< 2 Samueli 6 >
1 Davide anasonkhanitsanso pamodzi ankhondo 3,000 osankhidwa pakati pa Aisraeli.
2 Iye pamodzi ndi ankhondo ake onse anapita ku Baalahi ku Yuda kukatenga Bokosi la Chipangano la Mulungu, limene limadziwika ndi Dzina lake, dzina la Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pakati pa Akerubi amene ali pa Bokosi la Chipanganolo.
3 Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo,
4 imene inanyamula Bokosi la Mulungu, ndipo Ahiyo mwana wa Abinadabu ankayenda patsogolo pake.
5 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.
6 Atafika pa malo opunthira tirigu a Nakoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire Bokosi la Mulungu, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa.
7 Yehova anapsera mtima Uza chifukwa chochita chinthu chosayenera kuchitika. Choncho Mulungu anamukantha ndipo anafera pomwepo pambali pa Bokosi la Mulungulo.
8 Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.
9 Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Yehova ndipo anati, “Kodi Bokosi la Yehova lingafike bwanji kwathu?”
10 Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.
11 Bokosi la Yehova linakhala mʼnyumba ya Obedi-Edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri iyeyo ndi banja lake lonse.
12 Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri.
13 Anthu amene ananyamula Bokosi la Yehova ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye ankapereka nsembe ngʼombe yayimuna ndi mwana wangʼombe wonenepa.
14 Davide ankavina ndi mphamvu zake zonse pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala,
15 pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga.
16 Bokosi la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikulumpha ndi kuvina pamaso pa Yehova, ankamunyogodola mu mtima mwake.
17 Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova.
18 Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse.
19 Kenaka iye anagawira Aisraeli onsewo, aamuna ndi aakazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama, ndiponso keke yamphesa zowuma. Ndipo anthu onse anachokapo, napita aliyense ku nyumba kwake.
20 Davide atabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kudzakumana naye ndipo anati, “Kodi mfumu ya Israeli ingatero kudzilemekeza kwake lero, kudzithyolathyola pamaso pa akapolo aakazi, antchito ake ngati munthu wamba.”
21 Davide anamuyankha Mikala kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Yehova, amene anandisankha ine kupambana abambo ako, kapenanso kupambana banja la abambo ako. Ndipo anandisankha kuti ndikhale wolamulira Aisraeli, anthu a Yehova. Nʼchifukwa chake ndidzasangalalabe pamaso pa Yehova.
22 Ineyo ndidzadzinyoza kuposa apa, ndipo ndidzakhala wonyozeka mʼmaso mwako. Koma pakati pa akapolo aakazi awa amene umanena za iwo, ndidzalemekezedwa.”
23 Ndipo Mikala mwana wa Sauli sanakhalenso ndi mwana mpaka anamwalira.