< 2 Mafumu 9 >
1 Mneneri Elisa anayitanitsa mmodzi mwa ana a aneneri, namuwuza kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga botolo la mafuta mʼdzanja lako ndipo upite ku Ramoti Giliyadi.
선지자 엘리사가 선지자의 생도 중 하나를 불러 이르되 너는 허리를 동이고 이 기름병을 손에 가지고 길르앗 라못으로 가라
2 Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati.
거기 이르거든 님시의 손자 여호사밧의 아들 예후를 찾아 들어가서 그 형제 중에서 일어나게 하고 데리고 골방으로 들어가서
3 Ndipo ukatenge botololi ndi kuthira mafuta pa mutu wake ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ Kenaka ukatsekule chitseko ndi kuthawa ndipo usakachedwe!”
기름병을 가지고 그 머리에 부으며 이르기를 여호와의 말씀이 내가 네게 기름을 부어 이스라엘 왕을 삼노라 하셨느니라 하고 곧 문을 열고 도망하되 지체치 말지니라
4 Choncho mneneri wachinyamatayo anapita ku Ramoti Giliyadi.
그 소년 곧 소년 선지자가 드디어 길르앗 라못으로 가니라
5 Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.” Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?” Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”
저가 이르러 보니 군대 장관들이 앉았는지라 소년이 가로되 `장관이여 내가 당신에게 할 말씀이 있나이다' 예후가 가로되 `우리 모든 사람중에 뉘게 하려느냐' 가로되 `장관이여 당신에게니이다'
6 Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova.
예후가 일어나 집으로 들어가니 소년이 그 머리에 기름을 부으며 이르되 `이스라엘 하나님 여호와의 말씀이 내가 네게 기름을 부어 여호와의 백성 곧 이스라엘의 왕을 삼노니
7 Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli.
너는 네 주 아합의 집을 치라 내가 나의 종 곧 선지자들의 피와 여호와의 종들의 피를 이세벨에게 갚아주리라
8 Banja lonse la Ahabu lidzatheratu. Ndidzachotsa munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu kaya ndi kapolo kapena mfulu.
아합의 온 집이 멸망하리니 이스라엘 중에 매인 자나 놓인 자나 아합에게 속한 모든 남자는 내가 다 멸절하되
9 Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya.
아합의 집을 느밧의 아들 여로보암의 집과 같게 하며 또 아히야의 아들 바아사의 집과 같게 할지라
10 Kunena za Yezebeli, agalu adzamudya ku dera la Yezireeli ndipo palibe amene adzamuyike mʼmanda.’” Kenaka mneneriyo anatsekula chitseko nʼkuthawa.
이스르엘 지방에서 개들이 이세벨을 먹으리니 저를 장사할 사람이 없으리라 하셨느니라' 하고 곧 문을 열고 도망하니라
11 Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?” Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”
예후가 나와서 그 주의 신복들에게 이르니 한 사람이 묻되 평안이뇨 그 미친 자가 무슨 까닭으로 그대에게 왔더뇨 대답하되 그대들이 그 사람과 그 말한 것을 알리라
12 Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.” Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’”
무리가 가로되 당치 않은 말이라 그대는 우리에게 이르라 대답하되 저가 이리 이리 내게 말하여 이르기를 여호와의 말씀이 내가 네게 기름을 부어 이스라엘 왕을 삼는다 하셨다 하더라
13 Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”
무리가 각각 자기의 옷을 급히 취하여 섬돌 위 곧 예후의 밑에 깔고 나팔을 불며 가로되 예후는 왕이라 하니라
14 Choncho Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi, anachitira chiwembu Yoramu. (Nthawi imeneyi nʼkuti Yoramu ndi Aisraeli onse akuteteza Ramoti Giliyadi kwa Hazaeli mfumu ya ku Aramu,
이에 님시의 손자 여호사밧의 아들 예후가 요람을 배반하였으니 곧 요람이 온 이스라엘로 더불어 아람 왕 하사엘을 인하여 길르앗 라못을 지키다가
15 koma nʼkuti Yoramu atabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene Aaramu anamuvulaza pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya ku Aramu.) Yehu anati, “Ngati mukugwirizana nazo zimenezi, wina aliyense asatuluke mu mzinda muno kupita kukafotokoza nkhaniyi ku Yezireeli.”
아람 왕 하사엘로 더불어 싸울 때에 아람 사람에게 상한 것을 치료하려 하여 이스르엘로 돌아왔던 때라 예후가 이르되 너희 뜻에 합당하거든 한 사람이라도 이 성에서 도망하여 이스르엘에 전하러 가지 못하게 하라 하니라
16 Pamenepo Yehu anakwera galeta lake, napita ku Yezireeli, chifukwa Yoramu anali akupumula kumeneko ndipo Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, nʼkuti ali komweko kudzamuona.
예후가 병거를 타고 이스르엘로 가니 요람이 거기 누웠음이라 유다왕 아하시야는 요람을 보러 내려 왔더라
17 Mlonda amene ankayimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireeli ataona gulu lankhondo la Yehu likuyandikira, anafuwula kuti, “Ndikuona gulu lankhondo likubwera.” Yoramu analamula kuti, “Peza munthu wokwera kavalo, mutume kuti akakumane nawo ndi kuwafunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’”
이스르엘 망대에 파숫군 하나가 섰더니 예후의 무리의 오는 것을보고 가로되 내가 한 무리를 보나이다 요람이 가로되 한 사람을 말을 태워 보내어 맞아 평안이냐 묻게 하라
18 Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’” Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.” Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.”
한 사람이 말을 타고 가서 만나 가로되 왕의 말씀이 평안이냐 하시더이다 하매 예후가 가로되 평안이 네게 상관이 있느냐 내 뒤로 돌이키라 하니라 파숫군이 고하여 가로되 사자가 저희에게 갔으나 돌아오지 아니하나이다 하는지라
19 Choncho mfumu inatumanso munthu wina wachiwiri wokwera kavalo. Atafika kwa anthuwo iye anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’” Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”
다시 한 사람을 말을 태워 보내었더니 저희에게 가서 가로되 왕의 말씀이 평안이냐 하시더이다 하매 예후가 가로되 평안이 네게 상관이 있느냐 내 뒤로 돌이키라 하니라
20 Mlonda uja anakanenanso kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwereranso. Kuyendako kukukhala ngati kwa Yehu mwana wa Nimisi, iye amayenda ngati munthu wamisala.”
파숫군이 또 고하여 가로되 저도 저희에게까지 갔으나 돌아오지 아니하고 그 병거 모는 것이 님시의 손자 예후의 모는 것 같이 미치게 모나이다
21 Yoramu analamula kuti, “Konzani galeta langa.” Ndipo atakonza galeta lake, Yoramu mfumu ya Israeli ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda anakwera nʼkutuluka mu mzindamo, aliyense atakwera galeta lake, kukakumana ndi Yehu. Iwo anakumana ndi Yehu pa munda umene unali wa Naboti, wa ku Yezireeli.
요람이 가로되 메우라 하매 그 병거를 메운지라 이스라엘 왕 요람과 유다 왕 아하시야가 각각 그 병거를 타고 가서 예후를 맞을새 이스르엘 사람 나봇의 토지에서 만나매
22 Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?” Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”
요람이 예후를 보고 가로되 예후야 평안이냐 대답하되 네 어미 이세벨의 음행과 술수가 이렇게 많으니 어찌 평안이 있으랴
23 Yoramu anatembenuka, nathawa akufuwula kwa Ahaziya kuti, “Ahaziya, anthuwa atiwukira!”
요람이 곧 손을 돌이켜 도망하며 아하시야에게 이르되 아하시야여 반역이로다
24 Pamenepo Yehu anakoka uta wake ndipo analasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa. Muviwo unakalasa mtima wake ndipo anagwa pansi mʼgaleta lakelo.
예후가 힘을 다하여 활을 당기어 요람의 두 팔 사이를 쏘니 살이 그 염통을 꿰뚫고 나오매 저가 병거 가운데 엎드러진지라
25 Yehu anawuza Bidikara, mtsogoleri wa galeta lake kuti, “Munyamule ndipo ukamuponye mʼmunda umene unali wa Naboti wa ku Yezireeli, chifukwa kumbukira mmene iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu abambo ake, kuti Yehova ananeneratu za iye kuti,
예후가 그 장관 빗갈에게 이르되 그 시체를 취하여 이스르엘 사람 나봇의 밭에 던지라 네가 기억하려니와 이전에 너와 내가 함께 타고 그 아비 아합을 좇았을 때에 여호와께서 이 아래 같이 저의 일을 예언하셨느니라
26 ‘Zoonadi dzulo ndinaona magazi a Naboti ndi magazi a ana ake, akutero Yehova, ndipo Ine ndidzakubwezera ndithu choyipa chimenechi pa munda womwe uno, akutero Yehova.’ Tsono munyamule ndipo ukamuponye mʼmundamo, potsatira zimene Yehova ananena.”
여호와께서 말씀하시기를 내가 어젯날에 나봇의 피와 그 아들들의 피를 분명히 보았노라 또 말씀하시기를 이 토지에서 네게 갚으리라 하셨으니 그런즉 여호와의 말씀대로 그 시체를 취하여 이 밭에 던질지니라
27 Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko.
유다 왕 아하시야가 이를 보고 동산 정자 길로 도망하니 예후가 쫓아가며 이르되 저도 병거 가운데서 죽이라 하매 이블르암 가까운 구르 비탈에서 치니 저가 므깃도까지 도망하여 거기서 죽은지라
28 Antchito ake anamunyamulira mʼgaleta kupita naye ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide.
그 신복들이 저를 병거에 싣고 예루살렘에 이르러 다윗성에서 그 열조와 함께 그 묘실에 장사하니라
29 (Mʼchaka cha khumi ndi chimodzi cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya anakhala mfumu ya ku Yuda).
아합의 아들 요람의 십 일년에 아하시야가 유다 왕이 되었었더라
30 Kenaka Yehu anapita ku Yezireeli. Yezebeli atamva zimene zinachitika, anapaka zodzikometsera mʼmaso, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa zenera.
예후가 이스르엘에 이르니 이세벨이 듣고 눈을 그리고 머리를 꾸미고 창에서 바라보다가
31 Pamene Yehu ankalowa pa chipata iye anafunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere, iwe Zimuri, munthu wopha mbuye wako?”
예후가 문에 들어오매 가로되 주인을 죽인 너 시므리여 평안하냐
32 Yehu anakweza maso nayangʼana pa zenera, ndipo anafuwula kuti, “Kodi ndani ali mbali yanga? Ndani?” Anthu ofulidwa awiri kapena atatu anayangʼana Yehu pansipo.
예후가 얼굴을 들어 창을 향하고 가로되 내 편이 될 자가 누구냐 누구냐 하니 두어 내시가 예후를 내다보는지라
33 Yehu anawawuza kuti, “Muponyeni pansi!” Motero anamuponya pansi ndipo magazi ake ena anafalikira pa khoma ndi pa akavalo pamene ankamupondaponda.
가로되 저를 내려던지라 하니 내려던지매 그 피가 담과 말에게 뛰더라 예후가 그 시체를 밟으니라
34 Yehu analowa mʼnyumba yaufumu ndipo anadya ndi kumwa. Kenaka iye anati, “Kamutoleni mkazi wotembereredwayo, ndipo kamuyikeni mʼmanda, popeza ndi mwana wa mfumu.”
예후가 들어가서 먹고 마시고 가로되 가서 이 저주 받은 계집을 찾아 장사하라 저는 왕의 딸이니라 하매
35 Koma atapita kuti akamuyike mʼmanda, sanapeze kanthu kupatula chibade cha mutu wokha, mapazi ake ndi manja ake.
가서 장사하려 한즉 그 두골과 발과 손바닥 외에는 찾지 못한지라
36 Choncho iwo anabwerera kwa Yehu ndi kukamufotokozera kuti, “Mawu amene Yehova anayankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe ndi awa: Pa munda wa ku Yezireeli agalu adzadya mtembo wa Yezebeli.
돌아와서 고한대 예후가 가로되 이는 여호와께서 그 종 디셉 사람 엘리야로 말씀하신바라 이르시기를 이스르엘 토지에서 개들이 이세벨의 고기를 먹을지라
37 Mtembo wa Yezebeli udzakhala ngati zinyalala pa munda wa ku Yezireeli, kotero kuti palibe amene adzathe kunena kuti, ‘Uyu ndi Yezebeli.’”
그 시체가 이스르엘 토지에서 거름 같이 밭 면에 있으리니 이것이 이세벨이라고 가리켜 말하지 못하게 되리라 하셨느니라