< 2 Mafumu 7 >
1 Ndipo Elisa anati, “Mverani mawu a Yehova. Yehova akuti, ‘Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.’”
2 Mtsogoleri amene mfumu inkamudalira anati kwa munthu wa Mulungu, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Elisa anamuyankha kuti, “Taona, iweyo udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.”
3 Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa?
4 Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.”
5 Iwo ananyamuka ndi kachisisira kupita ku msasa wa Aaramu. Atafika mʼmalire a msasa, taonani, sanapeze munthu ndi mmodzi yemwe,
6 pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!”
7 Choncho ananyamuka nathawa ndi kachisisira ndipo anasiya matenti, akavalo ndi abulu awo. Iwo anasiya msasa wawo momwe unalili nathawa kupulumutsa miyoyo yawo.
8 Anthu akhate aja atafika mʼmalire mwa msasa analowa mʼtenti imodzi. Anadya ndi kumwa, natenga siliva, golide ndi zovala ndipo anachoka kupita kukazibisa. Atabwerera anakalowa mʼtenti ina ndipo anatenga zinthu mʼmenemo nakazibisanso.
9 Kenaka akhate aja anawuzana kuti, “Ife sitikuchita bwino. Lero ndi tsiku la uthenga wabwino ndipo tikungokhala chete. Tikadikira mpaka kucha, tidzalangidwa. Tiyeni msanga tikafotokoze zimenezi ku nyumba yaufumu.”
10 Choncho anapita nakayitana alonda a pa chipata cha mzinda ndi kufotokoza kuti, “Ife tinapita ku msasa wa Aaramu ndipo sitinapezeko munthu, kapena phokoso la wina aliyense koma tinangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire.”
11 Alonda a pa chipata aja analengeza uthengawu kwa okhala mʼnyumba yaufumu.
12 Mfumu inadzuka usiku ndipo inawuza atsogoleri ake a ankhondo kuti, “Ndikukuwuzani zimene Aaramu atichitira ife. Akudziwa kuti tikufa ndi njala; kotero achoka mu msasa wawo kukabisala kuthengo ndi kuti, ‘Iwowa atuluka ndithu, ndipo ife tidzawagwira amoyo ndi kulowa mu mzindamo.’”
13 Mmodzi mwa atsogoleri ake ankhondo anayankha kuti, “Chonde uzani anthu ena atenge akavalo asanu amene atsala mu mzinda muno. Taonani, zomwe zingawachitikire zidzakhala zofanana ndi zomwe zingachitikire ena onse amene atsala. Inde iwo adzangokhala ngati Aisraeli ena onse amene awonongeka kale. Choncho tiyeni tiwatume akafufuze zomwe zachitika.”
14 Choncho anasankha magaleta awiri pamodzi ndi akavalo ake, ndipo mfumu inawatuma kuti alondole gulu lankhondo la Aaramu. Mfumuyo inalamula oyendetsa akavalowo kuti, “Pitani kaoneni.”
15 Anthuwa anawalondola mpaka ku Yorodani, ndipo taonani, mʼnjira monse munali zovala zokhazokha ndi zinthu zimene Aaramu ankazitaya pamene ankathawa mofulumira. Ndipo amithengawo anabwerera ndi kudzafotokozera mfumu.
16 Tsono anthu a mu Samariya anatuluka nakafunkha ku msasa wa Aaramu. Kotero kuti makilogalamu atatu a ufa ankawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele ankawagulitsanso pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, monga momwe ananenera Yehova.
17 Tsono mfumu inayika mtsogoleri amene ankamudalira uja kuti akhale woyangʼanira pa chipata ndipo anthu anamupondaponda ku chipata kuja, ndipo anafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu ananenera mfumu itapita ku nyumba yake.
18 Zinachitika molingana ndi zomwe ananena munthu wa Mulungu zija kuti “Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.”
19 Mtsogoleriyu ananena kwa munthu wa Mulungu kuti, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Munthu wa Mulungu anamuyankha kuti, “Iwe udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.”
20 Ndipo izi ndi zomwe zinamuchitikiradi mtsogoleriyu, pakuti anthu anamupondaponda pa chipata ndipo anafa.