lodebara.”
王说:“他在哪里?”洗巴对王说:“他在罗·底巴,亚米利的儿子玛吉家里。”
5 Kotero mfumu inamubweretsa kuchokera ku Lodebara, ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli.
于是大卫王打发人去,从罗·底巴、亚米利的儿子玛吉家里召了他来。
6 Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
扫罗的孙子、约拿单的儿子米非波设来见大卫,伏地叩拜。大卫说:“米非波设!”米非波设说:“仆人在此。”
7 Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”
大卫说:“你不要惧怕,我必因你父亲约拿单的缘故施恩与你,将你祖父扫罗的一切田地都归还你;你也可以常与我同席吃饭。”
8 Mefiboseti anawerama pansi ndipo anati, “Mtumiki wanu ndine yani kuti musamale galu wakufa ngati ine?”
米非波设又叩拜,说:“仆人算什么,不过如死狗一般,竟蒙王这样眷顾!”
9 Kenaka Davide anayitanitsa Ziba, mtumiki wa Sauli, ndipo anati, “Ine ndapereka kwa chidzukulu cha mbuye wako chilichonse chimene chinali cha Sauli ndi banja lake.
王召了扫罗的仆人洗巴来,对他说:“我已将属扫罗和他的一切家产都赐给你主人的儿子了。
10 Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri).
你和你的众子、仆人要为你主人的儿子米非波设耕种田地,把所产的拿来供他食用;他却要常与我同席吃饭。”洗巴有十五个儿子,二十个仆人。
11 Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu.
洗巴对王说:“凡我主我王吩咐仆人的,仆人都必遵行。”王又说:“米非波设必与我同席吃饭,如王的儿子一样。”
12 Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna wotchedwa Mika, ndipo onse a banja la Ziba anali antchito a Mefiboseti.
米非波设有一个小儿子,名叫米迦。凡住在洗巴家里的人都作了米非波设的仆人。
13 Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse.
于是米非波设住在耶路撒冷,常与王同席吃饭。他两腿都是瘸的。

< 2 Samueli 9 >