< 2 Samueli 23 >
1 Nawa mawu otsiriza a Davide: “Mawu a Davide mwana wa Yese, mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba, munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo, woyimba nyimbo za Israeli:
2 “Mzimu wa Yehova unayankhula kudzera mwa ine; mawu ake anali pakamwa panga.
3 Mulungu wa Israeli anayankhula, Thanthwe la Israeli linati kwa ine: ‘Pamene munthu alamulira anthu mwachilungamo, pamene alamulira moopa Mulungu,
4 amakhala ngati kuwala kwa mmamawa, mmawa wopanda mitambo, monga kuwala pamene mvula yaleka kugwa imene imameretsa udzu mʼnthaka.’
5 “Kodi banja langa silolungama pamaso pa Mulungu? Kodi Iye sanachite pangano losatha ndi ine, lokonzedwa ndi lotetezedwa mbali zonse? Kodi sadzakwaniritsa chipulumutso changa, ndi kundipatsa chokhumba changa chilichonse?
6 Koma anthu oyipa ndiwo ayenera kutayidwa kunja ngati minga, imene sitengedwa ndi manja.
7 Aliyense amene wayikhudza mingayo amayidula pogwiritsa ntchito chigwandali kapena ndodo ya mkondo; nayitentha pa moto.”
8 Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti wa ku Takemoni mkulu wa atsogoleri a ankhondo atatu. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 800 nthawi imodzi.
9 Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi. Monga mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu a Davide, iye anali ndi Davide pamene anazunza Afilisti amene anasonkhana ku Pasi-Damimu kuchita nkhondo. Kenaka ankhondo a Israeli anabwerera mʼmbuyo.
10 Koma iye anayima osasuntha ndipo anakantha Afilisti mpaka mkono wake unatopa ndipo unakanirira ku lupanga lake. Yehova anapereka chigonjetso chachikulu pa tsiku limenelo. Asilikali anabwerera kwa Eliezara, kukatenga katundu wa anthu ophedwa.
11 Wotsatana naye anali Sama mwana wa Age Mharari. Pamene Afilisti anasonkhana pamalo pamene panali munda wa mphodza, ankhondo a Israeli anathawa Afilistiwo.
12 Koma Sama anayima pakati pa mundawo. Iye anawuteteza nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.
13 Pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri makumi atatu anabwera kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu.
14 Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu.
15 Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!”
16 Choncho anthu amphamvu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova.
17 Iye anati, “Inu Yehova, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi awa si magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Ndipo Davide sanamwe madziwo. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.
18 Abisai mʼbale wa Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300, choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja.
19 Kodi iyeyo sanali wolemekezeka koposa? Iye anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti sanali mʼgulu la anthu atatu aja.
20 Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.
21 Ndipo iye anakanthanso Mwigupto wamkulu msinkhu. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.
22 Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja.
23 Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu aja, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.
24 Mʼgulu la anthu makumi atatu aja munalinso awa: Asaheli mʼbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
25 Sama Mharodi, Elika Mherodi,
26 Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,
27 Abiezeri wa ku Anatoti, Sibekai Mhusati,
28 Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa,
29 Heledi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini,
30 Benaya Mpiratoni, Hidayi wa ku zigwa za Gaasi.
31 Abi-Aliboni Mwaribati, Azimaveti Mbarihumi,
32 Eliyahiba Msaaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,
33 mwana wa Sama Mharari, Ahiamu mwana wa Sarari Mharari,
34 Elifeleti mwana wa Ahasibai Mmaakati, Eliamu mwana wa Ahitofele Mgiloni,
35 Heziro wa ku Karimeli, Paarai Mwaribi,
36 Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, mwana wa Hagiri,
37 Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,
38 Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,
39 ndi Uriya Mhiti. Onse pamodzi analipo 37.