< 2 Petro 1 >
1 Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.
Συμεὼν Πέτρος, δοῦλος καὶ ἀπόστολος Ἰησοῦ Χριστοῦ, τοῖς ἰσότιμον ἡμῖν λαχοῦσι πίστιν ἐν δικαιοσύνῃ τοῦ Θεοῦ ἡμῶν καὶ σωτῆρος Ἰησοῦ Χριστοῦ·
2 Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.
χάρις ὑμῖν καὶ εἰρήνη πληθυνθείη ἐν ἐπιγνώσει τοῦ Θεοῦ, καὶ Ἰησοῦ τοῦ Κυρίου ἡμῶν.
3 Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake.
Ὡς πάντα ἡμῖν τῆς θείας δυνάμεως αὐτοῦ τὰ πρὸς ζωὴν καὶ εὐσέβειαν δεδωρημένης, διὰ τῆς ἐπιγνώσεως τοῦ καλέσαντος ἡμᾶς διὰ δόξης καὶ ἀρετῆς·
4 Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.
δι᾽ ὧν τὰ τίμια ἡμῖν καὶ μέγιστα ἐπαγγέλματα δεδώρηται, ἵνα διὰ τούτων γένησθε θείας κοινωνοὶ φύσεως, ἀποφυγόντες τῆς ἐν κόσμῳ ἐν ἐπιθυμίᾳ φθορᾶς.
5 Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru.
Καὶ αὐτὸ τοῦτο δέ, σπουδὴν πᾶσαν παρεισενέγκαντες, ἐπιχορηγήσατε ἐν τῇ πίστει ὑμῶν τὴν ἀρετήν, ἐν δὲ τῇ ἀρετῇ τὴν γνῶσιν,
6 Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu.
ἐν δὲ τῇ γνώσει τὴν ἐγκράτειαν, ἐν δὲ τῇ ἐγκρατείᾳ τὴν ὑπομονήν, ἐν δὲ τῇ ὑπομονῇ τὴν εὐσέβειαν,
7 Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi.
ἐν δὲ τῇ εὐσεβείᾳ τὴν φιλαδελφίαν, ἐν δὲ τῇ φιλαδελφίᾳ τὴν ἀγάπην.
8 Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu.
Ταῦτα γὰρ ὑμῖν ὑπάρχοντα καὶ πλεονάζοντα, οὐκ ἀργοὺς οὐδὲ ἀκάρπους καθίστησιν εἰς τὴν τοῦ Κυρίου ἡμῶν Ἰησοῦ Χριστοῦ ἐπίγνωσιν.
9 Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale.
ᾯ γὰρ μὴ πάρεστι ταῦτα, τυφλός ἐστι, μυωπάζων, λήθην λαβὼν τοῦ καθαρισμοῦ τῶν πάλαι αὐτοῦ ἁμαρτιῶν.
10 Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse.
Διὸ μᾶλλον, ἀδελφοί, σπουδάσατε βεβαίαν ὑμῶν τὴν κλῆσιν καὶ ἐκλογὴν ποιεῖσθαι· ταῦτα γὰρ ποιοῦντες οὐ μὴ πταίσητέ ποτε·
11 Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. (aiōnios )
οὕτω γὰρ πλουσίως ἐπιχορηγηθήσεται ὑμῖν ἡ εἴσοδος εἰς τὴν αἰώνιον βασιλείαν τοῦ Κυρίου ἡμῶν καὶ σωτῆρος Ἰησοῦ Χριστοῦ. (aiōnios )
12 Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano.
Διὸ οὐκ ἀμελήσω ἀεὶ ὑμᾶς ὑπομιμνῄσκειν περὶ τούτων, καίπερ εἰδότας, καὶ ἐστηριγμένους ἐν τῇ παρούσῃ ἀληθείᾳ.
13 Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani,
Δίκαιον δὲ ἡγοῦμαι, ἐφ᾽ ὅσον εἰμὶ ἐν τούτῳ τῷ σκηνώματι, διεγείρειν ὑμᾶς ἐν ὑπομνήσει·
14 chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu.
εἰδὼς ὅτι ταχινή ἐστιν ἡ ἀπόθεσις τοῦ σκηνώματός μου, καθὼς καὶ ὁ Κύριος ἡμῶν Ἰησοῦς Χριστὸς ἐδήλωσέ μοι.
15 Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse.
Σπουδάσω δὲ καὶ ἑκάστοτε ἔχειν ὑμᾶς μετὰ τὴν ἐμὴν ἔξοδον τὴν τούτων μνήμην ποιεῖσθαι.
16 Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake.
Οὐ γὰρ σεσοφισμένοις μύθοις ἐξακολουθήσαντες ἐγνωρίσαμεν ὑμῖν τὴν τοῦ Κυρίου ἡμῶν Ἰησοῦ Χριστοῦ δύναμιν καὶ παρουσίαν, ἀλλ᾽ ἐπόπται γενηθέντες τῆς ἐκείνου μεγαλειότητος.
17 Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.”
Λαβὼν γὰρ παρὰ Θεοῦ πατρὸς τιμὴν καὶ δόξαν, φωνῆς ἐνεχθείσης αὐτῷ τοιᾶσδε ὑπὸ τῆς μεγαλοπρεποῦς δόξης, Οὗτός ἐστιν ὁ υἱός μου ὁ ἀγαπητός, εἰς ὃν ἐγὼ εὐδόκησα·
18 Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija.
καὶ ταύτην τὴν φωνὴν ἡμεῖς ἠκούσαμεν ἐξ οὐρανοῦ ἐνεχθεῖσαν, σὺν αὐτῷ ὄντες ἐν τῷ ὄρει τῷ ἁγίῳ.
19 Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu.
Καὶ ἔχομεν βεβαιότερον τὸν προφητικὸν λόγον, ᾧ καλῶς ποιεῖτε προσέχοντες, ὡς λύχνῳ φαίνοντι ἐν αὐχμηρῷ τόπῳ, ἕως οὗ ἡμέρα διαυγάσῃ, καὶ φωσφόρος ἀνατείλῃ ἐν ταῖς καρδίαις ὑμῶν·
20 Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha.
τοῦτο πρῶτον γινώσκοντες, ὅτι πᾶσα προφητεία γραφῆς ἰδίας ἐπιλύσεως οὐ γίνεται.
21 Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.
Οὐ γὰρ θελήματι ἀνθρώπου ἠνέχθη ποτὲ προφητεία, ἀλλ᾽ ὑπὸ Πνεύματος Ἁγίου φερόμενοι ἐλάλησαν ἅγιοι Θεοῦ ἄνθρωποι.