< 2 Mafumu 16 >
1 Mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
2 Ahazi anakhala mfumu ali ndi zaka makumi awiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zabwino pamaso pa Yehova Mulungu wake monga momwe Davide kholo lake ankachitira.
3 Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Israeli mpaka kupereka mwana wake wamwamuna pa moto ngati nsembe yopsereza, potsatira zonyansa za anthu a mitundu imene Yehova anayipirikitsa mʼdzikomo Aisraeli asanafike.
4 Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzera mafano, pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
5 Ndipo Rezini mfumu ya Aramu ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli anapita kukachita naye nkhondo ku Yerusalemu ndipo anazinga Ahazi, koma sanathe kumugonjetsa.
6 Nthawi imeneyo Rezini mfumu ya Aramu anatenganso Elati ndi kumubwezera kwa Aaramu, nathamangitsa anthu a ku Yuda mu Elatimo. Aedomu anapita kukakhala ku Elati ndipo akukhalako mpaka lero lino.
7 Ahazi anatuma amithenga kwa Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya kuti, “Ine ndine mtumiki wanu ndipo ndili pansi panu. Bwerani mudzandipulumutse mʼdzanja la mfumu ya Aramu ndiponso mʼdzanja la mfumu ya Israeli amene akundithira nkhondo.”
8 Ndipo Ahazi anatenga siliva ndi golide amene anamupeza mʼNyumba ya Yehova ndi mosungira chuma cha nyumba ya mfumu ndi kutumiza ngati mphatso kwa mfumu ya ku Asiriya.
9 Mfumu ya ku Asiriya inamvera pokathira nkhondo mzinda wa Damasiko ndi kuwulanda. Anthu a mu mzindamo anawatumiza ku Kiri ndipo anapha Rezini.
10 Kenaka mfumu Ahazi inapita ku Damasiko kukakumana ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya. Iye anaona guwa lansembe ku Damasiko kuja ndipo anatumiza chitsanzo chake kwa wansembe Uriya, osasiyapo nʼkanthu komwe kuti athe kulimanga.
11 Choncho wansembe Uriya anamanga guwa lansembe molingana ndi chitsanzo chimene anamutumizira Mfumu Ahazi kuchokera ku Damasiko ndipo anatsiriza kumanga guwalo Ahazi asabwere kuchokera ku Damasiko kuja.
12 Mfumu itabwera kuchokera ku Damasiko kuja ndi kuona guwalo, inasendera pafupi ndi kupereka nsembe paguwapo.
13 Mfumu inapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya chakudya. Inapereka nsembe yachakumwa ndi kuwaza magazi a nsembe yake yachiyanjano paguwapo.
14 Guwa lamkuwa limene linali pamaso pa Yehova analichotsa kutsogolo kwa nyumbayo, kulichotsa pakati pa guwa latsopano ndi Nyumba ya Yehova ndi kukaliyika cha kumpoto kwa guwa latsopanolo.
15 Pamenepo Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uriya kuti, “Pa guwa lalikulu latsopano uziperekapo nsembe yopsereza ya mmawa ndi nsembe ya chakudya ya madzulo, nsembe yopsereza ya mfumu ndi nsembe yake ya chakudya ndiponso nsembe za anthu onse a mʼdziko, za chakudya ndi chakumwa. Pa guwali uziwazapo magazi a nsembe zonse zopsereza ndi nsembe zina zonse. Koma ine ndizigwiritsa ntchito guwa lansembe lamkuwa pofuna kufunsira nzeru.”
16 Ndipo wansembe Uriya anachita monga analamulira Mfumu Ahazi.
17 Mfumu Ahazi anachotsa maferemu a maphaka nachotsapo mabeseni. Iye anatsitsa mbiya yayikulu imene inali pamwamba pa ngʼombe zamkuwa ndipo anayika pansi pa chiwundo cha miyala.
18 Iye anachotsa kadenga ka pa Sabata kamene kanamangidwa mʼkati mwa Nyumba ya Yehova ndiponso anatseka chipata cholowera mfumu cha kunja kwa nyumba ya Yehova pofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya.
19 Ntchito zina za Ahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
20 Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.