< 2 Mafumu 20 >

1 Masiku amenewo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti: Konza nyumba yako chifukwa umwalira ndipo suchira.”
Naqueles dias caiu Ezequias enfermo de morte, e veio a ele Isaías profeta filho de Amoz, e disse-lhe: o SENHOR disse assim: Dá ordens à tua casa, porque hás de morrer, e não viverás.
2 Hezekiya anatembenuka nayangʼana ku khoma ndipo anapemphera kwa Yehova kuti,
Então virou ele seu rosto à parede, e orou ao SENHOR, e disse:
3 “Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri.
Rogo-te, ó SENHOR, rogo-te faças memória de que andei diante de ti em verdade e íntegro coração, e que fiz as coisas que te agradam. E chorou Ezequias com grande choro.
4 Yesaya asanatuluke mʼbwalo lapakati, Yehova anayankhula kuti,
E antes que Isaías saísse até a metade do pátio, veio a palavra do SENHOR a Isaías, dizendo:
5 “Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova.
Volta, e dize a Ezequias, príncipe de meu povo: Assim diz o SENHOR, o Deus de Davi teu pai: Eu ouvi tua oração, e vi tuas lágrimas: eis que eu te saro; ao terceiro dia subirás à casa do SENHOR.
6 Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’”
E acrescentarei a teus dias quinze anos, e te livrarei a ti e a esta cidade da mão do rei da Assíria; e ampararei esta cidade por causa de mim, e por causa de Davi meu servo.
7 Pamenepo Yesaya anati, “Konzani phala lankhuyu.” Iwo anakonza phalalo nalipaka pa chithupsacho ndipo Hezekiya anachira.
E disse Isaías: Tomai uma pasta de figos. E tomando-a, puseram sobre a chaga, e sanou.
8 Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?”
E Ezequias havia dito a Isaías: Que sinal terei de que o SENHOR me sarará, e que subirei à casa do SENHOR ao terceiro dia?
9 Yesaya anayankha kuti, “Chizindikiro cha Yehova chosonyeza kuti Iye adzachita chimene walonjeza ndi ichi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?”
E respondeu Isaías: Esta sinal terás do SENHOR, de que fará o SENHOR isto que disse: Avançará a sombra dez degraus, ou retrocederá dez degraus?
10 Hezekiya anati, “Nʼchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, kulekana nʼkuti chithunzithunzicho chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi.”
E Ezequias respondeu: Fácil coisa é que a sombra decline dez degraus: mas, que a sombra volte atrás dez degraus.
11 Pamenepo mneneri Yesaya anapemphera kwa Yehova ndipo Yehova anachititsa kuti chithunzithunzi chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi anamanga.
Então o profeta Isaías clamou ao SENHOR; e fez voltar a sombra pelos degraus que havia descido no relógio de Acaz, dez degraus atrás.
12 Pa nthawi imeneyo Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babuloni anatumiza amithenga kwa Hezekiya kukapereka makalata ndi mphatso, chifukwa nʼkuti atamva za kudwala kwa Hezekiyayo.
Naquele tempo Berodaque-Baladã, filho de Baladã, rei da Babilônia, enviou cartas e um presente a Ezequias, porque havia ouvido que Ezequias havia estado doente.
13 Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse.
E Ezequias os ouviu, e mostrou-lhes toda a casa das coisas preciosas, prata, ouro, e especiaria, e preciosos unguentos; e a casa de suas armas, e tudo o que havia em seus tesouros: nenhuma coisa restou que Ezequias não lhes mostrasse, tanto em sua casa como em todo o seu domínio.
14 Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
Então o profeta Isaías veio ao rei Ezequias, e disse-lhe: Que disseram aqueles homens, e de onde vieram a ti? E Ezequias lhe respondeu: De distantes terras vieram, de Babilônia.
15 Mneneriyo anafunsa kuti, “Kodi anaona chiyani mʼnyumba yanu yaufumu?” Hezekiya anayankha kuti, “Anaona china chilichonse mʼnyumba yanga yaufumu ndipo palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindinawaonetse mʼnyumba zanga zosungiramo chuma.”
E ele lhe voltou a dizer: Que viram em tua casa? E Ezequias respondeu: Viram tudo o que havia em minha casa; nada restou em meus tesouros que não lhes mostrasse.
16 Pamenepo Yesaya anawuza Hezekiya kuti, “Imvani zimene Yehova akunena:
Então Isaías disse a Ezequias: Ouve a palavra do SENHOR:
17 Taonani, masiku akubwera ndithu pamene zonse za mʼnyumba yanu yaufumu, zonse zimene makolo anu anazisunga mpaka lero, zidzatengedwa kupita ku Babuloni. Palibe chimene chidzatsale, akutero Yehova.
Eis que vêm dias, em que tudo o que está em tua casa, e tudo o que teus pais entesouraram até hoje, será levado a Babilônia, sem restar nada, disse o SENHOR.
18 Ndipo ena mwa ana anu omwe, amene mudzabereke adzatengedwa ndipo adzawasandutsa anthu ofulidwa mʼnyumba yaufumu ya mfumu ya Babuloni.”
E de teus filhos que sairão de ti, que haverás gerado, tomarão; e serão eunucos no palácio do rei da Babilônia.
19 Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhulawa ndi abwino. Pakuti iye ankaganiza kuti, ‘Kodi pa nthawi yanga sipadzakhala mtendere ndi bata?’”
Então Ezequias disse a Isaías: A palavra do SENHOR que falaste, é boa. Depois disse: Mas não haverá paz e verdade em meus dias?
20 Ntchito zina za Hezekiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
Os demais dos feitos de Ezequias, e todo o seu vigor, e como fez o tanque, e o aqueduto, e meteu as águas na cidade, não está escrito no livro das crônicas dos reis de Judá?
21 Hezekiya anamwalira nagona pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
E descansou Ezequias com seus pais, e reinou em seu lugar Manassés seu filho.

< 2 Mafumu 20 >