< 2 Samueli 13 >
1 Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola.
大衛的兒子押沙龍有一個美貌的妹子,名叫她瑪。大衛的兒子暗嫩愛她。
2 Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye.
暗嫩為他妹子她瑪憂急成病。她瑪還是處女,暗嫩以為難向她行事。
3 Koma Amnoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu mwana wamwamuna wa Simea, mʼbale wake wa Davide. Yonadabu anali munthu wochenjera kwambiri.
暗嫩有一個朋友,名叫約拿達,是大衛長兄示米亞的兒子。這約拿達為人極其狡猾;
4 Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?” Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.”
他問暗嫩說:「王的兒子啊,為何一天比一天瘦弱呢?請你告訴我。」暗嫩回答說:「我愛我兄弟押沙龍的妹子她瑪。」
5 Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.”
約拿達說:「你不如躺在床上裝病;你父親來看你,就對他說:『求父叫我妹子她瑪來,在我眼前預備食物,遞給我吃,使我看見,好從她手裏接過來吃。』」
6 Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.”
於是暗嫩躺臥裝病。王來看他,他對王說:「求父叫我妹子她瑪來,在我眼前為我做兩個餅,我好從她手裏接過來吃。」
7 Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.”
大衛就打發人到宮裏,對她瑪說:「你往你哥哥暗嫩的屋裏去,為他預備食物。」
8 Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo.
她瑪就到她哥哥暗嫩的屋裏;暗嫩正躺臥。她瑪摶麵,在他眼前做餅,且烤熟了,
9 Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana. Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka.
在他面前將餅從鍋裏倒出來,他卻不肯吃,便說:「眾人離開我出去吧!」眾人就都離開他,出去了。
10 Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake.
暗嫩對她瑪說:「你把食物拿進臥房,我好從你手裏接過來吃。」她瑪就把所做的餅拿進臥房,到她哥哥暗嫩那裏,
11 Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.”
拿着餅上前給他吃,他便拉住她瑪,說:「我妹妹,你來與我同寢。」
12 Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere.
她瑪說:「我哥哥,不要玷辱我。以色列人中不當這樣行,你不要做這醜事;
13 Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.”
你玷辱了我,我何以掩蓋我的羞恥呢?你在以色列中也成了愚妄人。你可以求王,他必不禁止我歸你。」
14 Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira.
但暗嫩不肯聽她的話,因比她力大,就玷辱她,與她同寢。
15 Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!”
隨後,暗嫩極其恨她,那恨她的心比先前愛她的心更甚,對她說:「你起來,去吧!」
16 Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.” Koma anakana kumumvera.
她瑪說:「不要這樣!你趕出我去的這罪比你才行的更重!」但暗嫩不肯聽她的話,
17 Amnoni anayitana wantchito wake ndipo anati, “Mutulutse mkazi uyu muno ndipo utseke chitseko akatuluka.”
就叫伺候自己的僕人來,說:「將這個女子趕出去!她一出去,你就關門,上閂。」
18 Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala.
那時她瑪穿着彩衣,因為沒有出嫁的公主都是這樣穿。暗嫩的僕人就把她趕出去,關門上閂。
19 Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita.
她瑪把灰塵撒在頭上,撕裂所穿的彩衣,以手抱頭,一面行走,一面哭喊。
20 Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa.
她胞兄押沙龍問她說:「莫非你哥哥暗嫩與你親近了嗎?我妹妹,暫且不要作聲,他是你的哥哥,不要將這事放在心上。」她瑪就孤孤單單地住在她胞兄押沙龍家裏。
21 Mfumu Davide itamva zimenezi, inakwiya kwambiri.
大衛王聽見這事,就甚發怒。
22 Abisalomu sananene mawu aliwonse kwa Amnoni; abwino kapena oyipa. Iye anamuda Amunoniyo chifukwa anachititsa manyazi mlongo wake Tamara.
押沙龍並不和他哥哥暗嫩說好說歹;因為暗嫩玷辱他妹妹她瑪,所以押沙龍恨惡他。
23 Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko.
過了二年,在靠近以法蓮的巴力‧夏瑣有人為押沙龍剪羊毛;押沙龍請王的眾子與他同去。
24 Abisalomu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Ometa nkhosa za mtumiki wanu anabwera. Chonde mfumu ndi akuluakulu anu mubwere kudzakhala nane?”
押沙龍來見王,說:「現在有人為僕人剪羊毛,請王和王的臣僕與僕人同去。」
25 Mfumu inayankha kuti, “Ayi mwana wanga, tisapite tonsefe. Tidzakhala cholemetsa kwa iwe.” Ngakhale Abisalomu anayesetsa kuwumiriza mfumuyo, inakana kupita. Mʼmalo mwake inangomudalitsa Abisalomuyo.
王對押沙龍說:「我兒,我們不必都去,恐怕使你耗費太多。」押沙龍再三請王,王仍是不肯去,只為他祝福。
26 Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.” Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?”
押沙龍說:「王若不去,求王許我哥哥暗嫩同去。」王說:「何必要他去呢?」
27 Koma Abisalomu anamuwumiriza, kotero analola kuti Amnoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye.
押沙龍再三求王,王就許暗嫩和王的眾子與他同去。
28 Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.”
押沙龍吩咐僕人說:「你們注意,看暗嫩飲酒暢快的時候,我對你們說殺暗嫩,你們便殺他,不要懼怕。這不是我吩咐你們的嗎?你們只管壯膽奮勇!」
29 Kotero antchito a Abisalomu anachita kwa Amnoni zimene Abisalomu anawalamula. Kenaka ana onse a mfumu anayimirira ndipo anakwera pa abulu awo nathawa.
押沙龍的僕人就照押沙龍所吩咐的,向暗嫩行了。王的眾子都起來,各人騎上騾子,逃跑了。
30 Ali mʼnjira, Davide anamva mphekesera yakuti, “Abisalomu wakantha ana onse a mfumu ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala.”
他們還在路上,有風聲傳到大衛那裏,說:「押沙龍將王的眾子都殺了,沒有留下一個。」
31 Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo.
王就起來,撕裂衣服,躺在地上。王的臣僕也都撕裂衣服,站在旁邊。
32 Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara.
大衛的長兄,示米亞的兒子約拿達說:「我主,不要以為王的眾子-少年人都殺了,只有暗嫩一個人死了。自從暗嫩玷辱押沙龍妹子她瑪的那日,押沙龍就定意殺暗嫩了。
33 Mbuye wanga mfumu musavutike ndi maganizo ndi nkhani yoti ana onse a mfumu afa. Wafa ndi Amnoni yekha.”
現在,我主我王,不要把這事放在心上,以為王的眾子都死了,只有暗嫩一個人死了。」
34 Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa. Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.”
押沙龍逃跑了。 守望的少年人舉目觀看,見有許多人從山坡的路上來。
35 Yehonadabu anati kwa mfumu, “Taonani ana a mfumu afika. Zachitika monga momwe mtumiki wanu ananenera.”
約拿達對王說:「看哪,王的眾子都來了,果然與你僕人所說的相合。」
36 Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa.
話才說完,王的眾子都到了,放聲大哭;王和臣僕也都哭得甚慟。
37 Abisalomu anathawa, napita kwa Talimai mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Koma mfumu Davide inalira mwana wake tsiku ndi tsiku.
押沙龍逃到基述王亞米忽的兒子達買那裏去了。大衛天天為他兒子悲哀。
38 Abisalomu atathawa ndi kupita ku Gesuri, anakhala kumeneko zaka zitatu.
押沙龍逃到基述,在那裏住了三年。
39 Ndipo Davide anagwidwa ndi chifundo chofuna kumulondola Abisalomu pakuti anali atatonthozedwa pa imfa ya Amnoni.
暗嫩死了以後,大衛王得了安慰,心裏切切想念押沙龍。