< 2 Samueli 4 >
1 Isiboseti mwana wa Sauli atamva kuti Abineri waphedwa ku Hebroni, anataya mtima ndipo Aisraeli onse anachita mantha kwambiri.
2 Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini,
3 chifukwa anthu a ku Beeroti anathawira ku Gitaimu ndipo akhala ali kumeneko ngati alendo mpaka lero lino.
4 (Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti).
5 Choncho Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti ananyamuka kupita ku nyumba ya Isi-Boseti, ndipo anafika nthawi ya masana kukutentha pamene iye amapumula.
6 Iwo analowa mʼchipinda chamʼkati ngati kuti amakatenga tirigu, ndipo anamulasa mʼmimba. Kenaka Rekabu ndi mʼbale wake Baana anathawa.
7 Iwo analowa mʼnyumbamo iye akugona pa bedi mʼchipinda chake. Atamulasa ndi kumupha, anadula mutu wake nʼkuwutenga, nayenda usiku wonse mʼnjira yopita ku Araba.
8 Iwo anabweretsa mutu wa Isi-Boseti kwa Davide ku Hebroni ndipo anati kwa mfumu, “Nawu mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu, amene anafuna kukuphani. Lero lino Yehova wabwezera mbuye wanga mfumu adani anu, Sauli ndi ana ake.”
9 Davide anayankha Rekabu ndi mʼbale wake Baana, ana a Rimoni wa ku Beeroti kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene wandipulumutsa ku mavuto anga onse,
10 pamene munthu wina anandiwuza kuti, ‘Sauli wafa’ ndipo ankaganiza kuti wabweretsa nkhani yabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha ku Zikilagi. Iyi inali mphotho imene ndinapereka kwa iyeyo chifukwa cha uthenga wake!
11 Nanji pamene anthu oyipa apha munthu wosalakwa ali mʼnyumba mwake ndiponso pa bedi lake! Kodi ine ndingaleke kukulangani ndi kukuchotsani pa dziko lapansi pano?”
12 Kotero Davide analamulira ankhondo ake, ndipo anawapha. Iwo anawadula manja ndi mapazi ndi kupachika matupi awo pa dziwe la ku Hebroni. Koma anatenga mutu wa Isi-Boseti nawuyika mʼmanda a Abineri ku Hebroni.