< 2 Samueli 22 >
1 Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
2 Iye anati, “Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.
3 Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
4 “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
5 “Mafunde a imfa anandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
6 Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane. (Sheol )
7 “Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinapemphera kwa Mulungu wanga. Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.
8 “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
9 Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
10 Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
11 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
12 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, mitambo yakuda ya mlengalenga.
13 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera makala amoto alawilawi.
14 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
15 Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
16 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera, ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.
17 “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama.
18 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.
19 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa.
20 Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
21 “Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
22 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga.
23 Malamulo ake onse ali pamaso panga, sindinasiye malangizo ake.
24 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
25 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa, molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake.
26 “Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu, kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
27 Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu, koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
28 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.
29 Inu Yehova, ndinu nyale yanga; Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
30 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
31 “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.
32 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
33 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga.
34 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
35 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
36 Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso; mumawerama kuti mundikweze.
37 Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino, kuti mapazi anga asaterereke.
38 “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha; sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa.
39 Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso; Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.
40 Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo; munagwaditsa adani anga pa mapazi anga.
41 Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa; ndipo ndinawononga adani anga.
42 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.
43 Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi; ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
44 “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
45 Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine, amandigonjera.
46 Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
47 “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa. Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga!
48 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga,
49 amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
50 Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
51 “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake, amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”