< 2 Mafumu 1 >

1 Atamwalira Ahabu, Mowabu anawukira Israeli.
阿哈布死後,摩阿布就背叛了以色列。
2 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake chammwamba ku Samariya, ndipo anavulala kwambiri. Choncho iye anatuma amithenga nawawuza kuti, “Pitani mukafunse kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, ngati ndichire matendawa.”
阿哈齊雅在撒瑪黎雅從樓上的欄杆上跌下來就病了,遂打發使者,吩咐他們說:「你們去求問厄刻龍的神巴耳則步布,我這病寒能好嗎﹖」
3 Koma mngelo wa Yehova anawuza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake inu mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni?’
上主的使者對提市貝人厄里亞說:「快起身,去迎撒瑪黎雅王的使者,問他們說:你們去求問厄刻龍的神巴耳則步布,難道在以色列沒有天主嗎﹖
4 Tsono Yehova akuti, ‘Iweyo sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’” Ndipo Eliya ananyamuka.
為此,上主這樣說:你再不能從你所上的床上下來,你必定要死。」厄里亞就去了。
5 Amithenga aja atabwerera kwa mfumu, mfumuyo inawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwabwerera?”
使者回來見了君王,阿哈齊雅問他們說:「你們為什麼回來了。」
6 Iwo anayankha kuti, “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe, ndipo anatiwuza kuti, bwererani kwa mfumu imene inakutumani ndipo mukayiwuze kuti, ‘Yehova akuti, kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni? Tsono sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’”
他們回答說:「有一個人迎上我們來,對我們說:你們回去見打發你們來的君王,對他說:上主這樣說:你派人去求問厄刻龍的神巴耳則步布,難道以色列沒有天主嗎﹖為此,你再不能從你所上的床上下來,你必定要死。」
7 Mfumu inafunsa amithengawo kuti, “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo ndi kukuwuzani zimenezi amaoneka bwanji?”
君王問他們說:「迎上你們,且告訴你們這些話的是怎樣的一個人﹖」
8 Iwo anayankha kuti, “Munthuyo anavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake.” Mfumu inati, “Munthu ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.”
他們回答說,「是一個身穿皮毛衣,腰束皮帶的人。」君王說:「這一定是提市貝人厄里亞。」
9 Pamenepo mfumu inatuma mtsogoleri wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kwa Eliya. Mtsogoleriyo anapita kwa Eliya, amene anali atakhala pamwamba pa phiri, ndipo anati, “Munthu wa Mulungu, mfumu ikuti, ‘Tsikani!’”
王遂派五十夫長,帶領五十人,去見厄里亞。他上去見厄里亞,厄里亞正坐在山頂上。五十夫長便對厄里亞說:「天主的人,王命你下去。」
10 Eliya anayankha mtsogoleriyo kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu makumi asanu akowo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
厄里亞回答五十夫長說:「如果我是天主的人,願火從天降下,吞噬你和你這五十人! 」果然有火從天降下,吞噬了他和那五十人。
11 Zitachitika izi, mfumu inatumanso mtsogoleri wina pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleriyo anati kwa Eliya, “Munthu wa Mulungu, zimene mfumu ikunena ndi izi, ‘Tsikani msangamsanga!’”
王又另派一個五十夫長,帶領五十人,去見厄里亞。五十夫長上去對厄里亞說:「天主的人! 王這樣吩咐:要你快下山! 」
12 Eliya anayankha kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu ako makumi asanuwo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
厄里亞回答說:「如果我是天主的人,願火從天降下,吞噬你和你這五十人。」果然天主的火從天降下,吞噬了他和那五十人。
13 Ndipo mfumu inatumanso mtsogoleri wachitatu pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleri wachitatuyu anakwera pa phiripo ndi kugwada pamaso pa Eliya. Iye anayankhula mopemba kuti, “Munthu wa Mulungu, chonde musandiwononge ineyo pamodzi ndi atumiki makumi asanu anuwa!
王又派第三個五十夫長,帶領五十人去。這第三個五十夫長上去,一來到就屈膝跪在厄里亞面前,哀求他說:「天主的人,願我的生命和我這五十人的生命,在你眼中有點價值!
14 Taonani, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kupsereza atsogoleri awiri pamodzi ndi anthu awo onse. Koma tsopano musawononge moyo wanga!”
有火從天降下,吞噬了前兩個五十夫長,和他們每人帶領的五十人;現在,願我的生命在你眼中有點價值! 」
15 Mngelo wa Yehova anati kwa Eliya, “Pita naye, usamuope.” Choncho Eliya ananyamuka natsika naye limodzi kupita kwa mfumu.
上主的使者對厄里亞說:「你同他下去! 不必害怕。」厄里亞就起身同他一起下去見君王,
16 Eliya anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chiyani munatumiza amithenga kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, kukafunsa ngati muti muchire? Kodi mu Israeli mulibe Mulungu woti nʼkukuyankhani funso lanu? Choncho, popeza mwachita izi, simudzadzuka pamene mwagonapo; mudzafa ndithu.’”
對君王說:「上主這樣說:由於你打發使者去求問厄刻龍的神巴耳則步布,好像在以色列沒有天主可以向他求問指示一樣,因此,你再不能從你所上的床下來,你必定要死。」
17 Motero Ahaziya anafadi, monga mwa mawu a Yehova amene Eliya anayankhula. Tsono popeza Ahaziya analibe mwana, Yoramu analowa ufumu mʼmalo mwake mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda.
阿哈齊雅果然如上主藉著厄里亞所說的話死了;因為他沒有兒子,他的兄弟耶曷蘭繼位為王,時在猶大王約沙法特的兒子約蘭第二年。
18 Ntchito zina zonse zimene Ahaziya anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
阿哈齊雅其餘的事蹟,都記載在以色列列王實錄上。

< 2 Mafumu 1 >