< 2 Mafumu 8 >

1 Ndipo Elisa anawuza mayi amene anamuukitsira mwana wake kuti, “Choka kuno pamodzi ndi banja lako ndipo ukakhale kulikonse ukufuna, chifukwa Yehova akubweretsa njala ya zaka zisanu ndi ziwiri mʼdziko muno.”
Elisée, s’adressant à la femme dont il avait rappelé le fils à la vie, lui dit: "Lève-toi, pars avec les tiens et va séjourner où tu pourras car l’Eternel a fait appel à la famine, et déjà elle arrive dans le pays pour sévir sept années."
2 Mayiyo ananyamuka nachita zimene munthu wa Mulungu ananena. Iye pamodzi ndi banja lake anachoka nakakhala ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
La femme se leva et, se conformant à la parole de l’homme de Dieu, elle émigra avec les siens et élut domicile dans le pays des Philistins pendant sept années.
3 Zitatha zaka zisanu ndi ziwirizo anabwera kuchokera ku dziko la Afilisti ndipo anapita kwa mfumu kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake.
Au bout de ces sept années, la femme revint du pays des Philistins; elle se mit en campagne pour réclamer auprès du roi au sujet de sa maison et de son champ.
4 Ndipo mfumu inkayankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu kuti, “Tandiwuza zinthu zikuluzikulu zimene Elisa wachita.”
Or, le roi était en train de s’entretenir avec Ghéhazi, serviteur de l’homme de Dieu, et lui disait: "Fais-moi donc le récit des grandes choses accomplies par Elisée."
5 Pamene Gehazi ankayiwuza mfumuyo momwe Elisa anaukitsira anthu akufa, mayi amene mwana wake Elisa anamuukitsa kwa akufayo analowa kudzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Gehazi anati, “Mbuye wanga mfumu, mayi wake ndi uyu ndipo mwana wakeyo ndi uyu amene Elisa anamuukitsa kwa akufa.”
Tandis qu’il racontait au roi le fait de la résurrection du mort, voici que la femme dont le fils avait été rappelé à la vie vint implorer justice pour sa maison et son champ. Ghéhazi dit: "Mon seigneur le roi, tu vois là la femme en personne et son fils qu’Elisée a rendu à la vie."
6 Mfumu inafunsa mayiyo za nkhaniyi ndipo iye anayifotokozera mfumuyo. Ndipo mfumu inasankha munthu woti ayendetse nkhani yake ndipo inati, “Mubwezereni zonse zimene zinali zake, kuphatikizapo phindu lonse lochokera mʼmunda wake, kuyambira tsiku limene anachoka mpaka tsopano lino.”
Le roi interrogea la femme, qui lui raconta tout, et le roi la fit accompagner par un officier avec cette mission: "Qu’on lui restitue tout ce qui lui appartient ainsi que tous les produits donnés par son champ du jour où elle a quitté ce pays jusqu’à cette heure."
7 Elisa anapita ku Damasiko, ndipo Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu ankadwala. Mfumuyo itawuzidwa kuti, “Munthu wa Mulungu wabwera kuno kuchokera kutali,”
Elisée vint à Damas, alors que Ben-Hadad, roi de Syrie, était malade. Le roi en fut informé en ces termes: "L’Homme de Dieu est arrivé en ces lieux."
8 inawuza Hazaeli kuti, “Tenga mphatso ndipo pita ukakumane ndi munthu wa Mulungu. Ukandifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’”
Le roi dit à Hazaël: "Munis-toi d’un présent et va à la rencontre de l’homme de Dieu. Consulte l’Eternel par son entremise pour savoir si je guérirai de cette maladie."
9 Choncho Hazaeli anapita kukakumana ndi Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso za zinthu zosiyanasiyana zabwino kwambiri za ku Damasiko. Iye analowa mʼnyumba ya Elisa ndi kuyima pamaso pake, ndipo anati, “Mwana wanu Beni-Hadadi wandituma kuti ndidzakufunseni kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’”
Hazaël alla au-devant d’Elisée, emmenant avec lui un présent composé de tout ce qu’il y avait de meilleur à Damas, une charge de quarante chameaux; il s’avança, et, se présentant à lui, il dit: "Ton fils Ben-Hadad, roi de Syrie, m’a envoyé vers toi et demande: Guérirai-je de ma maladie?"
10 Elisa anayankha kuti, “Pita ndipo ukamuwuze kuti, ‘Udzachira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa kuti adzafabe.”
Elisée lui répondit: "Va lui dire: Tu guériras, mais l’Eternel m’a fait voir que sa mort est certaine."
11 Elisa anamuyangʼana kwambiri Hazaeli mpaka anachita manyazi. Pamenepo munthu wa Mulungu anayamba kulira.
Puis l’homme de Dieu leva ses regards et les tint fixés sur lui jusqu’à le rendre confus; finalement, il se mit à pleurer.
12 Hazaeli anafunsa kuti, “Mbuye wanga mukulira chifukwa chiyani?” Elisa anayankha kuti, “Chifukwa ndikudziwa choyipa chimene udzachitira Aisraeli. Udzatentha mizinda yawo ya chitetezo, udzapha anyamata awo ndi lupanga, udzaphwanyitsa pansi makanda awo ndiponso udzatumbula mimba za akazi awo oyembekezera.”
Hazaël l’interrogea: "Pourquoi, mon seigneur, pleures-tu? C’Est que je sais, répondit-il, combien tu feras de mal aux enfants d’Israël: tu livreras aux flammes leurs forteresses, tu feras périr par l’épée leurs jeunes gens, tu écraseras leurs petits enfants, et tu déchireras le sein de leurs femmes enceintes."
13 Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?” Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”
Hazaël répliqua: "Mais qu’est donc ton serviteur, ce simple chien, pour accomplir ces hauts faits? C’Est que, répondit Elisée, l’Eternel t’a montré à moi régnant sur la Syrie."
14 Choncho Hazaeli anasiyana ndi Elisa ndi kubwerera kwa mbuye wake. Beni-Hadadi atafunsa kuti, “Elisa wakuwuza chiyani?” Hazaeli anayankha kuti, “Elisa wandiwuza kuti inu mudzachira ndithu.”
Il prit congé d’Elisée et revint auprès de son maître, qui lui demanda: "Que t’a dit Elisée? Il m’a dit que tu guérirais," répondit-il.
15 Koma mmawa mwake Hazaeli anatenga nsalu yokhuthala ndi kuyiviyika mʼmadzi ndipo anaphimba nayo nkhope ya mfumu, kotero mfumuyo inafa. Hazaeli analowa ufumu mʼmalo mwake.
Le lendemain, il prit la couverture, la trempa dans l’eau et l’étendit sur la figure du roi, de sorte qu’il mourut. Hazaël s’empara de la royauté à sa place.
16 Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israeli, Yehosafati ali mfumu ya ku Yuda, Yehoramu mwana wake anakhala mfumu ya Ayuda.
La cinquième année du règne de Joram, fils d’Achab (roi d’Israël alors que Josaphat était roi de Juda), Joram, fils de Josaphat, devint roi de Juda.
17 Yehoramu analowa ufumu ali ndi zaka 32, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.
Agé de trente-deux ans à son avènement, il régna huit ans à Jérusalem.
18 Iye anatsatira khalidwe la mafumu a ku Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, popeza iye anakwatira mwana wa Ahabu. Yehoramu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
Il suivit la conduite des rois d’Israël, agissant comme la maison d’Achab; car il avait pris pour femme une fille d’Achab. Il fit donc ce qui est mal aux yeux de l’Eternel.
19 Komabe, chifukwa cha mtumiki wake Davide, Yehova sanafune kuwononga Yuda popeza Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa nyale pamodzi ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
Cependant le Seigneur, en faveur de David, son serviteur, ne voulut pas détruire Juda, fidèle à la promesse qu’il lui avait faite de lui assurer à jamais un domaine à lui et à ses descendants.
20 Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira ulamuliro wa Yuda ndipo anadzisankhira mfumu.
De son temps, Edom, faisant défection, se rendit indépendant de Juda et se donna un roi.
21 Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Ndipo iye anakantha Aedomu amene anamuzungulira pamodzi ndi oyendetsa magaleta ake usiku. Koma ankhondo ake anathawa napita ku misasa yawo.
Joram passa à Çaïr, avec toute sa cavalerie. En pleine nuit, il se leva pour attaquer les Iduméens qui le cernaient lui et les chefs de la cavalerie, mais le peuple chercha un refuge dans ses tentes.
22 Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira Yuda. Nthawi yomweyo mzinda wa Libina unawukiranso.
Edom secoua ainsi la domination de Juda jusqu’à ce jour; à la même époque, Libna se rendit également indépendante.
23 Ndipo ntchito zina za Yehoramu ndi zonse zomwe anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
Le reste de l’histoire de Joram et ses faits et gestes sont consignés dans le livre des annales des rois de Juda.
24 Choncho Yehoramu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Joram s’endormit avec ses pères, et fut enseveli à côté d’eux dans la Cité de David. Achazia, son fils, lui succéda.
25 Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israeli, Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
La douzième année du règne de Joram, fils d’Achab, roi d’Israël, Achazia, fils de Joram, devint roi de Juda.
26 Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake anali Ataliya, chidzukulu cha Omiri mfumu ya Israeli.
Achazia avait vingt-deux ans à son avènement, et il régna un an à Jérusalem. Le nom de sa mère était Athalie; elle était fille d’Omri, roi d’Israël.
27 Iye anatsatira makhalidwe a banja la Ahabu ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga linachitira banja la Ahabu, pakuti anali mkamwini wa banja la Ahabu.
Il imita la conduite de la maison d’Achab, faisant, comme elle, ce qui est mal aux yeux de l’Eternel, en digne allié de la maison d’Achab.
28 Ahaziya anapita pamodzi ndi Yoramu mwana wa Ahabu kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yoramu.
Il fit, de concert avec Joram, fils d’Achab, une expédition militaire contre Hazaël, roi de Syrie, du côté de Ramot-Galaad; las Syriens blessèrent Joram.
29 Choncho mfumu Yoramu inabwerera ku Yezireeli kuti ikachire mabala ake amene Aaramu anamuvulaza ku Rama pa nkhondo yake ndi Hazaeli mfumu ya Aramu. Tsono Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda anapita ku Yezireeli kuti akamuone Yoramu mwana wa Ahabu, popeza nʼkuti akudwala.
Alors le roi Joram s’en retourna chez lui, pour se remettre à Jezreël des blessures que lui avaient infligées les Syriens à Rama, lors de sa campagne contre Hazaël, roi de Syrie. Achazia, fils de Joram, roi de Juda, descendit pour rendre visite à Joram, fils d’Achab, à Jezreël, au cours de sa maladie.

< 2 Mafumu 8 >