< 2 Petro 2 >

1 Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi.
But there were also false prophets among the people, even as there will be false teachers among you; who will privately introduce destructive sects, denying even the Lord who bought them, bringing on themselves swift destruction.
2 Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi.
And many will follow their lewd practices, on account of whom, they way of truth will be evil spoken of.
3 Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira.
And through covetousness, they will make merchandise of you, by fictitious tales: to whom the punishment threatened of old lingers not, and their destruction slumbers not.
4 Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. (Tartaroō g5020)
For God, indeed, did not spare the angels who sinned, but with chains of darkness confining them in Tartarus, delivered them over to be kept for judgment; (Tartaroō g5020)
5 Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo.
and did not spare the old world, but saved Noah, the eighth, a proclaimer of righteousness, when he brought the flood upon the world of the ungodly;
6 Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu.
and having reduced to ashes the cities of Sodom and Gomorrah, punished them with an overthrow, making them an example to those who should afterward live ungodly:
7 Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa.
and rescued righteous Lot, exceedingly grieved by the lewd behavior of the lawless:
8 (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva).
(for; --that righteous man, dwelling among them, by the sight and report of their unlawful deeds, tormented his righteous soul from day to day; )
9 Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.
the Lord knows how to rescue the godly out of temptation, and to reserve the unrighteous to a day of judgment to be punished;
10 Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro. Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba.
but especially those who go after the flesh in the lust of uncleanness, and who despise government: being audacious, self-willed, who fear not to revile dignitaries;
11 Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye.
whereas, angels, who are greater in strength and power, do not bring a reviling accusation against them before the Lord.
12 Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa.
But these, as natural, irrational animals, made for capture and destruction, speaking evil of matters which they do not understand, shall be utterly destroyed by their own corruptions;
13 Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo.
receiving the due reward of unrighteousness. These delight to spend the day in luxurious festivity: they are spots and blemishes, reveling in their deceits when they feast with you;
14 Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa!
having eyes full of the adulteress, incessantly sinning, alluring unstable souls; having a heart exercised with insatiable desires; an accursed progeny:
15 Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama.
having forsaken the right path, they have wandered, following in the way of Balaam, the son of Bosor, who loved the wages of iniquity,
16 Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo.
and was convicted of his transgression; the dumb brute, speaking with man's voice, reprimanded the madness of the prophet.
17 Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani.
These are wells without water, clouds driven by a tempest; for whom the blackness of darkness is reserved forever:
18 Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa.
for, speaking great swelling words of falsehood, they allure by the lusts of the flesh, even by lasciviousness, those who have actually fled away from them who are living in error.
19 Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira.
They promise them liberty, whilst they themselves are slaves of corruption: for every one is enslaved by that which overcomes him.
20 Ngati anapulumuka ku zodetsa za dziko lapansi podziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, pambuyo pake nagwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zomwezo, potsiriza adzakhala oyipa kuposa mmene analili poyamba.
Now, if, having fled away from the pollutions of the world, through the knowledge of the Lord and Saviour Jesus Christ, and being again entangled, they are overcome by them; their last condition is worse than the first.
21 Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa.
Therefore, it has been better for them not to have known the way of righteousness, than having known it, turn away from the holy commandment delivered to them.
22 Kwa iwo miyambi iyi ndi yoona, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndipo, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhunizikanso mʼmatope.”
But the saying of the true proverb has happened to them: "The dog is returned to his own vomit; and the washed hog, to its wallowing in the mire."

< 2 Petro 2 >