< 2 Samueli 19 >

1 Yowabu anawuzidwa kuti, “Mfumu ikulira maliro a Abisalomu.”
Nunciatum est autem Ioab quod rex fleret et lugeret filium suum:
2 Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake.
et versa est victoria in luctum in die illa omni populo: audivit enim populus in die illa dici: Dolet rex super filio suo.
3 Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo.
Et declinavit populus in die illa ingredi civitatem, quomodo declinare solet populus versus et fugiens de prælio.
4 Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”
Porro rex operuit caput suum, et clamabat voce magna: Fili mi Absalom, Absalom fili mi, fili mi.
5 Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu.
Ingressus ergo Ioab ad regem in domum, dixit: Confudisti hodie vultus omnium servorum tuorum, qui salvam fecerunt animam tuam, et animam filiorum tuorum, et filiarum tuarum, et animam uxorum tuarum, et animam concubinarum tuarum.
6 Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa.
Diligis odientes te, et odio habes diligentes te: et ostendisti hodie quia non curas de ducibus tuis, et de servis tuis: et vere cognovi modo, quia si Absalom viveret, et omnes nos occubuissemus, tunc placeret tibi.
7 Tsopano pitani mukawalimbikitse asilikali anu. Ine ndikulumbira mwa Yehova kuti ngati inu simupita palibe munthu amene adzatsale ali ndi inu polowa dzuwa. Ichi chidzakhala choyipa kwambiri kuposa zovuta zonse zimene zinakugwerani kuyambira muli mnyamata mpaka lero.”
Nunc igitur surge, et procede, et alloquens satisfac servis tuis: iuro enim tibi per Dominum, quod si non exieris, ne unus quidem remansurus sit tecum nocte hac: et peius erit hoc tibi, quam omnia mala, quæ venerunt super te ab adolescentia tua usque in præsens.
8 Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye. Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo.
Surrexit ergo rex et sedit in porta: et omni populo nunciatum est quod rex sederet in porta: venitque universa multitudo coram rege: Israel autem fugit in tabernacula sua.
9 Pakati pa mafuko onse a Israeli, anthu amakangana ndipo amati, “Mfumu inatipulumutsa mʼmanja mwa adani anthu. Iye ndi amene anatilanditsa mʼdzanja la Afilisti. Koma tsopano wathawa mʼdziko muno chifukwa cha Abisalomu.
Omnis quoque populus certabat in cunctis tribubus Israel, dicens: Rex liberavit nos de manu inimicorum nostrorum, ipse salvavit nos de manu Philisthinorum: et nunc fugit de terra propter Absalom.
10 Ndipo Abisalomu amene ife tinamudzoza kuti atilamulire wafa pa nkhondo. Tsono nʼchifukwa chiyani simukunena kanthu za kubweretsanso mfumu?”
Absalom autem, quem unximus super nos, mortuus est in bello: usquequo siletis, et non reducitis regem?
11 Mfumu Davide inatumiza uthenga uwu kwa ansembe Zadoki ndi Abiatara, “Funsani akuluakulu a Yuda, ‘Nʼchifukwa chiyani inu mukukhala otsiriza kuyitana mfumu ku nyumba yake yaufumu, pakuti zimene zikunenedwa mu Israeli yense zamveka kwa mfumu ndi onse amene akukhala nayo.
Rex vero David misit ad Sadoc et Abiathar sacerdotes, dicens: Loquimini ad maiores natu Iuda, dicentes: Cur venitis novissimi ad reducendum regem in domum suam? (Sermo autem omnis Israel pervenerat ad regem in domo eius.)
12 Inu ndinu abale anga enieni, mafupa anga ndi mnofu wanga. Nʼchifukwa chiyani inuyo mukukhala otsiriza kubweretsa mfumu?’
Fratres mei vos, os meum, et caro mea vos, quare novissimi reducitis regem?
13 Ndipo munene kwa Amasa, ‘Kodi iwe si mʼbale wanga weniweni? Mulungu andilange, andilange kwambiri ngati kuyambira tsopano sukhala mtsogoleri wa ankhondo anga kulowa mʼmalo mwa Yowabu.’”
Et Amasæ dicite: Nonne os meum, et caro mea es? Hæc faciat mihi Deus, et hæc addat, si non magister militiæ fueris coram me omni tempore pro Ioab.
14 Davide anakopa mitima ya anthu onse a Yuda ndipo anthuwo anakhala ngati munthu mmodzi. Iwo anatumiza mawu kwa mfumu, “Bwererani inu ndi anthu anu onse.”
Et inclinavit cor omnium virorum Iuda, quasi viri unius: miseruntque ad regem, dicentes: Revertere tu, et omnes servi tui.
15 Kotero mfumu inabwerera ndipo inakafika mpaka ku Yorodani. Tsono anthu a ku Yuda anabwera ku Giligala kuti akakumane ndi mfumu ndi kumuwolotsa Yorodani.
Et reversus est rex: et venit usque ad Iordanem, et omnis Iuda venit usque in Galgalam ut occurreret regi, et traduceret eum Iordanem.
16 Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, anabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide.
Festinavit autem Semei filius Gera filii Iemini de Bahurim, et descendit cum viris Iuda in occursum regis David
17 Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu.
cum mille viris de Beniamin, et Siba puer de domo Saul: et quindecim filii eius, ac viginti servi erant cum eo: et irrumpentes Iordanem, ante regem
18 Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna. Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu,
transierunt vada, ut traducerent domum regis, et facerent iuxta iussionem eius: Semei autem filius Gera prostratus coram rege, cum iam transisset Iordanem,
19 ndipo anati, “Mbuye wanga musaganizire za kulakwa kwanga. Musakumbukire zolakwa zimene mtumiki wanu anakuchitirani tsiku limene mbuye wanga mfumu mumachoka mu Yerusalemu. Mfumu musazikumbukirenso zimenezi.
dixit ad eum: Ne reputes mihi domine mi iniquitatem, neque memineris iniuriarum servi tui in die qua egressus es domine mi rex de Ierusalem, neque ponas rex in corde tuo.
20 Pakuti ine mtumiki wanu ndazindikira kuti ndachimwa. Koma lero ndabwera ngati woyamba wa nyumba ya Yosefe yonse kudzakumana nanu mbuye wanga mfumu.”
Agnosco enim servus tuus peccatum meum: et idcirco hodie primus veni de omni domo Ioseph, descendique in occursum domini mei regis.
21 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati, “Kodi Simei saphedwa chifukwa cha ichi? Iye anatukwana wodzozedwa wa Yehova.”
Respondens vero Abisai filius Sarviæ, dixit: Numquid pro his verbis non occidetur Semei, quia maledixit christo Domini?
22 Davide anayankha kuti, “Kodi inu ana a Zeruya, ndikuchitireni chiyani? Lero lino iwe wakhala mdani wanga! Kodi wina aphedwe lero mu Israeli? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu mu Israeli?”
Et ait David: Quid mihi, et vobis filii Sarviæ? cur efficimini mihi hodie in satan? ergone hodie interficietur vir in Israel? an ignoro hodie me factum regem super Israel?
23 Ndipo mfumu inati kwa Simei, “Iwe Simei suphedwa.” Ndipo mfumuyo inalonjeza ndi lumbiro.
Et ait rex Semei: Non morieris. Iuravitque ei.
24 Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake.
Miphiboseth quoque filius Saul descendit in occursum regis illotis pedibus, et intonsa barba: vestesque suas non laverat a die qua egressus fuerat rex, usque ad diem reversionis eius in pace.
25 Pamene anafika kuchokera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?”
Cumque Ierusalem occurrisset regi, dixit ei rex: Quare non venisti mecum Miphiboseth?
26 Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga mfumu, pakuti ine wantchito wanu ndine wolumala. Ndinati, ‘Andikonzere chishalo cha bulu wanga ndipo ndidzakwera kuti ndipite ndi mfumu.’ Koma Ziba wantchito wanga anandilakwitsa.
Et respondens ait: Domine mi rex, servus meus contempsit me: dixique ei ego famulus tuus ut sterneret mihi asinum, et ascendens abirem cum rege: claudus enim sum servus tuus.
27 Ndipo wayankhula zosinjirira za ine mtumiki wanu kwa inu mbuye wanga mfumu. Mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu ndipo chitani chimene chikukomerani.
Insuper et accusavit me servum tuum ad te dominum meum regem: tu autem domine mi rex, sicut angelus Dei es, fac quod placitum est tibi.
28 Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?”
Neque enim fuit domus patris mei, nisi morti obnoxia domino meo regi: tu autem posuisti me servum tuum inter convivas mensæ tuæ: quid ergo habeo iustæ querelæ? aut quid possum ultra vociferari ad regem?
29 Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.”
Ait ergo ei rex: Quid ultra loqueris? fixum est quod locutus sum: tu, et Siba dividite possessiones.
30 Mefiboseti anati kwa mfumu, “Muloleni atenge zonse, pakuti tsopano mbuye wanga mwafika kwanu mu mtendere.”
Responditque Miphiboseth regi: Etiam cuncta accipiat, postquam reversus est dominus meus rex pacifice in domum suam.
31 Barizilai Mgiliyadi anabweranso kuchokera ku Rogelimu kudzawoloka Yorodani ndi mfumu ndi kumuperekeza kuchokera kumeneko.
Berzellai quoque Galaadites, descendens de Rogelim, traduxit regem Iordanem, paratus etiam ultra fluvium prosequi eum.
32 Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri.
Erat autem Berzellai Galaadites senex valde, id est octogenarius, et ipse præbuit alimenta regi, cum moraretur in Castris: fuit quippe vir dives nimis.
33 Mfumu inati kwa Barizilai, “Woloka nane ndipo ukakhale ndi ine mu Yerusalemu ndipo ineyo ndidzakusamalira.”
Dixit itaque rex ad Berzellai: Veni mecum, ut requiescas securus mecum in Ierusalem.
34 Barizilai anayankha mfumu kuti, “Kodi zakhala zaka zingati zoti ndikhale ndi moyo, kuti ndipite ku Yerusalemu ndi mfumu?
Et ait Berzellai ad regem: Quot sunt dies annorum vitæ meæ, ut ascendam cum rege in Ierusalem?
35 Ine tsopano ndili ndi zaka 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa? Kodi mtumiki wanu angathe kuzindikira kukoma kwa zimene akudya ndi kumwa? Kodi ndingathe kumva kuyimba kwa amuna ndi akazi? Nʼchifukwa chiyani wantchito wanu akakhale ngati katundu kwa mbuye wanga mfumu?
Octogenarius sum hodie: numquid vigent sensus mei ad discernendum suave, aut amarum? aut delectare potest servum tuum cibus et potus? vel audire possum ultra vocem cantorum, atque cantatricum? quare servus tuus sit oneri domino meo regi?
36 Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pangʼono kuti ndiwoloke Yorodani pamodzi ndi mfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere?
Paululum procedam famulus tuus ab Iordane tecum: non indigeo hac vicissitudine,
37 Muloleni, mtumiki wanu abwerere, kuti ndikafere kwathu pafupi ndi manda a abambo ndi amayi anga. Koma nayu mtumiki wanu Kimuhamu. Muloleni iye awoloke nanu mbuye wanga mfumu. Mumuchitire chilichonse chimene chikukomereni!”
sed obsecro ut revertar servus tuus, et moriar in civitate mea, et sepeliar iuxta sepulchrum patris mei, et matris meæ. Est autem servus tuus Chamaam, ipse vadat tecum, domine mi rex, et fac ei quidquid tibi bonum videtur.
38 Mfumu inati, “Kimuhamu adzawoloka ndi ine, ndipo ndidzamuchitira iye chilichonse chimene chidzakondweretsa iwe. Ndipo chilichonse chimene udzandipempha ine ndidzakuchitira.”
Dixit itaque ei rex: Mecum transeat Chamaam, et ego faciam ei quidquid tibi placuerit, et omne, quod petieris a me, impetrabis.
39 Kotero anthu onse anawoloka Yorodani ndipo kenaka mfumu inawoloka. Mfumu inapsompsona Barizilai ndi kumupatsa madalitso ndipo Barizilaiyo anabwerera kwawo.
Cumque transisset universus populus et rex Iordanem, osculatus est rex Berzellai, et benedixit ei: et ille reversus est in locum suum.
40 Pamene mfumu inawolokera ku Giligala, Kimuhamu anawoloka naye. Ankhondo onse a Yuda ndi theka la ankhondo a Israeli onse anaperekeza mfumu.
Transivit ergo rex in Galgalam, et Chamaam cum eo. omnis autem populus Iuda traduxerat regem, et media tantum pars adfuerat de populo Israel.
41 Kenaka Aisraeli onse amabwera kwa mfumu nʼkumati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani abale athu, anthu a ku Ayuda, anakubani mfumu, nawoloka nanu Yorodani inu ndi banja lanu, pamodzi ndi anthu ake onse?”
Itaque omnes viri Israel concurrentes ad regem dixerunt ei: Quare te furati sunt fratres nostri viri Iuda, et traduxerunt regem et domum eius Iordanem, omnesque viros David cum eo?
42 Ayuda onse anayankha Aisraeli kuti, “Ife timachita zimenezi chifukwa mfumu ndi mʼbale wathu. Nʼchifukwa chiyani inu mwapsa mtima ndi zimenezi? Kodi ife tinadya chakudya chilichonse cha mfumu? Kodi chilipo chimene ife tatenga kukhala chathu?”
Et respondit omnis vir Iuda ad viros Israel: Quia mihi propior est rex: cur irasceris super hac re? numquid comedimus aliquid ex rege, aut munera nobis data sunt?
43 Aisraeli anayankha Ayuda kuti, “Ife ndi magawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo kuwonjezera apo, ife tili ndi zinthu zambiri mwa Davide kuposa inu. Tsono nʼchifukwa chiyani mukutichita chipongwe? Kodi ife si amene tinayamba kunena za kubweretsa mfumu yathu?” Koma anthu a Yuda anayankha mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israeli.
Et respondit vir Israel ad viros Iuda, et ait: Decem partibus maior ego sum apud regem, magisque ad me pertinet David quam ad te: cur fecisti mihi iniuriam, et non mihi nunciatum est priori, ut reducerem regem meum? Durius autem responderunt viri Iuda viris Israel.

< 2 Samueli 19 >