< 2 Mafumu 19 >

1 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova.
ויהי כשמע המלך חזקיהו ויקרע את בגדיו ויתכס בשק ויבא בית יהוה
2 Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi.
וישלח את אליקים אשר על הבית ושבנא הספר ואת זקני הכהנים מתכסים בשקים--אל ישעיהו הנביא בן אמוץ
3 Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.
ויאמרו אליו כה אמר חזקיהו יום צרה ותוכחה ונאצה היום הזה כי באו בנים עד משבר וכח אין ללדה
4 Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’”
אולי ישמע יהוה אלהיך את כל דברי רבשקה אשר שלחו מלך אשור אדניו לחרף אלהים חי והוכיח בדברים אשר שמע יהוה אלהיך ונשאת תפלה בעד השארית הנמצאה
5 Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya,
ויבאו עבדי המלך חזקיהו--אל ישעיהו
6 Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine.
ויאמר להם ישעיהו כה תאמרון אל אדניכם כה אמר יהוה אל תירא מפני הדברים אשר שמעת אשר גדפו נערי מלך אשור אתי
7 Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’”
הנני נתן בו רוח ושמע שמועה ושב לארצו והפלתיו בחרב בארצו
8 Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
וישב רבשקה וימצא את מלך אשור נלחם על לבנה כי שמע כי נסע מלכיש
9 Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa:
וישמע אל תרהקה מלך כוש לאמר הנה יצא להלחם אתך וישב וישלח מלאכים אל חזקיהו לאמר
10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’
כה תאמרון אל חזקיהו מלך יהודה לאמר אל ישאך אלהיך אשר אתה בטח בו לאמר לא תנתן ירושלם ביד מלך אשור
11 Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka?
הנה אתה שמעת את אשר עשו מלכי אשור לכל הארצות--להחרימם ואתה תנצל
12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa?
ההצילו אתם אלהי הגוים אשר שחתו אבותי את גוזן ואת חרן ורצף ובני עדן אשר בתלאשר
13 Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”
איו מלך חמת ומלך ארפד ומלך לעיר ספרוים הנע ועוה
14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova.
ויקח חזקיהו את הספרים מיד המלאכים ויקראם ויעל בית יהוה ויפרשהו חזקיהו לפני יהוה
15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
ויתפלל חזקיהו לפני יהוה ויאמר יהוה אלהי ישראל ישב הכרבים אתה הוא האלהים לבדך לכל ממלכות הארץ אתה עשית את השמים ואת הארץ
16 Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.
הטה יהוה אזנך ושמע פקח יהוה עיניך וראה ושמע את דברי סנחריב אשר שלחו לחרף אלהים חי
17 “Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo.
אמנם יהוה החריבו מלכי אשור את הגוים--ואת ארצם
18 Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu.
ונתנו את אלהיהם באש כי לא אלהים המה כי אם מעשה ידי אדם עץ ואבן--ויאבדום
19 Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”
ועתה יהוה אלהינו הושיענו נא מידו וידעו כל ממלכות הארץ כי אתה יהוה אלהים לבדך
20 Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’”
וישלח ישעיהו בן אמוץ אל חזקיהו לאמר כה אמר יהוה אלהי ישראל אשר התפללת אלי אל סנחרב מלך אשור שמעתי
21 Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa: “Namwali wa Ziyoni akukunyoza ndi kukuseka iwe. Mwana wamkazi wa Yerusalemu akupukusa mutu wake kumbuyo kwako.
זה הדבר אשר דבר יהוה עליו בזה לך לעגה לך בתולת בת ציון--אחריך ראש הניעה בת ירושלם
22 Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani? Kodi ndani amene wamufuwulira mawu ako ndi kumuyangʼana monyada? Wachitiratu izi Woyera wa Israeli!
את מי חרפת וגדפת ועל מי הרימות קול ותשא מרום עיניך על קדוש ישראל
23 Kudzera mwa amithenga ako wonyoza Ambuye. Ndipo wanena kuti, ‘Ndi magaleta ochuluka ndinakwera mapiri ataliatali, pa msonga za mapiri a Lebanoni. Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri, mitengo yake ya payini yabwino kwambiri. Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni, mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.
ביד מלאכיך חרפת אדני ותאמר ברכב (ברב) רכבי אני עליתי מרום הרים ירכתי לבנון ואכרת קומת ארזיו מבחור ברשיו ואבואה מלון קצה יער כרמלו
24 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo ndipo ndinamwa madzi a kumeneko. Ndi mapazi anga ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’”
אני קרתי ושתיתי מים זרים ואחרב בכף פעמי כל יארי מצור
25 “‘Kodi sunamvepo? Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale. Ndinazikonzeratu masiku amakedzana; tsopano ndachita kuti zichitikedi, iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa kukhala milu ya miyala.
הלא שמעת למרחוק אתה עשיתי למימי קדם ויצרתיה עתה הביאתיה--ותהי להשות גלים נצים ערים בצרות
26 Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu, athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi. Ali ngati mbewu za mʼmunda, ngati udzu wanthete, ali ngati udzu womera pa denga, umene umawuma usanakule nʼkomwe.’”
וישביהן קצרי יד--חתו ויבשו היו עשב שדה וירק דשא חציר גגות ושדפה לפני קמה
27 “‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako, kutuluka kwako ndi kulowa kwako, ndi mkwiyo wako pa Ine.
ושבתך וצאתך ובאך ידעתי ואת התרגזך אלי
28 Chifukwa chakuti wandikwiyira ndipo ndamva za mwano wako, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako, ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa njira yomwe unadzera pobwera.’
יען התרגזך אלי ושאננך עלה באזני--ושמתי חחי באפך ומתגי בשפתיך והשבתיך בדרך אשר באת בה
29 “Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi: “Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa, ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera. Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola, mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.
וזה לך האות--אכול השנה ספיח ובשנה השנית סחיש ובשנה השלישית זרעו וקצרו ונטעו כרמים--ואכלו פרים
30 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsale adzazika mizu ndi kubereka zipatso.
ויספה פליטת בית יהודה הנשארה--שרש למטה ועשה פרי למעלה
31 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala, ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.” “Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.
כי מירושלם תצא שארית ופליטה מהר ציון קנאת יהוה (צבאות) תעשה זאת
32 “Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi: “‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu kapena kuponyamo muvi. Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.
לכן כה אמר יהוה אל מלך אשור לא יבא אל העיר הזאת ולא יורה שם חץ ולא יקדמנה מגן ולא ישפך עליה סללה
33 Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera; sadzalowa mu mzinda umenewu, akutero Yehova.
בדרך אשר יבא בה ישוב ואל העיר הזאת לא יבא נאם יהוה
34 Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’”
וגנותי אל העיר הזאת להושיעה--למעני ולמען דוד עבדי
35 Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda!
ויהי בלילה ההוא ויצא מלאך יהוה ויך במחנה אשור מאה שמונים וחמשה אלף וישכימו בבקר והנה כלם פגרים מתים
36 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko.
ויסע וילך וישב סנחריב מלך אשור וישב בנינוה
37 Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
ויהי הוא משתחוה בית נסרך אלהיו ואדרמלך ושראצר (בניו) הכהו בחרב והמה נמלטו ארץ אררט וימלך אסר חדן בנו תחתיו

< 2 Mafumu 19 >