< 2 Akorinto 1 >
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi mʼbale wathu Timoteyo, Kulembera mpingo wa Mulungu mu Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse mu Akaya monse.
Paul, apôtre de Jésus-Christ, par la volonté de Dieu, et Timothée, son frère, à l’Eglise de Dieu qui est à Corinthe, et à tous les saints qui sont dans toute l’Achaïe.
2 Mukhale ndi chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
Grâce à vous, et paix par Dieu notre Père, et par Notre Seigneur Jésus-Christ.
3 Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse.
Béni le Dieu et Père de Notre Seigneur Jésus-Christ, le Père des miséricordes et le Dieu de toute consolation!
4 Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.
Qui nous console dans toutes nos afflictions, afin que nous puissions nous-mêmes, par l’encouragement que Dieu nous donne, consoler aussi ceux qui sont sous le poids de toute sorte de maux.
5 Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri.
Car, comme les souffrances du Christ abondent en nous, c’est aussi par le Christ que notre consolation abonde.
6 Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife.
Or si nous sommes dans l’affliction, c’est pour votre encouragement et votre salut; si nous sommes consolés, c’est pour votre consolation; si nous sommes encouragés, c’est pour votre encouragement et votre salut qui s’accomplit par votre patience à supporter les mêmes souffrances que nous supportons nous-mêmes.
7 Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi.
Ce qui nous donne une ferme espérance pour vous, sachant que, comme vous avez part aux souffrances, vous l’aurez aussi à la consolation.
8 Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo.
Car nous ne voulons pas, mes frères, que vous ignoriez, touchant la tribulation qui nous est survenue en Asie, que le poids en a été excessif et au-dessus de nos forces, au point que nous étions las de vivre.
9 Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa.
Mais nous, nous avons reçu en nous-mêmes l’arrêt de la mort, afin que nous ne mettions pas notre confiance en nous, mais en Dieu qui ressuscite les morts,
10 Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe.
Qui nous a délivrés de si grands périls, qui nous en délivre, et qui, comme nous l’espérons de lui, nous en délivrera encore,
11 Mutithandize potipempherera. Pamenepo ambiri adzathokoza mʼmalo mwathu, chifukwa cha chisomo chake poyankha mapemphero a anthu ambiri.
Surtout vous nous aidant en priant pour nous, afin que, comme le don qui est en nous a été fait en considération d’un grand nombre, un grand nombre en rende grâces pour nous.
12 Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu.
Car notre gloire, la voici: Le témoignage de notre conscience, que c’est dans la simplicité du cœur et dans la sincérité de Dieu, et non point selon la sagesse de la chair, mais avec la grâce de Dieu, que nous nous sommes conduits dans ce monde, mais plus particulièrement envers vous.
13 Pakuti sitikukulemberani zoti simungawerenge kapena kumvetsetsa.
En effet, nous ne vous écrivons que les choses que vous avez lues et reconnues. Or j’espère que vous reconnaîtrez jusqu’à la fin,
14 Monga mwamva pangʼono chabe, ndikuyembekeza kuti mudzamvetsa kwenikweni, kuti mutha kutinyadira monga ife tidzakunyadirani, pa tsiku la Ambuye Yesu.
Comme vous l’avez reconnu en partie, que nous sommes votre gloire, de même que vous serez la nôtre au jour de Notre Seigneur Jésus-Christ.
15 Popeza ndinatsimikiza mtima za ichi, nʼchifukwa chake ndinafuna kuti poyamba, ndidzakuchezereni kuti mupindule pawiri.
C’est dans cette confiance que je voulais venir d’abord vous voir, pour que vous reçussiez une seconde grâce;
16 Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya.
Passer par chez vous en allant en Macédoine, et revenir de Macédoine près de vous, et par vous être conduit en Judée.
17 Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?”
Ayant donc eu ce dessein, ai-je été inconstant? ou bien, ce que je projette, le projetai-je selon la chair, de sorte qu’en moi il y ait OUI et NON?
18 Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.”
Mais Dieu est fidèle témoin que la parole que nous vous avons annoncée n’a point été dans ce OUI et NON.
19 Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.”
Car le fils de Dieu, Jésus-Christ, que nous vous avons prêché, moi, Silvain et Timothée, ne fut point oui et non; mais oui fut seul en lui.
20 Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu.
En effet, toutes les promesses quelconques de Dieu sont en lui le oui; c’est pourquoi nous disons aussi par lui Amen à Dieu pour notre gloire.
21 Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife,
Or celui qui nous affermit avec vous dans le Christ, et qui nous a oints, c’est Dieu,
22 nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.
Qui nous a aussi marqués de son sceau, et a donné le gage de l’Esprit dans nos cœurs.
23 Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni.
Pour moi, je prends Dieu à témoin sur mon âme, que c’est pour vous épargner, que je ne suis point encore venu à Corinthe;
24 Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.
ce n’est pas que nous dominions sur votre foi; au contraire, nous coopérons à votre joie, car vous êtes fermes dans la foi.