< 2 Mafumu 11 >

1 Ataliya amayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakawononga banja lonse la mfumu.
Athalia vero mater Ochoziae, videns mortuum filium suum, surrexit, et interfecit omne semen regium.
2 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe.
Tollens autem Iosaba filia regis Ioram, soror Ochoziae, Ioas filium Ochoziae, furata est eum de medio filiorum regis, qui interficiebantur, et nutricem eius de triclinio: et abscondit eum a facie Athaliae ut non interficeretur.
3 Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
Eratque cum ea sex annis clam in domo Domini: porro Athalia regnavit super terram.
4 Koma mʼchaka chachisanu ndi chiwiri, Yehoyada anatumiza mawu kukayitana atsogoleri olamulira asilikali 100 olondera mfumu ndiponso alonda olonda nyumba yaufumu ndipo anabwera nawo mʼNyumba ya Yehova. Iye anapangana nawo pangano ndipo anawalumbiritsa mʼnyumba ya Yehova. Kenaka anawaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja.
Anno autem septimo misit Ioiada, et assumens centuriones, et milites introduxit ad se in templum Domini, pepigitque cum eis foedus: et adiurans eos in domo Domini, ostendit eis filium regis:
5 Yehoyada anawalamulira kuti, “Chimene muti muchite ndi ichi: Inu magulu atatu amene muti mudzakhale pa ntchito tsiku la Sabata, gulu loyamba lidzalondera nyumba ya mfumu,
et praecepit illis, dicens: Iste est sermo, quem facere debetis:
6 gulu lachiwiri lidzalondera Chipata cha Suri, ndipo gulu lachitatu lidzalondera chipata cha kumbuyo kwa asilikali amene amasinthana polondera nyumbayo.
Tertia pars vestrum introeat sabbato, et observet excubias domus regis. Tertia autem pars sit ad portam Seir, et tertia pars sit ad portam, quae est post habitaculum scutariorum: et custodietis excubias domus Messa.
7 Ndipo inu amene muli mʼmagulu ena awiri amene simugwira ntchito pa tsiku la Sabata, nonse mudzalondere mfumu ku nyumbayo.
Duae vero partes e vobis, omnes egredientes sabbato, custodiant excubias domus Domini circa regem.
8 Mudzakhale mozungulira mfumuyo, munthu aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake. Wina aliyense amene adzakuyandikireni adzayenera kuphedwa. Muzikhala pafupi ndi mfumu kulikonse kumene ikupita.”
Et vallabitis eum, habentes arma in manibus vestris: si quis autem ingressus fuerit septum templi, interficiatur: eritisque cum rege introeunte et egrediente.
9 Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada.
Et fecerunt centuriones iuxta omnia, quae praeceperat eis Ioiada sacerdos: et assumentes singuli viros suos, qui ingrediebantur sabbato, cum his qui egrediebantur sabbato, venerunt ad Ioiadam sacerdotem.
10 Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova.
Qui dedit eis hastas, et arma regis David, quae erant in domo Domini.
11 Alondawo, aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake, anayima mozungulira mfumu, pafupi ndi guwa lansembe ndi nyumbayo, kuchokera mbali ya kummwera mpaka mbali ya kumpoto kwa nyumbayo.
Et steterunt singuli habentes arma in manu sua a parte templi dextera, usque ad partem sinistram altaris, et aedis, circum regem.
12 Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumuyo namuveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano ndi kumuyika kukhala mfumu. Iwo anamudzoza ndipo anthu anamuwombera mʼmanja akufuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
Produxitque filium regis, et posuit super eum diadema, et testimonium: feceruntque eum regem, et unxerunt: et plaudentes manu, dixerunt: Vivat rex.
13 Ataliya atamva phokoso limene alonda ndi anthuwo amachita, anapita ku Nyumba ya Yehova kumene kunali anthuwo.
Audivit autem Athalia vocem populi currentis: et ingressa ad turbas in templum Domini,
14 Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
vidit regem stantem super tribunal iuxta morem, et cantores, et tubas prope eum, omnemque populum terrae laetantem, et canentem tubis: et scidit vestimenta sua, clamavitque: Coniuratio, coniuratio.
15 Wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a asilikali 100 amene amayangʼanira asilikaliwo kuti, “Mutulutseni ameneyo pakati panu ndipo muphe ndi lupanga aliyense amene adzamutsata.” Pakuti nʼkuti wansembeyo atanena kuti, “Ataliyayo asaphedwere mʼNyumba ya Yehova.”
Praecepit autem Ioiada centurionibus, qui erant super exercitum, et ait eis: Educite eam extra septa templi, et quicumque eam secutus fuerit, feriatur gladio. Dixerat enim sacerdos: Non occidatur in templo Domini.
16 Choncho anamugwira pamene amafika pa malo amene akavalo amalowera ku nyumba ya mfumu ndipo anamuphera pamenepo.
Imposueruntque ei manus, et impegerunt eam per viam introitus equorum, iuxta palatium, et interfecta est ibi.
17 Tsono Yehoyada anachititsa pangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu kuti adzakhala anthu a Yehova. Iye anachititsanso pangano pakati pa mfumu ndi anthu.
Pepigit ergo Ioiada foedus inter Dominum et populum, et inter regem, et inter populum, ut esset populus Domini, et inter regem et populum.
18 Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova.
Ingressusque est omnis populus terrae templum Baal, et destruxerunt aras eius, et imagines contriverunt valide: Mathan quoque sacerdotem Baal occiderunt coram altari. Et posuit sacerdos custodias in domo Domini.
19 Iye anatenga atsogoleri a asilikali 100 aja, alonda olonda nyumba yaufumu pamodzi ndi anthu onse a mʼdzikomo ndipo onse pamodzi anayitulutsa mfumu mʼNyumba ya Yehova ndi kukalowa ku nyumba yaufumu podzera pa chipata cha alonda. Ndipo mfumuyo inakhala pa mpando wake waufumu.
Tulitque centuriones, et Cerethi et Phelethi legiones, et omnem populum terrae, deduxeruntque regem de domo Domini: et venerunt per viam portae scutariorum in palatium, et sedit super thronum regum.
20 Choncho anthu onse a mʼdzikomo anasangalala. Ndipo mu mzindamo munakhala bata chifukwa Ataliya nʼkuti ataphedwa ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.
Laetatusque est omnis populus terrae, et civitas conquievit: Athalia autem occisa est gladio in domo regis.
21 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anayamba kulamulira.
Septemque annorum erat Ioas, cum regnare coepisset.

< 2 Mafumu 11 >