< 2 Samueli 24 >

1 Nthawi inanso Yehova anawakwiyira Aisraeli ndipo anawutsa mtima wa Davide kuti awavutitse ndipo anati, “Pita kawerenge Aisraeli ndi Ayuda.”
ויסף אף יהוה לחרות בישראל ויסת את דוד בהם לאמר לך מנה את ישראל ואת יהודה׃
2 Choncho mfumu inati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali nawo. “Pitani pakati pa mafuko onse a Israeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba kuti mukawerenge anthu omenya nkhondo ndi cholinga choti ndidziwe chiwerengero chawo.”
ויאמר המלך אל יואב שר החיל אשר אתו שוט נא בכל שבטי ישראל מדן ועד באר שבע ופקדו את העם וידעתי את מספר העם׃
3 Koma Yowabu anayankha mfumu kuti, “Yehova Mulungu wanu achulukitse ankhondo anu kukhala miyandamiyanda, ndipo alole inu mbuye wanga mfumu mudzazione zimenezi. Koma nʼchifukwa chiyani inu mbuye wanga mfumu mukufuna kuchita zimenezi?”
ויאמר יואב אל המלך ויוסף יהוה אלהיך אל העם כהם וכהם מאה פעמים ועיני אדני המלך ראות ואדני המלך למה חפץ בדבר הזה׃
4 Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu ndi atsogoleri a ankhondo. Choncho anachoka pamaso pa mfumu kupita kukawerenga anthu omenya nkhondo mu Israeli.
ויחזק דבר המלך אל יואב ועל שרי החיל ויצא יואב ושרי החיל לפני המלך לפקד את העם את ישראל׃
5 Atawoloka Yorodani, iwo anamanga misasa yawo pafupi ndi Aroeri kummwera kwa mzinda wa ku chigwa ndipo kenaka iwo anapita ku dziko la Gadi mpaka ku Yazeri.
ויעברו את הירדן ויחנו בערוער ימין העיר אשר בתוך הנחל הגד ואל יעזר׃
6 Iwo anapita ku Giliyadi ndi ku chigwa cha Tahitimu Hodisi ndipo anapitirira mpaka ku Dani Yaani ndi madera ozungulira Sidoni.
ויבאו הגלעדה ואל ארץ תחתים חדשי ויבאו דנה יען וסביב אל צידון׃
7 Kenaka iwo anapita molunjika linga la ku Turo ndi ku mizinda yonse ya Ahivi ndi Akanaani. Pomaliza anapita ku Beeriseba ku Negevi wa ku Yuda.
ויבאו מבצר צר וכל ערי החוי והכנעני ויצאו אל נגב יהודה באר שבע׃
8 Atayendayenda mʼdziko lonse anabwerera ku Yerusalemu patapita miyezi isanu ndi inayi ndi masiku makumi awiri.
וישטו בכל הארץ ויבאו מקצה תשעה חדשים ועשרים יום ירושלם׃
9 Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa mfumu: Mu Israeli munali anthu 800,000 amphamvu amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga ndipo mu Yuda munali anthu 500,000.
ויתן יואב את מספר מפקד העם אל המלך ותהי ישראל שמנה מאות אלף איש חיל שלף חרב ואיש יהודה חמש מאות אלף איש׃
10 Davide anatsutsika mu mtima mwake atatha kuwerenga anthuwo ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono Yehova, ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”
ויך לב דוד אתו אחרי כן ספר את העם ויאמר דוד אל יהוה חטאתי מאד אשר עשיתי ועתה יהוה העבר נא את עון עבדך כי נסכלתי מאד׃
11 Davide asanadzuke mmawa mwake mawu a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlosi wa Davide kuti,
ויקם דוד בבקר ודבר יהוה היה אל גד הנביא חזה דוד לאמר׃
12 “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’”
הלוך ודברת אל דוד כה אמר יהוה שלש אנכי נוטל עליך בחר לך אחת מהם ואעשה לך׃
13 Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa iye, “Kodi mungakonde kuti mʼdziko mwanu mukhale njala kwa zaka zitatu? Kapena kuti mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu? Kapena kuti mʼdziko muno mukhale mliri kwa masiku atatu? Tsopano, ganizirani bwino ndipo musankhe chomwe mudzamuyankhe amene wandituma.”
ויבא גד אל דוד ויגד לו ויאמר לו התבוא לך שבע שנים רעב בארצך אם שלשה חדשים נסך לפני צריך והוא רדפך ואם היות שלשת ימים דבר בארצך עתה דע וראה מה אשיב שלחי דבר׃
14 Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ife atilange ndi Yehova pakuti chifundo chake ndi chachikulu, koma ndisalangidwe ndi anthu.”
ויאמר דוד אל גד צר לי מאד נפלה נא ביד יהוה כי רבים רחמו וביד אדם אל אפלה׃
15 Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba.
ויתן יהוה דבר בישראל מהבקר ועד עת מועד וימת מן העם מדן ועד באר שבע שבעים אלף איש׃
16 Pamene mngelo anatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
וישלח ידו המלאך ירושלם לשחתה וינחם יהוה אל הרעה ויאמר למלאך המשחית בעם רב עתה הרף ידך ומלאך יהוה היה עם גרן האורנה היבסי׃
17 Davide ataona mngelo amene ankakantha anthu uja, anati kwa Yehova, “Ine ndi amene ndachimwa. Ine mʼbusa ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Langani ineyo pamodzi ndi banja langa.”
ויאמר דוד אל יהוה בראתו את המלאך המכה בעם ויאמר הנה אנכי חטאתי ואנכי העויתי ואלה הצאן מה עשו תהי נא ידך בי ובבית אבי׃
18 Tsiku limenelo Gadi anapita kwa Davide ndi kukanena kuti, “Pitani kamangeni guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.”
ויבא גד אל דוד ביום ההוא ויאמר לו עלה הקם ליהוה מזבח בגרן ארניה היבסי׃
19 Ndipo Davide anapita monga momwe Yehova anamulamulira kudzera mwa Gadi.
ויעל דוד כדבר גד כאשר צוה יהוה׃
20 Arauna atayangʼana ndi kuona mfumu ndi anthu ake akubwera kumene kunali iye, iyeyo anatuluka ndi kuwerama pamaso pa mfumu mpaka nkhope yake kugunda pansi.
וישקף ארונה וירא את המלך ואת עבדיו עברים עליו ויצא ארונה וישתחו למלך אפיו ארצה׃
21 Arauna anati, “Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mfumu mwabwera kwa mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti, “Kudzagula malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe kuti mliri uli pa anthuwa usiye.”
ויאמר ארונה מדוע בא אדני המלך אל עבדו ויאמר דוד לקנות מעמך את הגרן לבנות מזבח ליהוה ותעצר המגפה מעל העם׃
22 Arauna anati kwa Davide, “Mbuye wanga mfumu mutenge chilichonse chimene chikukondweretseni ndi kuchipereka nsembe. Nazi ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, nazi zopunthira tirigu ndi magoli angʼombe kuti zikhale nkhuni.
ויאמר ארונה אל דוד יקח ויעל אדני המלך הטוב בעינו ראה הבקר לעלה והמרגים וכלי הבקר לעצים׃
23 Inu mfumu, Arauna akupereka zonsezi kwa inu mfumu.” Arauna anatinso kwa iye, “Yehova Mulungu wanu akuvomerezeni.”
הכל נתן ארונה המלך למלך ויאמר ארונה אל המלך יהוה אלהיך ירצך׃
24 Koma mfumu inayankha Arauna kuti, “Ayi, Ine ndikunenetsa kuti ndikulipira. Sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe yopsereza imene sindinavutikire.” Kotero Davide anagula malo wopunthira tiriguwo ndi ngʼombe ndipo anapereka kwa Araunayo masekeli asiliva makumi asanu.
ויאמר המלך אל ארונה לא כי קנו אקנה מאותך במחיר ולא אעלה ליהוה אלהי עלות חנם ויקן דוד את הגרן ואת הבקר בכסף שקלים חמשים׃
25 Davide anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Ndipo Yehova anayankha pempherolo mʼmalo mwa dziko lonse, ndipo mliri unatha pa Aisraeli.
ויבן שם דוד מזבח ליהוה ויעל עלות ושלמים ויעתר יהוה לארץ ותעצר המגפה מעל ישראל׃

< 2 Samueli 24 >