< 2 Mafumu 4 >
1 Mkazi wa mmodzi mwa ana a aneneri anafuwula kwa Elisa kuti, “Mtumiki wanu, mwamuna wanga wamwalira ndipo inu mukudziwa kuti ankaopa Yehova. Koma tsopano munthu amene mwamuna wanga anakongolako zinthu zake, akubwera kudzatenga ana anga awiri aamuna kuti akhale akapolo ake.”
Mulier autem quædam de uxoribus prophetarum clamabat ad Eliseum, dicens: Servus tuus vir meus mortuus est, et tu nosti quia servus tuus fuit timens Dominum: et ecce creditor venit ut tollat duos filios meos ad serviendum sibi.
2 Elisa anayankha mayiyo kuti, “Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?” Mayiyo anayankha kuti, “Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe.”
Cui dixit Eliseus: Quid vis ut faciam tibi? Dic mihi, quid habes in domo tua? At illa respondit: Non habeo ancilla tua quidquam in domo mea, nisi parum olei, quo ungar.
3 Elisa anati, “Pita kabwereke mitsuko yonse yopanda kanthu kwa anzako. Usakabwereke mitsuko yochepa.
Cui ait: Vade, pete mutuo ab omnibus vicinis tuis vasa vacua non pauca.
4 Kenaka ukalowe mʼnyumba mwako ndi kudzitsekera iwe ndi ana ako. Mukakatero mukakhuthulire mafuta mʼmitsuko yonseyo, ndipo mtsuko uliwonse ukadzaza muzikawuyika pambali.”
Et ingredere, et claude ostium tuum, cum intrinsecus fueris tu, et filii tui: et mitte inde in omnia vasa hæc: et cum plena fuerint, tolles.
5 Mayi uja anachoka kwa Elisa nakadzitsekera ndi ana ake. Anthu anabweretsa mitsuko kwa iye ndipo ankathiramo mafuta.
Ivit itaque mulier, et clausit ostium super se, et super filios suos: illi offerebant vasa, et illa infundebat.
6 Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, “Bweretsa mtsuko wina.” Koma iye anayankha kuti, “Mitsuko yonse yatha.” Pamenepo mafuta analeka kutuluka.
Cumque plena fuissent vasa, dixit ad filium suum: Affer mihi adhuc vas. Et ille respondit: Non habeo. Stetitque oleum.
7 Mayiyo anapita nakamuwuza munthu wa Mulungu amene anamuyankha kuti, “Pita, kagulitse mafutawo ndipo ukabweze ngongole ija. Ndalama zotsalazo zikakhale zako ndi ana ako.”
Venit autem illa, et indicavit homini Dei. Et ille, Vade, inquit, vende oleum, et redde creditori tuo: tu autem, et filii tui vivite de reliquo.
8 Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu. Kumeneko kunkakhala mayi wina wachuma amene anawumiriza Elisa kuti adye chakudya. Choncho nthawi iliyonse imene Elisa amadutsa kumeneko, ankayima ndi kudya.
Facta est autem quædam dies, et transibat Eliseus per Sunam: erat autem ibi mulier magna, quæ tenuit eum ut comederet panem: cumque frequenter inde transiret, divertebat ad eam ut comederet panem.
9 Mayiyo anawuza mwamuna wake kuti, “Taonani, ine ndikudziwa kuti munthu amene amadutsa pano nthawi zambiriyu ndi munthu woyera wa Mulungu.
Quæ dixit ad virum suum: Animadverto quod vir Dei sanctus est iste, qui transit per nos frequenter.
10 Tiyeni timumangire kachipinda kakangʼono pa denga la nyumbayi ndi kumuyikiramo bedi ndi tebulo, mpando ndi nyale. Akabwera kuno azikhala mʼmenemo.”
Faciamus ergo ei cœnaculum parvum, et ponamus ei in eo lectulum, et mensam, et sellam, et candelabrum, ut cum venerit ad nos, maneat ibi.
11 Tsiku lina pamene Elisa anafika ku Sunemu, iye anakalowa mʼchipinda chake chija nagona mʼmenemo.
Facta est ergo dies quædam, et veniens divertit in cœnaculum, et requievit ibi.
12 Iye anati kwa mtumiki wake Gehazi, “Muyitane Msunemuyu.” Ndipo anapita kukamuyitana mayiyo, ndipo anabwera nayima pamaso pa Elisa.
Dixitque ad Giezi puerum suum: Voca Sunamitidem istam. Qui cum vocasset eam, et illa stetisset coram eo,
13 Elisa anati kwa Gehazi, “Muwuze mayiyo kuti, ‘Wavutika potichitira zonsezi. Nanga tsopano ifeyo tikuchitire chiyani? Kodi ukufuna kuti tikadziwitse mfumu kapena mtsogoleri wa ankhondo zimene watichitirazi?’” Mayiyo anayankha kuti, “Ine ndimakhala mwamtendere pakati pa abale anga.”
dixit ad puerum suum: Loquere ad eam: Ecce, sedule in omnibus ministrasti nobis, quid vis ut faciam tibi? numquid habes negotium, et vis ut loquar regi, sive principi militiæ? Quæ respondit: In medio populi mei habito.
14 Elisa anafunsanso Gehazi kuti, “Kodi tingamuchitire chiyani?” Gehazi anati, “Ndithu, mayiyu alibe mwana ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.”
Et ait: Quid ergo vult ut faciam ei? Dixitque Giezi: Ne quæras: filium enim non habet, et vir eius senex est.
15 Pamenepo Elisa anati, “Muyitane.” Choncho Gehazi anamuyitana, ndipo iye anabwera nayima pa khomo.
Præcepit itaque ut vocaret eam: quæ cum vocata fuisset, et stetisset ante ostium,
16 Elisa anati kwa mayiyo, “Nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, udzakhala utanyamula mwana wamwamuna mʼmanja mwako.” Mayiyo anatsutsa zimenezi nanena kuti, “Ayi mbuye wanga. Inu munthu wa Mulungu, musanamize mdzakazi wanu!”
dixit ad eam: In tempore isto, et in hac eadem hora, si vita comes fuerit, habebis in utero filium. At illa respondit: Noli quæso, domine mi, vir Dei, noli mentiri ancillæ tuæ.
17 Koma mayi uja anakhala woyembekezera, ndipo chaka chotsatiracho, nthawi ngati yomweyo anabereka mwana wamwamuna monga momwe Elisa anamuwuzira.
Et concepit mulier, et peperit filium in tempore, et in hora eadem, qua dixerat Eliseus.
18 Mwana uja anakula, ndipo tsiku lina anapita kwa abambo ake amene anali ndi anthu odula tirigu.
Crevit autem puer. Et cum esset quædam dies, et egressus isset ad patrem suum, ad messores,
19 Mwanayo anafuwula kwa abambo ake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mayo! Mutu wanga ine!” Abambo akewo anawuza wantchito wake kuti, “Munyamule ndi kukamupereka kwa amayi ake.”
ait patri suo: Caput meum doleo, caput meum doleo. At ille dixit puero: Tolle, et duc eum ad matrem suam.
20 Wantchito uja atamunyamula ndi kumupereka kwa amayi ake. Mwanayo anakhala pa miyendo ya amayi akeyo mpaka masana, ndipo pambuyo pake anamwalira.
Qui cum tulisset, et duxisset eum ad matrem suam, posuit eum illa super genua sua usque ad meridiem, et mortuus est.
21 Mayiyo ananyamula mwanayo nakamugoneka pa bedi la munthu wa Mulungu uja. Kenaka anatseka chitseko iye nʼkuchokapo.
Ascendit autem, et collocavit eum super lectulum hominis Dei, et clausit ostium: et egressa,
22 Iye anayitanitsa mwamuna wake namuwuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi kuti ndipite mofulumira kwa munthu wa Mulungu nʼkubwererako.”
vocavit virum suum, et ait: Mitte mecum, obsecro, unum de pueris, et asinam, ut excurram usque ad hominem Dei, et revertar.
23 Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.” Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”
Qui ait illi: Quam ob causam vadis ad eum? hodie non sunt Calendæ, neque Sabbatum. Quæ respondit: Vadam:
24 Mayiyo anamangirira chishalo pa bulu ndipo anawuza wantchito wake kuti, “Yendetsa bulu mofulumira. Usachepetse liwiro pokhapokha nditakuwuza.”
Stravitque asinam, et præcepit puero: Mina, et propera, ne mihi moram facias in eundo: et hoc age quod præcipio tibi.
25 Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli. Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo!
Profecta est igitur, et venit ad virum Dei in montem Carmeli: cumque vidisset eam vir Dei econtra, ait ad Giezi puerum suum: Ecce Sunamitis illa.
26 Thamanga msanga ukakumane naye ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi muli bwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Kodi mwana wanu ali bwino?’” Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”
Vade ergo in occursum eius, et dic ei: Recte ne agitur circa te, et circa virum tuum, et circa filium tuum? Quæ respondit: Recte.
27 Atafika kwa munthu wa Mulunguyo pa phiripo, mayiyo anagwira mapazi a Elisa. Gehazi anabwera kuti amukankhe, koma munthu wa Mulungu anati, “Musiye! Iyeyu ali pa mavuto aakulu, koma Yehova wandibisira zimenezi ndipo sanandiwuze chifukwa chake.”
Cumque venisset ad virum Dei in montem, apprehendit pedes eius: et accessit Giezi ut amoveret eam. Et ait homo Dei: Dimitte illam: anima enim eius in amaritudine est, et Dominus celavit a me, et non indicavit mihi.
28 Tsono mayiyo anati, “Mbuye wanga, kodi ine ndinakupemphani mwana? Kodi sindinakuwuzeni kuti musandinamize?”
Quæ dixit illi: Numquid petivi filium a Domino meo? numquid non dixi tibi: Ne illudas me?
29 Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”
Et ille ait ad Giezi: Accinge lumbos tuos, et tolle baculum meum in manu tua, et vade. Si occurrerit tibi homo, non salutes eum: et si salutaverit te quispiam, non respondeas illi: et pones baculum meum super faciem pueri.
30 Koma mayi wake wa mwana uja anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Choncho Elisa ananyamuka natsatira mayiyo.
Porro mater pueri ait: Vivit dominus, et vivit anima tua, non dimittam te. Surrexit ergo, et secutus est eam.
31 Gehazi anatsogola nakagoneka ndodoyo pa nkhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena kugwedezeka kuonetsa kuti ali moyo. Choncho Gehazi anabwerera kukakumana ndi Elisa ndipo anamuwuza kuti, “Mwanayo sanatsitsimuke.”
Giezi autem præcesserat ante eos, et posuerat baculum super faciem pueri, et non erat vox, neque sensus: reversusque est in occursum eius, et nunciavit ei, dicens: Non surrexit puer.
32 Ndipo Elisa atafika ku nyumbako, taonani, mwanayo anali wakufa atamugoneka pa bedi lake.
Ingressus est ergo Eliseus domum, et ecce puer mortuus iacebat in lectulo eius:
33 Elisa analowa mʼnyumbamo natseka chitseko. Anali awiri okha mʼchipindamo ndipo iye anapemphera kwa Yehova.
ingressusque clausit ostium super se, et super puerum: et oravit ad Dominum.
34 Kenaka anakwera pa bedi ndi kumugonera mwanayo, pakamwa pake panakhudzana ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, ndipo manja ake anakhudzana ndi manja a mwanayo. Pamene ankadzitambalitsa yekha pa mwanayo, thupi la mwanayo linayamba kufunda.
Et ascendit, et incubuit super puerum: posuitque os suum super os eius, et oculos suos super oculos eius, et manus suas super manus eius: et incurvavit se super eum, et calefacta est caro pueri.
35 Elisa anatembenuka nayenda uku ndi uku kamodzi mʼchipindamo ndipo kenaka anakweranso pa bedi nagoneranso mwanayo. Mwanayo anayetsemula kasanu ndi kawiri ndipo anatsekula maso ake.
At ille reversus, deambulavit in domo, semel huc atque illuc: et ascendit, et incubuit super eum: et oscitavit puer septies, aperuitque oculos.
36 Elisa anayitana Gehazi ndipo anati, “Muyitane Msunemuyo.” Ndipo anaterodi. Mayiyo atabwera, Elisa anati, “Tenga mwana wako.”
At ille vocavit Giezi, et dixit ei: Voca Sunamitidem hanc. Quæ vocata, ingressa est ad eum. Qui ait: Tolle filium tuum.
37 Mayiyo analowa, nagwada pa mapazi a Elisa, naweramitsa mutu wake pansi. Kenaka ananyamula mwana wake natuluka.
Venit illa, et corruit ad pedes eius, et adoravit super terram: tulitque filium suum, et egressa est,
38 Elisa anabwerera ku Giligala ndipo ku dera limenelo kunali njala. Elisa akukumana ndi ana a aneneri, anati kwa mtumiki wake, “Ika mʼphika waukulu pa moto ndipo uwaphikire chakudya anthu awa.”
et Eliseus reversus est in Galgala. Erat autem fames in terra, et filii prophetarum habitabant coram eo. dixitque uni de pueris suis: Pone ollam grandem, et coque pulmentum filiis prophetarum.
39 Mmodzi mwa ana aneneriwo anapita kuthengo kukafuna ndiwo ndipo anakapeza mpesa wakuthengo. Iye anathyolako zipatso zake nadzaza nsalu yake. Atabwerera, anazidula zipatsozo naziyika mu mʼphika, ngakhale kuti panalibe amene ankazidziwa.
Et egressus est unus in agrum ut colligeret herbas agrestes: invenitque quasi vitem silvestrem, et collegit ex ea colocynthidas agri, et implevit pallium suum, et reversus concidit in ollam pulmenti: nesciebat enim quid esset.
40 Anawapakulira anthu chakudyacho, koma atayamba kudya, anthuwo anafuwula kuti, “Inu munthu wa Mulungu muli imfa mu mʼphikamu!” Ndipo sakanatha kudya chakudyacho.
Infuderunt ergo sociis, ut comederent: cumque gustassent de coctione, clamaverunt, dicentes: Mors in olla vir Dei. Et non potuerunt comedere.
41 Elisa anati, “Bweretsani ufa.” Iye anathira ufa mu mʼphikamo ndipo anati, “Perekani chakudyachi kwa anthu kuti adye.” Ndipo mu mʼphikamo munalibenso zoopsa.
At ille, Afferte, inquit, farinam. Cumque tulissent, misit in ollam, et ait: Infunde turbæ, ut comedant. Et non fuit amplius quidquam amaritudinis in olla.
42 Munthu wina wochokera ku Baala-Salisa anabwera atamutengera munthu wa Mulungu malofu a barele makumi awiri opangidwa kuchokera ku zokolola zoyamba kucha, pamodzinso ndi ngala zatsopano za tirigu. Elisa anati kwa munthuyo, “Apatse anthu kuti adye.”
Vir autem quidam venit de Baalsalisa deferens viro Dei panes primitiarum, viginti panes hordeaceos, et frumentum novum in pera sua. At ille dixit: Da populo, ut comedat.
43 Mtumiki wake anafunsa kuti, “Kodi ndikachigawe motani chakudyachi kwa anthu 100?” Koma Elisa anamuwuzanso kuti, “Apatse anthu adye. Pakuti izi ndi zimene Yehova akunena kuti, ‘Iwo adzadya chakudyachi ndipo china chidzatsalako.’”
Responditque ei minister eius: Quantum est hoc, ut apponam centum viris? Rursum ille ait: Da populo, ut comedat: hæc enim dicit Dominus: Comedent, et supererit.
44 Tsono iye anachipereka kwa anthuwo ndipo anadya china nʼkutsalako, molingana ndi mawu a Yehova.
Posuit itaque coram eis: qui comederunt, et superfuit iuxta verbum Domini.