< 2 Samueli 16 >

1 Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo.
Cumque David transisset paululum montis verticem, apparuit Siba puer Miphiboseth in occursum eius, cum duobus asinis, qui onerati erant ducentis panibus, et centum alligaturis uvæ passæ, et centum massis palatharum, et utre vini.
2 Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?” Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.”
Et dixit rex Sibæ. Quid sibi volunt hæc? Responditque Siba: Asini, domesticis regis ut sedeant: panes et palathæ ad vescendum pueris tuis: vinum autem ut bibat siquis defecerit in deserto.
3 Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?” Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’”
Et ait rex: Ubi est filius domini tui? Responditque Siba regi: Remansit in Ierusalem, dicens: Hodie restituet mihi domus Israel regnum patris mei.
4 Ndipo mfumu inati kwa Ziba, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako tsopano.” Ziba anati, “Ine modzichepetsa ndikukugwandirani, mbuye wanga mfumu, kuti ndipeze chisomo pamaso panu.”
Et ait rex Sibæ: Tua sint omnia quæ fuerunt Miphiboseth. Dixitque Siba: Oro ut inveniam gratiam coram te, domine mi rex.
5 Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera.
Venit ergo rex David usque Bahurim: et ecce egrediebatur inde vir de cognatione domus Saul, nomine Semei, filius Gera, procedebatque egrediens, et maledicebat,
6 Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake.
mittebatque lapides contra David, et contra universos servos regis David: omnis autem populus, et universi bellatores a dextro, et a sinistro latere regis incedebant.
7 Potukwana, Simeiyo amati, “Choka iwe, choka iwe, munthu wopha anthu, munthu wachabechabe iwe!
Ita autem loquebatur Semei cum malediceret regi: Egredere, egredere vir sanguinum, et vir Belial.
8 Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!”
Reddidit tibi Dominus universum sanguinem domus Saul: quoniam invasisti regnum pro eo, et dedit Dominus regnum in manu Absalom filii tui, et ecce premunt te mala tua, quoniam vir sanguinum es.
9 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.”
Dixit autem Abisai filius Sarviæ, regi: Quare maledicit canis hic mortuus domino meo regi? vadam, et amputabo caput eius.
10 Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’”
Et ait rex: Quid mihi et vobis est filii Sarviæ? dimittite eum, ut maledicat: Dominus enim præcepit ei ut malediceret David: et quis est qui audeat dicere, quare sic fecerit?
11 Tsono Davide anati kwa Abisai ndi akuluakulu ake onse, “Mwana wanga wobereka ndekha akufuna kundipha. Nanji tsono munthu wa fuko la Benjamini uyu! Musiyeni; mulekeni atukwane pakuti Yehova wachita kumuwuza kuti atero.
Et ait rex Abisai, et universis servis suis: Ecce filius meus, qui egressus est de utero meo, quærit animam meam: quanto magis nunc filius Iemini? dimittite eum ut maledicat iuxta præceptum Domini:
12 Mwina Yehova adzaona mazunzo anga ndipo adzandibwezera zabwino chifukwa cha kutukwanidwa kumene ndikulandira lero.”
si forte respiciat Dominus afflictionem meam, et reddat mihi Dominus bonum pro maledictione hac hodierna.
13 Kotero Davide ndi anthu ake anapitirira kuyenda mu msewu pamene Simei amayenda mʼmbali mwa phiri moyangʼanana naye akutukwana ndi kuponya miyala pamene amayenda nʼkumamutsiranso dothi.
Ambulabat itaque David et socii eius per viam cum eo. Semei autem per iugum montis ex latere, contra illum gradiebatur, maledicens, et mittens lapides adversum eum, terramque spargens.
14 Mfumu ndi anthu ake onse anafika kumene amapita atatopa kwambiri. Ndipo kumeneko anapumula.
Venit itaque rex, et universus populus cum eo lassus, et refocillati sunt ibi.
15 Pa nthawi imeneyi Abisalomu ndi Aisraeli ena onse anabwera ku Yerusalemu, Ahitofele anali naye.
Absalom autem et omnis populus eius ingressi sunt Ierusalem, sed et Achitophel cum eo.
16 Tsono Husai Mwariki bwenzi la Davide anapita kwa Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu! Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”
Cum autem venisset Chusai Arachites amicus David ad Absalom, locutus est ad eum: Salve rex, salve rex.
17 Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?”
Ad quem Absalom, Hæc est, inquit, gratia tua ad amicum tuum? quare non ivisti cum amico tuo?
18 Husai anati kwa Abisalomu, “Ayi, ndidzakhala wake wa amene Yehova wamusankha, wosankhidwa ndi anthu awa ndi anthu onse a Israeli, ndipo ndidzakhala wake nthawi zonse.
Responditque Chusai ad Absalom: Nequaquam: quia illius ero, quem elegit Dominus, et omnis hic populus, et universus Israel, et cum eo manebo.
19 Kodi ndidzatumikiranso yani? Kodi sinditumikira mwana wa mfumu? Monga momwe ndinatumikira abambo anu, kotero ndidzatumikiranso inu.”
Sed ut et hoc inferam, cui ego serviturus sum? nonne filio regis? sicut parui patri tuo, ita parebo et tibi.
20 Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?”
Dixit autem Absalom ad Achitophel: Inite consilium quid agere debeamus.
21 Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.”
Et ait Achitophel ad Absalom: Ingredere ad concubinas patris tui, quas dimisit ad custodiendam domum: ut cum audierit omnis Israel quod fœdaveris patrem tuum, roborentur tecum manus eorum.
22 Choncho anamangira tenti Abisalomu pa denga la nyumba ndipo iye anagona ndi azikazi a abambo ake Aisraeli onse akuona.
Tetenderunt ergo Absalom tabernaculum in solario, ingressusque est ad concubinas patris sui coram universo Israel.
23 Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele.
Consilium autem Achitophel, quod dabat in diebus illis, quasi siquis consuleret Deum: sic erat omne consilium Achitophel, et cum esset cum David, et cum esset cum Absalom.

< 2 Samueli 16 >