< 2 Mafumu 24 >
1 Pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anadzathira nkhondo dzikolo ndipo Yehoyakimu anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zitatu. Koma kenaka anasintha maganizo ake nawukira Nebukadinezara.
2 Yehova anatumiza magulu a Ababuloni, Aaramu, Amowabu ndi Aamoni, kudzathira nkhondo Yuda. Iye anawatumiza kudzawononga Yuda molingana ndi mawu amene Yehova ananeneratu kudzera mwa aneneri ake.
3 Ndithu, izi zinachitikira Yuda monga momwe Yehova analamulira nʼcholinga choti awachotse pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase ndi zonse zimene anachita,
4 kuphatikizapo kukhetsa magazi a anthu osalakwa. Chifukwa iye anadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osalakwa ndipo Yehova sanafune kumukhululukira.
5 Ntchito zina za Yehoyakimu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
6 Yehoyakimu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
7 Mfumu ya Igupto sinatulukenso mʼdziko lake chifukwa mfumu ya Babuloni inalanda mayiko onse kuchokera ku Mtsinje wa ku Igupto mpaka ku Mtsinje wa Yufurate.
8 Yehoyakini anakhala mfumu ali ndi zaka 18 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.
9 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira abambo ake.
10 Nthawi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ku Yerusalemu nazinga mzindawo ndi misasa ya nkhondo
11 ndipo Nebukadinezara anafika ku mzindawo pamene ankhondo ake anawuzinga.
12 Yehoyakini mfumu ya Yuda pamodzi ndi amayi ake, atumiki ake, anthu ake olemekezeka ndiponso akuluakulu onse anadzipereka kwa mfumu ya ku Babuloni. Mfumu ya Babuloni inagwira Yoyakini ukapolo mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.
13 Monga ananenera Yehova, Nebukadinezara anachotsa chuma chonse cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso cha mʼnyumba ya mfumu ndipo anatenga ziwiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Yehova zimene Solomoni mfumu ya Israeli anapanga.
14 Anatenga anthu onse a mu Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo. Akuluakulu onse pamodzi ndi anthu ankhondo, anthu onse aluso ndi amisiri osula onse pamodzi analipo 10,000. Osauka okha ndiye anatsala mʼdzikomo.
15 Nebukadinezara anatenga Yehoyakini ngati kapolo kupita naye ku Babuloni. Mu Yerusalemu anatenganso amayi a mfumu, akazi ake, akuluakulu ake ndiponso anthu olemekezeka mʼdzikomo.
16 Mfumu ya Babuloni inatumizanso ku Babuloni anthu ankhondo 70,000, anthu amphamvu ndi okonzeka kupita ku nkhondo, anthu aluso ndi amisiri osula 1,000.
17 Iye analonga ufumu Mataniya, malume wa Yoyakini mʼmalo mwake ndipo anasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya.
18 Zedekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 21 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
19 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Yehoyakimu.
20 Zonsezi zinachitikira Yerusalemu ndi Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Mulungu ndipo pa mapeto pake anawachotsa pamaso pake. Ndipo Zedekiya anawukira mfumu ya Babuloni.