< 2 Samueli 3 >
1 Nkhondo ya pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide inachitika nthawi yayitali. Mphamvu za Davide zinkakulirakulirabe, pamene banja la Sauli mphamvu zake zimapita zicheperachepera.
2 Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli.
3 Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli. Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;
4 wachinayi anali Adoniya, amayi ake anali Hagiti; wachisanu, Sefatiya amayi ake anali Abitali;
5 ndipo wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila, mkazi wa Davide. Ana awa a Davide anabadwira ku Hebroni.
6 Pamene kunali nkhondo pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide, Abineri anayamba kudzipatsa yekha mphamvu pakati pa banja la Sauli.
7 Sauli anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa mwana wa Ayiwa. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mzikazi wa abambo anga?”
8 Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu!
9 Mulungu andilange ine Abineri, andilange kwambiri, ngati sindichitira Davide zimene Yehova anamulonjeza iye mwa lumbiro.
10 Ndidzachotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazikitsa ufumu wa Davide pa Aisraeli onse ndi Yuda kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba.”
11 Isiboseti sanayerekezenso kunena mawu ena kwa Abineri, chifukwa ankamuopa.
12 Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.”
13 Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.”
14 Ndipo Davide anatuma amithenga kwa Isi-Boseti mwana wa Sauli, kumulamula kuti, “Patse mkazi wanga Mikala, amene ndinamukwatira ndi makungu 100 a msonga za mavalo a Afilisti.”
15 Kotero Isi-Boseti analamulira ndipo anakamutenga kwa mwamuna wake Palitieli mwana wa Laisi.
16 Koma mwamuna wake anapita naye akulira pambuyo pake njira yonse mpaka ku Bahurimu. Kenaka Abineri anati kwa iye, “Bwerera kwanu!” Ndipo anabwerera kwawo.
17 Abineri anakambirana ndi akuluakulu a Israeli ndipo anati, “Kwa kanthawi mwakhala mukufuna kulonga Davide kuti akhale mfumu yanu.
18 Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’”
19 Abineri anayankhulanso nawo yekha anthu a fuko la Benjamini. Kenaka anapita ku Hebroni kukamuwuza Davide zonse zimene Aisraeli ndi fuko lonse la Benjamini amafuna kuchita.
20 Abineri, amene anali ndi anthu makumi awiri, atafika kwa Davide ku Hebroni, Davide anamukonzera phwando pamodzi ndi anthu ake.
21 Ndipo Abineri anawuza Davide kuti, “Loleni kuti ndipite msanga kukasonkhanitsa Aisraeli onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuye wanga mfumu, kuti adzachite nanu pangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Kotero Davide analola Abineri kuti apite, ndipo anapita mwamtendere.
22 Nthawi yomweyo ankhondo a Davide ndi Yowabu anafika kuchokera kumene anakathira nkhondo ndipo anabweretsa katundu wambiri wolanda ku nkhondo. Koma Abineri sanalinso ndi Davide ku Hebroni, chifukwa Davide anamulola kuti apite, ndipo anapita mu mtendere.
23 Yowabu ndi asilikali onse amene anali naye atafika, anawuzidwa kuti Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu ndipo kuti mfumu yamulola kuti apite ndi kuti wapita ndi mtendere.
24 Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Mwachita chiyani? Taonani, Abineri anabwera kwa inu. Nʼchifukwa chiyani mwamulola kuti apite? Tsopanotu wapitadi!
25 Inu mukumudziwa bwino Abineri mwana wa Neri. Iye anabwera kudzakunamizani ndi kudzaona mayendedwe anu ndiponso kudzaona zonse zimene mukuchita.”
26 Kenaka Yowabu anachoka pamaso pa Davide ndipo anatumiza amithenga kutsatira Abineri, ndipo anabwera naye kuchokera ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanadziwe zimenezi.
27 Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa.
28 Patapita nthawi, Davide atamva zimenezi anati, “Ine ndi ufumu wanga tidzakhala osalakwa pamaso pa Yehova pa imfa ya Abineri mwana wa Neri.
29 Mlandu umenewu ukhala pa Yowabu ndi banja lonse la abambo ake! Mʼbanja la Yowabu musadzasowe munthu wodwala matenda a chizonono kapena khate, kapena wolumala woyendera ndodo kapena wophedwa ndi lupanga, kapena wosowa chakudya.”
30 (Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anapha Abineri chifukwa iye anapha mʼbale wawo Asaheli ku nkhondo ku Gibiyoni).
31 Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi anthu onse amene anali nawo, “Ngʼambani zovala zanu ndipo muvale ziguduli, muyende mukulira patsogolo pa Abineri.” Mfumu Davide mwini anayenda motsatira chitandacho.
32 Iwo anamuyika Abineri mʼmanda ku Hebroni ndipo mfumu inalira mokweza pa manda a Abineri. Ndipo anthu onse analiranso.
33 Mfumu inayimba nyimbo iyi ya maliro a Abineri: “Abineri nʼkufa motere monga mmene chimafera chitsiru.
34 Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulungidwa. Iwe wafa monga mmene amafera anthu pamaso pa anthu oyipa.” Ndipo anthu onse analiranso kulirira Abineri.
35 Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!”
36 Anthu onse anadziwa zimenezi ndipo zinawakondweretsa ndithu. Zonse zimene mfumu inachita zinawakondweretsa.
37 Kotero tsiku limeneli anthu onse ndi Aisraeli onse anadziwa kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abineri mwana wa Neri aphedwe.
38 Ndipo mfumu inati kwa ankhondo ake, “Kodi inu simukudziwa kuti lero mu Israeli mwagwa kalonga ndi munthu wamkulu?
39 Ndipo lero, ngakhale ine ndine mfumu yodzozedwa, ndilibe mphamvu ndipo ana awa a Zeruya ndi amphamvu kwa ine. Yehova abwezere woyipa molingana ndi zoyipa zake!”