< 2 Yohane 1 >

1 Ndine mkulu wampingo, kulembera: Mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndi kwa ana ake amene ndimawakonda mʼchoonadi. Ndipo sindine ndekha amene ndimawakonda, komanso onse odziwa choonadi.
The elder unto the elect lady and her children, whom I love in truth; and not I only, but also all they that know the truth;
2 Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chimakhala mwa ife ndipo chidzakhala mwa ife mpaka muyaya. (aiōn g165)
for the truth’s sake which abideth in us, and it shall be with us for ever: (aiōn g165)
3 Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.
Grace, mercy, peace shall be with us, from God the Father, and from Jesus Christ, the Son of the Father, in truth and love.
4 Ndinakondwera kwambiri nditapeza ana anu ena akuyenda mʼchoonadi, monga Atate anatilamulira.
I rejoice greatly that I have found [certain] of thy children walking in truth, even as we received commandment from the Father.
5 Ndipo tsopano, amayi wokondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lomwe lija takhala nalo kuyambira pachiyambi. Ine ndikukupemphani kuti tidzikondana wina ndi mnzake.
And now I beseech thee, lady, not as though I wrote to thee a new commandment, but that which we had from the beginning, that we love one another.
6 Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.
And this is love, that we should walk after his commandments. This is the commandment, even as ye heard from the beginning, that ye should walk in it.
7 Ndikunena zimenezi chifukwa anthu ambiri onyenga, amene savomereza kuti Yesu Khristu anabwera monga munthu, akuyenda mʼdziko lapansi. Munthu aliyense otere ndi wonyenga ndiponso wokana Khristu.
For many deceivers are gone forth into the world, [even] they that confess not that Jesus Christ cometh in the flesh. This is the deceiver and the antichrist.
8 Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma chitani khama kuti mukalandire mphotho yanu yonse.
Look to yourselves, that ye lose not the things which we have wrought, but that ye receive a full reward.
9 Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana.
Whosoever goeth onward and abideth not in the teaching of Christ, hath not God: he that abideth in the teaching, the same hath both the Father and the Son.
10 Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni.
If any one cometh unto you, and bringeth not this teaching, receive him not into [your] house, and give him no greeting:
11 Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.
for he that giveth him greeting partaketh in his evil works.
12 Ndili nazo zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata. Mʼmalo mwake, ndikuyembekeza kufika kwanuko kuti tidzakambirane nanu pamaso ndi pamaso, potero chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.
Having many things to write unto you, I would not [write them] with paper and ink: but I hope to come unto you, and to speak face to face, that your joy may be fulfilled.
13 Ana a mlongo wanu wosankhidwa ndi Mulungu akupereka moni.
The children of thine elect sister salute thee.

< 2 Yohane 1 >