< 2 Samueli 11 >

1 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.
It came about in the springtime, at the time when kings normally go to war, that David sent out Joab, his servants, and all the army of Israel. They destroyed the army of Ammon and besieged Rabbah. But David stayed in Jerusalem.
2 Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri.
So it came about one evening that David got up from his bed and walked on the roof of his palace. From there he happened to see a woman who was bathing, and the woman was very beautiful to look at.
3 Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?”
So David sent and he asked people who would know about the woman. Someone said, “Is not this Bathsheba, the daughter of Eliam, and is she not the wife of Uriah the Hittite?”
4 Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake.
David sent messengers and took her; she came in to him, and he slept with her (for she had just purified herself from menstruation). Then she returned to her house.
5 Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.”
The woman conceived, and she sent and told David; she said, “I am pregnant.”
6 Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide.
Then David sent to Joab saying, “Send me Uriah the Hittite.” So Joab sent Uriah to David.
7 Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera.
When Uriah arrived, David asked him how Joab was, how the army was doing, and how the war was going.
8 Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya.
David said to Uriah, “Go down to your house and wash your feet.” So Uriah left the king's palace, and the king sent a gift for Uriah after he left.
9 Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake.
But Uriah slept at the door of the king's palace with all the servants of his master, and he did not go down to his house.
10 Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?”
When they told David, “Uriah did not go down to his house,” David said to Uriah, “Have you not come from a journey? Why did you not go down to your house?”
11 Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”
Uriah answered David, “The ark, and Israel and Judah are staying in tents, and my master Joab and my master's servants are camped in an open field. How then can I go into my house to eat and to drink and to sleep with my wife? As sure as you are alive, I will not do this.”
12 Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo.
So David said to Uriah, “Stay here today also, and tomorrow I will let you leave.” So Uriah stayed in Jerusalem that day and the next day.
13 Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake.
When David called him, he ate and drank before him, and David made him drunk. At evening Uriah went out to sleep on his bed with the servants of his master; he did not go down to his house.
14 Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya.
So in the morning David wrote a letter to Joab, and sent it by the hand of Uriah.
15 Mʼkalatayo analembamo kuti, “Uriya mumuyike patsogolo penipeni, pamene pali nkhondo yoopsa. Ndipo mumusiye yekha kuti akanthidwe ndi kufa.”
David wrote in the letter saying, “Set Uriah at the very front of the most intense battle, and then withdraw from him, that he may be hit and killed.”
16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu.
So as Joab watched the siege upon the city, he assigned Uriah to the place where he knew the strongest enemy soldiers would be fighting.
17 Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso.
When the men of the city went out and fought against Joab's army, some of the soldiers of David fell, and Uriah the Hittite was also killed there.
18 Yowabu anatumiza wamthenga kwa Davide kukafotokoza mwatsatanetsatane za nkhondoyo.
When Joab sent word to David about everything concerning the war,
19 Iye anamulangiza wa mthengayo kuti, “Pamene ukatsiriza kufotokozera mfumu za ku nkhondozi,
he commanded the messenger, saying, “When you have finished telling all the things concerning the war to the king,
20 mfumu ikapsa mtima, ndipo akakakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani munapita pafupi ndi mzindawo kukamenya nkhondo? Inu simunadziwe kuti atha kukuponyerani mivi kuchokera pa khoma?
it may happen that the king will become angry, and he will say to you, 'Why did you go so near to the city to fight? Did you not know that they would shoot from the wall?
21 Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’”
Who killed Abimelech son of Jerub-Besheth? Did not a woman cast an upper millstone on him from the wall, so that he died at Thebez? Why did you go so near the wall?' Then you must answer, 'Your servant Uriah the Hittite is dead also.'”
22 Mthengayo ananyamuka, ndipo atafika anamuwuza Davide zonse zimene Yowabu anamutuma kuti akanene.
So the messenger left and went to David and told him everything that Joab had sent him to say.
23 Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo.
Then the messenger said to David, “The enemy were stronger than we were at first; they came out to us into the field, but we drove them back to the entrance of the gate.
24 Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.”
Then their shooters shot at your soldiers from off the wall, and some of the king's servants were killed, and your servant Uriah the Hittite was killed too.”
25 Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.”
Then David said to the messenger, “Say this to Joab, 'Do not let this displease you, for the sword devours one as well as another. Make your battle even stronger against the city, and overthrow it,' and encourage him.”
26 Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, analira maliro.
So when the wife of Uriah heard that Uriah her husband was dead, she lamented deeply for her husband.
27 Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo.
When her sorrow passed, David sent and took her home to his palace, and she became his wife and bore him a son. But what David had done displeased Yahweh.

< 2 Samueli 11 >