< 2 Samueli 15 >

1 Patapita nthawi, Abisalomu anadzipezera galeta ndi akavalo pamodzi ndi amuna makumi asanu amene amathamanga patsogolo pake.
ויהי מאחרי כן ויעש לו אבשלום מרכבה וססים וחמשים איש רצים לפניו׃
2 Iye amadzuka mmamawa ndi kuyima pa njira yopita ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi zodandaula zopita nazo kwa mfumu kuti akaweruze, Abisalomu amamuyitana iye ndi kumufunsa kuti, “Kodi ukuchokera ku limodzi mwa mafuko a Israeli?”
והשכים אבשלום ועמד על יד דרך השער ויהי כל האיש אשר יהיה לו ריב לבוא אל המלך למשפט ויקרא אבשלום אליו ויאמר אי מזה עיר אתה ויאמר מאחד שבטי ישראל עבדך׃
3 Kenaka Abisalomu amanena kwa iye kuti, “Taona, madandawulo ako ndi abwino ndi oyenera, koma palibe woyimira mfumu woti akumvere.”
ויאמר אליו אבשלום ראה דברך טובים ונכחים ושמע אין לך מאת המלך׃
4 Ndipo Abisalomu amawonjezera kunena kuti, “Ine ndikanangosankhidwa kukhala woweruza mʼdziko muno bwenzi munthu aliyense amene ali ndi madandawulo kapena milandu akubwera kwa ine ndipo ndikanaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.”
ויאמר אבשלום מי ישמני שפט בארץ ועלי יבוא כל איש אשר יהיה לו ריב ומשפט והצדקתיו׃
5 Ndipo nthawi zonse amati munthu akasendera pafupi ndi kumugwandira, Abisalomu amatambalitsa dzanja lake, kumuyimiritsa munthuyo ndi kupsompsona.
והיה בקרב איש להשתחות לו ושלח את ידו והחזיק לו ונשק לו׃
6 Abisalomu amachitira izi Aisraeli onse amene amabwera kwa mfumu kuti adzaweruzidwe ndipo Abisalomuyo anagwira mtima anthu a mu Israeli.
ויעש אבשלום כדבר הזה לכל ישראל אשר יבאו למשפט אל המלך ויגנב אבשלום את לב אנשי ישראל׃
7 Patapita zaka zinayi Abisalomu anati kwa mfumu, “Loleni ndipite ku Hebroni kuti ndikakwaniritse lonjezo limene ndinachita kwa Yehova.
ויהי מקץ ארבעים שנה ויאמר אבשלום אל המלך אלכה נא ואשלם את נדרי אשר נדרתי ליהוה בחברון׃
8 Pamene mtumiki wanu amakhala ku Gesuri ku Aramu, anachita lonjezo ili: ‘Ngati Yehova adzandibweretsadi ku Yerusalemu, ndidzapembedza Yehovayo mu Hebroni.’”
כי נדר נדר עבדך בשבתי בגשור בארם לאמר אם ישיב ישיבני יהוה ירושלם ועבדתי את יהוה׃
9 Mfumu inati kwa iye, “Pita mu mtendere” Kotero iye anapita ku Hebroni.
ויאמר לו המלך לך בשלום ויקם וילך חברונה׃
10 Ndipo Abisalomu anatuma amithenga ake mwamseri kwa mafuko onse a Israeli kukanena kuti, “Mukangomva kulira kwa malipenga pamenepo munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu mu Hebroni.’”
וישלח אבשלום מרגלים בכל שבטי ישראל לאמר כשמעכם את קול השפר ואמרתם מלך אבשלום בחברון׃
11 Anthu 200 ochokera mu Yerusalemu anapita naye Abisalomu. Iwo anayitanidwa monga alendo ndipo anapita osadziwa chilichonse pa nkhaniyi.
ואת אבשלום הלכו מאתים איש מירושלם קראים והלכים לתמם ולא ידעו כל דבר׃
12 Pamene Abisalomu amapereka nsembe, iye anayitanitsanso Ahitofele Mgiloni, mlangizi wa Davide, wa ku Gilo, kotero kuwukiraku kunakula kwambiri, ndipo anthu otsatira Abisalomu anapitirira kuchuluka.
וישלח אבשלום את אחיתפל הגילני יועץ דוד מעירו מגלה בזבחו את הזבחים ויהי הקשר אמץ והעם הולך ורב את אבשלום׃
13 Munthu wina anabweretsa uthenga ndi kudzamuwuza Davide kuti, “Mitima ya Aisraeli onse ili pa Abisalomu.”
ויבא המגיד אל דוד לאמר היה לב איש ישראל אחרי אבשלום׃
14 Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.”
ויאמר דוד לכל עבדיו אשר אתו בירושלם קומו ונברחה כי לא תהיה לנו פליטה מפני אבשלום מהרו ללכת פן ימהר והשגנו והדיח עלינו את הרעה והכה העיר לפי חרב׃
15 Akuluakulu a mfumu anamuyankha kuti, “Antchito anu ndi okonzeka kuchita chilichonse chimene mbuye wathu mfumu mukufuna kuchita.”
ויאמרו עבדי המלך אל המלך ככל אשר יבחר אדני המלך הנה עבדיך׃
16 Mfumu inanyamuka pamodzi ndi banja lake lonse. Koma iye anasiya azikazi khumi kuti azisamalira nyumba yaufumu.
ויצא המלך וכל ביתו ברגליו ויעזב המלך את עשר נשים פלגשים לשמר הבית׃
17 Kotero mfumu inanyamuka pamodzi ndi anthu onse oyitsatira, ndipo anayima pamalo pena chapatalipo.
ויצא המלך וכל העם ברגליו ויעמדו בית המרחק׃
18 Ankhondo ake onse anayamba kuyenda pamaso pa Davide, ndipo Akereti ndi Apeleti, pamodzinso ndi Agiti okwanira 600 amene anamutsata kuchokera ku Gati, nawonso anayenda pamaso pake.
וכל עבדיו עברים על ידו וכל הכרתי וכל הפלתי וכל הגתים שש מאות איש אשר באו ברגלו מגת עברים על פני המלך׃
19 Mfumu inati kwa Itai Mgiti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ukupita ndi ife? Bwerera ndipo ukakhale ndi mfumu Abisalomu. Iwe ndiwe mlendo munthu wothawa kwawo.
ויאמר המלך אל אתי הגתי למה תלך גם אתה אתנו שוב ושב עם המלך כי נכרי אתה וגם גלה אתה למקומך׃
20 Wangobwera dzulo lomweli, lero ndikutenge kuti uziyendayenda ndi ife, pamene ine sindikudziwa kumene ndikupita? Bwerera, ndipo tenga abale ako. Chifundo ndi kukhulupirika zikhale nawe.”
תמול בואך והיום אנועך עמנו ללכת ואני הולך על אשר אני הולך שוב והשב את אחיך עמך חסד ואמת׃
21 Koma Itai anayankha mfumu kuti, “Pali Yehova wamoyo, kulikonse kumene mbuye wanga mfumu mudzakhala, kaya ndi moyo kapena imfa, mtumiki wanu adzakhala komweko.”
ויען אתי את המלך ויאמר חי יהוה וחי אדני המלך כי אם במקום אשר יהיה שם אדני המלך אם למות אם לחיים כי שם יהיה עבדך׃
22 Davide anati kwa Itai, “Tiye pita nafe” Kotero Itai Mgiti anayenda pamodzi ndi anthu ake ndi mabanja amene anali naye.
ויאמר דוד אל אתי לך ועבר ויעבר אתי הגתי וכל אנשיו וכל הטף אשר אתו׃
23 Anthu onse a madera ozungulira analira mofuwula pamene anthu onsewo amadutsa. Mfumunso inawoloka chigwa cha Kidroni, ndipo anthu onse anayenda kulowera ku chipululu.
וכל הארץ בוכים קול גדול וכל העם עברים והמלך עבר בנחל קדרון וכל העם עברים על פני דרך את המדבר׃
24 Zadoki anali nawonso, ndipo Alevi onse amene anali naye ananyamula Bokosi la Chipangano la Mulungu. Iwo anayika pansi Bokosi la Mulungulo ndipo Abiatara ankapereka nsembe mpaka pamene anthu onse anamaliza kutuluka mu mzinda.
והנה גם צדוק וכל הלוים אתו נשאים את ארון ברית האלהים ויצקו את ארון האלהים ויעל אביתר עד תם כל העם לעבור מן העיר׃
25 Kenaka mfumu inati kwa Zadoki, “Tenga Bokosi la Mulungu ubwerere nalo mu mzinda. Ngati ndidzapeza chifundo pamaso pa Yehova, adzandibweretsa kuti ndilionenso ndi malo ake okhalamo.
ויאמר המלך לצדוק השב את ארון האלהים העיר אם אמצא חן בעיני יהוה והשבני והראני אתו ואת נוהו׃
26 Koma iye anati, ‘Akapanda kukondwera nane,’ chabwino, andichite chimene chimukomere.”
ואם כה יאמר לא חפצתי בך הנני יעשה לי כאשר טוב בעיניו׃
27 Mfumu inatinso kwa wansembe Zadoki, “Kodi siwe mlosi? Bwerera mu mzinda mwamtendere pamodzi ndi mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiatara. Iwe ndi Abiatara tengani ana anu awiri.
ויאמר המלך אל צדוק הכהן הרואה אתה שבה העיר בשלום ואחימעץ בנך ויהונתן בן אביתר שני בניכם אתכם׃
28 Ine ndidzadikira powolokera Yorodani ku chipululu mpaka nditalandira mawu ochokera kwa iwe ondiwuza mmene zilili zinthu.”
ראו אנכי מתמהמה בעברות המדבר עד בוא דבר מעמכם להגיד לי׃
29 Kotero Zadoki ndi Abiatara ananyamula Bokosi la Mulungu lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo anakakhala kumeneko.
וישב צדוק ואביתר את ארון האלהים ירושלם וישבו שם׃
30 Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita.
ודוד עלה במעלה הזיתים עלה ובוכה וראש לו חפוי והוא הלך יחף וכל העם אשר אתו חפו איש ראשו ועלו עלה ובכה׃
31 Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.”
ודוד הגיד לאמר אחיתפל בקשרים עם אבשלום ויאמר דוד סכל נא את עצת אחיתפל יהוה׃
32 Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe anthu ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki anadzakumana naye atangʼamba mkanjo wake ndi kudzithira fumbi kumutu.
ויהי דוד בא עד הראש אשר ישתחוה שם לאלהים והנה לקראתו חושי הארכי קרוע כתנתו ואדמה על ראשו׃
33 Davide anati kwa iye, “Ngati iwe upite ndi ine, udzakhala chondilemetsa.
ויאמר לו דוד אם עברת אתי והית עלי למשא׃
34 Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele.
ואם העיר תשוב ואמרת לאבשלום עבדך אני המלך אהיה עבד אביך ואני מאז ועתה ואני עבדך והפרתה לי את עצת אחיתפל׃
35 Kodi ansembe, Zadoki ndi Abiatara, sakukhala nawe kumeneko? Ukawawuze zonse zimene umamva mʼnyumba yaufumu.
והלוא עמך שם צדוק ואביתר הכהנים והיה כל הדבר אשר תשמע מבית המלך תגיד לצדוק ולאביתר הכהנים׃
36 Ana awo awiri, Ahimaazi wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiatara ali nawo pamodzi, uzikawatuma kwa ine ndi china chilichonse chimene ukamve.”
הנה שם עמם שני בניהם אחימעץ לצדוק ויהונתן לאביתר ושלחתם בידם אלי כל דבר אשר תשמעו׃
37 Ndipo Husai bwenzi la Davide anafika ku Yerusalemu pamene Abisalomu amalowa mu mzinda.
ויבא חושי רעה דוד העיר ואבשלם יבא ירושלם׃

< 2 Samueli 15 >